Anthu ndi osaona mtima
Mtima wa munthu ndi wosaona mtima
Yehova atamva fungo labwino anati mu mtima mwake: “Sindidzatembereranso nthaka chifukwa cha munthu, ngakhale kuti maganizo a mu mtima mwake ndi oyipa kuyambira ubwana wake. Ndipo sindidzawononganso zolengedwa zonse zamoyo monga ndachitiramu. (Genesis 8:21)
Mtima wa munthu ndi wonyenga kupambana zinthu zonse ndipo kuyipa kwake nʼkosachizika. Ndani angathe kuwumvetsa? (Yeremiya 17:9)
Pakuti mu mtima mumatuluka maganizo oyipa, zakupha, zachigololo, zadama, zakuba, zaumboni wonama ndi zachipongwe. (Mateyu 15:19)
Pakuti kuchokera mʼkati mwa mitima ya anthu, mumatuluka maganizo oyipa, chiwerewere, kuba, kupha, chigololo, dyera, nkhwidzi, chinyengo, machitidwe onyansa, kaduka, chipongwe, kudzikuza ndi kupusa. (Marko 7:21-22)
Anthu amaona mtima pangʼono chabe
Masiku amenewo kunalibe mfumu ku Israeli. Aliyense amachita zomwe zinamukomera. (Oweruza 17:6)
Zitsanzo za anthu osaona mtima
...chonsecho abambo anu akhala akundinyenga posintha malipiro anga kakhumi konse. Komabe Mulungu sanalole kuti andichitire choyipa (Genesis 31:7)
Aisraeli achimwa. Iwo aphwanya pangano limene ndinawalamula kuti asunge. Anatengako zinthu zina zofunika kuwonongedwa. Choncho anabako, ananena bodza ndi kuyika zinthu zakubazo pamodzi ndi katundu wawo. Akani anayankha kuti, “Zoona! Ine ndachimwira Yehova Mulungu wa Israeli. Chimene ndachita ine ndi ichi: Ndinaona mwa zinthu zolanda ku nkhondo zija, mkanjo wokongola wa ku Babuloni, makilogalamu awiri a siliva ndiponso golide wolemera theka la kilogalamu. Zimenezi ndinazikhumba ndipo ndinazitenga. Ndazibisa mʼkati mwa tenti yanga, ndipo siliva ali pansi pake.” (Yoswa 7:11, 20-21)
Koma ana akewo sanatengere makhalidwe ake abwino. Iwo ankapotokera ku zoyipa namatsata phindu mwachinyengo. Ankalandira ziphuphu ndi kumaweruza mwachinyengo. (1 Samueli 8:3)
Ukamuwuze kuti: ‘Yehova akuti, Kodi siwapha munthu ndi kumulandanso munda wake?’ Ndipo ukamuwuzenso kuti, ‘Yehova akuti, Pamalo pamene agalu ananyambita magazi a Naboti, pamalo pomwepo agalu adzanyambita magazi ako, inde, akonso!’ ” (1 Mafumu 21:19)
Ngakhale kuchokera tsiku lawo lobadwa oyipa amasochera; kuchokera mʼmimba ya amayi awo, iwo ndi otayika ndipo amayankhula mabodza. (Masalimo 58:3)
Atsogoleri ako ndi owukira, anthu ogwirizana ndi mbala; onse amakonda ziphuphu ndipo amathamangira mphatso. Iwo sateteza ana amasiye; ndipo samvera madandawulo a akazi amasiye. (Yesaya 1:23)
Ali ngati agalu amene ali ndi njala yayikulu; sakhuta konse. Abusa nawonso samvetsa zinthu; onse amachita monga akufunira, aliyense amafunafuna zomupindulitsa iye mwini. (Yesaya 56:11)
“Kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, onse ali ndi dyera lofuna kupeza phindu mwa kuba; aneneri pamodzi ndi ansembe omwe, onse amachita zachinyengo. (Yeremiya 6:13)
“Kodi inu muziba ndi kupha, kuchita chigololo ndi kulumbira monama, kufukiza lubani kwa Baala ndi kutsatira milungu ina imene simunayidziwe, Kodi Nyumba ino imene imadziwika ndi Dzina langa, yasanduka phanga la anthu olanda zinthu anzawo mwachifwamba inu mukuona? Komatu ndakhala ndi kuziona zonsezi! akutero Yehova.” (Yeremiya 7:9, 11)
Atsogoleri ake ali ngati mimbulu yokhadzula nyama; amakhetsa magazi ndi kupha anthu kuti apeze phindu loyipa. Anthu a mʼdzikomo amasautsa anzawo ndi kulanda anthu osowa. Amazunza anthu osauka ndi amphawi. Amavutitsa alendo posawachitira zinthu mwachilungamo. (Ezekieli 22:27, 29)
Inu Aisraeli, imvani mawu a Yehova, chifukwa Yehova ali ndi mlandu ndi inu amene mumakhala mʼdzikoli: “Mʼdziko mwanu mulibe kukhulupirika, mulibe chikondi mulibe kulabadira za Mulungu. Muli kutemberera kokha, kunama ndi kupha. Kuba ndi kuchita chigololo; machimo achita kunyanya ndipo akungokhalira kuphana. (Hoseya 4:1-2)
Atsogoleri a Yuda ali ngati anthu amene amasuntha miyala ya mʼmalire. Ndidzawakhutulira ukali wanga ngati madzi a chigumula. (Hoseya 5:10)
Pamene ndichiritsa Israeli, machimo a Efereimu amaonekera poyera ndiponso milandu ya Samariya sibisika. Iwo amachita zachinyengo, mbala zimathyola nyumba, achifwamba amalanda anthu katundu mʼmisewu. (Hoseya 7:1)
Munthu wamalonda amagwiritsa ntchito masikelo achinyengo; iyeyo amakonda kubera anthu. (Hoseya 12:7)
Inu anthu oyipa, kodi Ine nʼkuyiwala chuma chanu chimene munachipeza mwachinyengo, ndiponso muyeso wanu woperewera umene ndi wotembereredwa? Kodi ndimutenge ngati wosalakwa munthu amene ali ndi sikelo yachinyengo, ndiponso miyeso yabodza mʼthumba lake? Anthu ake olemera amachita zachiwawa; anthu ake ndi abodza ndipo pakamwa pawo pamayankhula zachinyengo. (Mika 6:10-12)
Koma mmodzi wa ophunzira ake, Yudasi Isikarioti, amene pambuyo pake adzamupereka anati, “Nʼchifukwa chiyani mafuta awa sanagulitsidwe ndipo ndalama zake nʼkuzipereka kwa osauka?” Mafutawo anali a mtengo wa malipiro a chaka chimodzi. Iye sananene izi chifukwa cha kuganizira osauka koma chifukwa anali mbava; ngati wosunga thumba la ndalama, amabamo zomwe ankayikamo. (Yohane 12:4-6)
Iwo anafuwula nati, “Ameneyu ayi! Mutipatse ife Baraba!” Barabayo anali wachifwamba. (Yohane 18:40)
Koma munthu wina dzina lake Hananiya, pamodzi ndi mkazi wake Safira, anagulitsanso munda wawo. Mogwirizana ndi mkazi wakeyo anapatulapo pa ndalamazo nazisunga, ndipo anatenga zotsalazo ndi kukapereka kwa atumwi. Koma Petro anamufunsa kuti, “Hananiya, chifukwa chiyani Satana anadzaza chotere mu mtima wako kuti unamize Mzimu Woyera ndipo wapatula ndi kusunga ndalama? Kodi sunali wako usanagulitse? Ndipo utagulitsa ndalamazo sizinali mʼmanja mwako kodi? Nʼchiyani chinakuchititsa zimenezi? Iwe sunanamize anthu koma Mulungu.” Hananiya atamva mawu amenewa anagwa pansi namwalira. Onse amene anamva zimene zinachitikazi anachita mantha kwambiri. Kenaka anyamata anafika, nakulunga thupi lake, ndipo anamunyamula ndi kukamuyika mʼmanda. Patapita maora atatu mkazi wake analowa, wosadziwa zimene zinachitika. Petro anamufunsa iye kuti, “Tandiwuza, kodi izi ndi ndalama zonse zimene iwe ndi Hananiya munalandira mutagulitsa munda?” Mkaziyo anati, “Inde ndi zimenezo.” Petro anati kwa iye, “Bwanji inu munapangana kuyesa Mzimu wa Ambuye? Taona! Anthu amene anakayika mwamuna wako mʼmanda ali pa khomo, ndipo adzakunyamula iwenso.” Nthawi yomweyo anagwa pansi pa mapazi a Petro ndipo anamwalira. Ndipo anyamata aja analowa, napeza kuti wafa kale, anamunyamula ndi kukamuyika pafupi ndi mwamuna wake. (Machitidwe a Atumwi 5:1-10)
Mneneri wina, mmodzi wa iwo omwewo anati, “Akrete nthawi zonse ndi amabodza, akhalidwe loyipitsitsa ndiponso alesi adyera.” (Tito 1:12)
Anthu ena onse amene sanaphedwe ndi miliri imeneyi sanalapebe kuti asiye ntchito zawo zoyipa. Iwo sanasiye kupembedza ziwanda ndi mafano agolide, asiliva, amkuwa, amwala ndi amtengo, mafano amene sangathe kuona, kumva kapena kuyankhula. Sanalapenso kuleka zakupha, zamatsenga awo, zachigololo zawo kapena umbava wawo. (Chivumbulutso 9:20-21)
Fanizo logwiritsa ntchito kusaona mtima ngati chitsanzo
Yesu anawuza ophunzira ake kuti, “Panali munthu wina wachuma amene kapitawo wake anzake anamuneneza kuti amawononga chuma chakecho. Choncho anamuyitana ndi kumufunsa kuti, ‘Kodi nʼchiyani chimene ndikumva za iwe? Pereka tsatanetsatane wa ntchito yako, pakuti supitirizanso kukhala kapitawo wanga.’ “Kapitawoyo analingalira kuti, ‘Kodi tsopano ndidzachita chiyani? Bwana wanga andichotsa ntchito. Ine ndilibe mphamvu zokwanira zolimira, komanso ine ndimachita manyazi kupempha. Ine ndikudziwa chimene ndidzachita kotero kuti, pamene ntchito yanga yatha pano, anthu adzandilandire mʼnyumba zawo.’ “Choncho iye anayitana aliyense amene anali ndi ngongole kwa bwana wake. Iye anafunsa woyamba, ‘Kodi uli ndi ngongole yotani kwa bwana wanga?’ “Iye anayankha kuti, ‘Migolo yamafuta a olivi 800.’ “Kapitawo uja anamuwuza iye, ‘Tenga pamene unalemba ngongole yakoyo, khala pansi msanga ndipo lemba kuti ndi migolo 400.’ “Kenaka iye anafunsa wachiwiri kuti, ‘Nanga iwe uli ndi ngongole yotani?’ “Iye ayankha kuti madengu a tirigu 1,000. “Iye anati, ‘Tenga pamene unalemba ngongole yakoyo ndipo ulembepo 800.’ “Bwana anayamikira kapitawo wosakhulupirikayo popeza anachita mochenjera. Pakuti anthu a dziko lino lapansi ndi ochenjera kwambiri akamachita zinthu ndi anthu ofanana nawo kuposa anthu a kuwunika. (Luka 16:1-8)
Kusaona mtima kobisika mʼchipembedzo
“Kodi inu muziba ndi kupha, kuchita chigololo ndi kulumbira monama, kufukiza lubani kwa Baala ndi kutsatira milungu ina imene simunayidziwe, ndipo kenaka nʼkubwera kudzayima pamaso panga mʼNyumba ino, Nyumba imene imadziwika ndi Dzina langa, inu nʼkumati, ‘Tapulumuka.’ Mwapulumuka kuti muzichitabe zonyansazi? Kodi Nyumba ino imene imadziwika ndi Dzina langa, yasanduka phanga la anthu olanda zinthu anzawo mwachifwamba inu mukuona? Komatu ndakhala ndi kuziona zonsezi! akutero Yehova.” (Yeremiya 7:9-11)
Yesu analowa mʼdera lina la Nyumba ya Mulungu ndipo anatulutsa kunja anthu onse amene ankachita malonda. Anagubuduza matebulo a osinthira ndalama ndi mipando ya ogulitsa nkhunda. Iye anawawuza kuti, “Zinalembedwa kuti Nyumba yanga idzatchedwa Nyumba ya mapemphero koma inu mwayisandutsa phanga la anthu achifwamba.” (Mateyu 21:12-13)
“Tsoka kwa inu, aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi achiphamaso! Mumayeretsa kunja kwa chikho ndi mbale, koma mʼkatimo mwadzaza ndi dyera ndi kusadziretsa. (Mateyu 23:25)
Atafika ku Yerusalemu, Yesu analowa mʼbwalo lakunja la Nyumba ya Mulungu ndipo anayamba kupirikitsa anthu amene amagula ndi kugulitsa mʼmenemo. Anagubuduza matebulo a osintha ndalama ndi mipando ya ogulitsa nkhunda, ndipo Iye sanalole aliyense kugulitsa malonda mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu. Ndipo pamene ankawaphunzitsa, Iye anati, “Kodi sikunalembedwe kuti, ‘Nyumba yanga idzatchedwa Nyumba ya mapemphero kwa anthu a mitundu yonse?’ Koma inu mwayisandutsa ‘phanga la achifwamba.’ ” (Marko 11:15-17)
Kenaka Ambuye anamuwuza kuti, “Inu Afarisi mumatsuka kunja kwa chikho ndi mbale, koma mʼkati mwanu ndi modzaza ndi kudzikonda ndi zoyipa. (Luka 11:39)
Kenaka Iye analowa mʼdera la Nyumba ya Mulungu ndi kuyamba kutulutsa kunja amene amachita malonda. Iye anawawuza kuti, “Zinalembedwa kuti Nyumba yanga idzakhala nyumba ya mapemphero, koma inu mwayisadutsa phanga la achifwamba.” (Luka 19:45-46)
Paja pali anthu ambiri osaweruzika, makamaka mʼgulu la anthu a mdulidwe, oyankhula nkhani zopanda pake ndi kusocheretsa anzawo. Ayenera kuletsedwa kuyankhula chifukwa akusokoneza mabanja athunthu pophunzitsa zinthu zomwe sayenera kuwaphunzitsa. Iwo amachita izi kuti apeze ndalama mwachinyengo. (Tito 1:10-11)
Mulungu amafuna kuona mtima kwathunthu
Ambuye ndi choonadi, Satana ndi wabodza
Ambuye ndi choonadi
Mawu anasandulika thupi ndipo anakhala pakati pathu. Ife tinaona ulemerero wake, ulemerero wa Iye amene ndi Mwana mmodzi yekhayo wa Atate, wodzaza ndi chisomo ndi choonadi. (Yohane 1:14)
Yesu anayankha kuti, “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate popanda kudzera mwa Ine. (Yohane 14:6)
Koma pamene Iye, Mzimu wachoonadi, abwera, adzakutsogolerani mʼchoonadi chonse. Iye sadzayankhula mwa Iye yekha, adzayankhula zokhazo zimene wamva ndipo Iye adzakuwuzani zimene zikubwera. (Yohane 16:13)
Pakuti pali atatu amene amachitira umboni. (1 Yohane 5:7)
Satana ndi wabodza
Inu ndinu ana a mdierekezi. Iye ndiye abambo anu ndipo mukufuna kuchita zimene abambo anuwo amakhumba. Iye anali wakupha kuyambira pachiyambi, sanasunge choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene Iye anena bodza, amayankhula chiyankhulo chobadwa nacho, popeza ndi wabodza ndipo ndi bambo wa mabodza. (Yohane 8:44)
Pansi pa lamulo la Chipangano Chakale
“Usabe. (Eksodo 20:15)
“ ‘Musabe. “ ‘Musamanamizane. “ ‘Musachitirane zinthu mwachinyengo. “ ‘Musalumbire mʼdzina langa monyenga popeza kutero ndi kuyipitsa dzina la Mulungu wanu. Ine ndine Yehova. “ ‘Musapsinje mnzanu kapena kumulanda zinthu zake. “ ‘Musasunge malipiro a munthu wantchito usiku wonse mpaka mmawa. (Levitiko 19:11-13)
“ ‘Musamachite za chinyengo poweruza mlandu, kapena poyeza utali, kulemera ngakhalenso kuchuluka kwa zinthu. Miyeso ya sikelo, miyeso yoyezera kulemera kwa zinthu, miyeso yotchedwa efa ndi miyeso yotchedwa hini zikhale zolungama. Ine ndine Yehova, Mulungu wanu amene ndinakutulutsani ku dziko la Igupto. (Levitiko 19:35-36)
“ ‘Ngati unagulitsa kapena kugula malo ako kwa mnzako wa mʼdzikomo, pasakhale kuchenjeretsana. Ugule kwa mnzako potsata chiwerengero cha zaka zimene zatha kuyambira pa chikondwerero cha chaka cha makumi asanu chapita. Ndipo mnzakoyo akugulitse potsata chiwerengero cha zaka zokolola zomwe zatsala. Zaka zikakhala zochuluka, uwonjezere mtengo, ndipo zaka zikakhala zochepa, uchepetse mtengo, pakuti chimene iye akukugulitsa ndi zaka zokolola. Musachenjeretsane koma muope Mulungu wanu. Ine ndine Yehova Mulungu wanu. (Levitiko 25:14-17)
“Usabe. (Deuteronomo 5:19)
Musamasunthe mwala wa malire anu ndi mnzanu amene anayikidwa ndi makolo anu pa cholowa chimene mulandire mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani. (Deuteronomo 19:14)
Musamakhale ndi miyeso iwiri yosiyana mʼthumba mwanu, wolemera ndi wopepuka. Musamakhale ndi milingo iwiri yosiyana mʼnyumba mwanu, waukulu ndi waungʼono. Muyenera kukhala ndi miyeso ndi milingo yoyenera ndi yosanyenga kuti mukhalitse mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani. Pakuti Yehova Mulungu wanu amanyansidwa ndi aliyense wochita za chinyengo zoterezi. (Deuteronomo 25:13-16)
Ngati mfundo yaikulu ya Baibulo
...asunge lilime lake ku zoyipa ndi milomo yake kuti isayankhule zonama. (Masalimo 34:13)
Zoonadi inu mumafuna choonadi mu ziwalo zamʼkati mwanga; mumandiphunzitsa nzeru mʼkati mwanga mwenimweni. (Masalimo 51:6)
Musadalire kulanda mwachinyengo kapena katundu wobedwa; ngakhale chuma chanu chichuluke, musayike mtima wanu pa icho. (Masalimo 62:10)
Makhalidwe ochitira ena chifundo ndi owonetsa kukhulupirika asakuchokere. Uwamangirire mʼkhosi mwako ngati mkanda ndi kuwalemba pa mtima pako. (Miyambo 3:3)
Usiyiretu kuyankhula zokhotakhota; ndipo ulekeretu kuyankhula zinthu zonyansa. (Miyambo 4:24)
Munthu wachabechabe, munthu woyipa, amangoyendayenda ndi kumayankhula zoyipa, (Miyambo 6:12)
Pali zinthu zisanu ndi chimodzi zimene Yehova amadana nazo, zinthu zisanu ndi ziwiri zimene zimamunyansa: mboni yonama yoyankhula mabodza komanso munthu amene amayambitsa mikangano pakati pa abale. (Miyambo 6:16, 19)
Muyeso wachinyengo Yehova umamunyansa, koma amakondwera ndi muyeso woyenera. (Miyambo 11:1)
Pakamwa pa bodza pamamunyansa Yehova, koma amakondwera ndi anthu oyankhula zoona. (Miyambo 12:22)
Munthu wolungama amadana ndi zabodza, koma zochita za munthu woyipa zimanyansa ndiponso zimachititsa manyazi. (Miyambo 13:5)
Mboni yokhulupirika sinama, koma mboni yonyenga imayankhula zabodza. (Miyambo 14:5)
Mboni yokhulupirika imapulumutsa miyoyo, koma mboni yabodza imaphetsa. (Miyambo 14:25)
Kuyankhula bwino sikuyenerana ndi chitsiru, nanji kuyankhula bodza kungayenerane kodi ndi mfumu? (Miyambo 17:7)
Miyeso ndi masikelo achilungamo zimachokera kwa Yehova; miyala yonse yoyesera ya mʼthumba anayipanga ndi Yehova. (Miyambo 16:11)
Masikelo ndi miyeso ya zinthu imene ili yachinyengo zonsezi Yehova zimamunyansa. (Miyambo 20:10)
Miyeso yosintha imamunyansa Yehova; ndipo masikelo onyenga si abwino. (Miyambo 20:23)
Mʼmphawi usamubere chifukwa ndi osauka, ndipo usawapondereze anthu osowa mʼbwalo la milandu, pakuti Yehova adzawateteza pa mlandu wawo ndipo adzalanda moyo onse amene amawalanda iwo. (Miyambo 22:22-23)
Usasunthe mwala wamʼmalire akalekale amene anayikidwa ndi makolo ako. (Miyambo 22:28)
Usasunthe mwala wa mʼmalire akalekale kapena kulowerera mʼminda ya ana amasiye, (Miyambo 23:10)
Gula choonadi ndipo usachigulitse; ugulenso nzeru, mwambo ndiponso kumvetsa zinthu bwino. (Miyambo 23:23)
Amene amabera abambo ake kapena amayi ake namanena kuti “kumeneko sikulakwa,” ndi mnzake wa munthu amene amasakaza. (Miyambo 28:24)
...kukaniza munthu ufulu wake pamaso pa Wammwambamwamba, kumana munthu chiweruzo cholungama— kodi Ambuye saona zonsezi? (Maliro 3:35-36)
Zinthu zoti muchite ndi izi: Muziwuzana zoona zokhazokha, muziweruza moona ndi mwachilungamo mʼmabwalo anu; musamachitire mnzanu chiwembu, musamakonde kulumbira zonama. Zonsezi Ine ndimadana nazo,” akutero Yehova. (Zekariya 8:16-17)
Amisonkho nawonso anabwera kudzabatizidwa. Iwo anafunsa kuti, “Aphunzitsi, ife tichite chiyani?” Iye anawawuza kuti, “Musalandire moposa zimene muyenera.” Kenaka asilikali ena anamufunsa kuti, “Nanga ife tichite chiyani?” Iye anayankha kuti, “Musamalande ndalama moopseza ndipo musamanamizire anthu, khutitsidwani ndi malipiro anu.” (Luka 3:12-14)
...tsono, iwe amene umaphunzitsa ena, sudziphunzitsa wekha kodi? Kodi iwe amene umalalikira kuti anthu asabe, umabanso? Kodi iwe amene umanena kuti anthu asachite chigololo, umachitanso chigololo? Kodi iwe amene umanyasidwa ndi mafano, umalandanso za mʼnyumba zopembedzera mafanowo? (Aroma 2:21-22)
Chokha choti mwakasumirana chikuonetseratu kuti mwagonjetsedwa kale. Bwanji osangolola kuti ena akulakwireni? Bwanji osangolola kuti ena akubereni? Mʼmalo mwake, inuyo ndiye mumabera ena ndi kuwalakwira, ndipo mumachita izi kwa abale anu. Kodi simukudziwa kuti munthu woyipa sadzalowa mu ufumu wa Mulungu? Musanyengedwe: achigololo, kapena opembedza mafano, kapena achiwerewere, kapena amuna adama, kapena ogonana ndi amuna okhaokha; kapena akuba, kapena aumbombo, kapena oledzera, kapena achipongwe, kapena opeza ndalama mwachinyengo sadzalowa mu ufumu wa Mulungu. (1 Akorinto 6:7-10)
Chifukwa chake, aliyense wa inu aleke kunama ndipo ayankhule zoona kwa mʼbale wake, pakuti ife tonse ndife ziwalo za thupi limodzi. (Aefeso 4:25)
Tsono imani mwamphamvu, mutamangira choonadi ngati lamba mʼchiwuno mwanu, mutavala chilungamo ngati chitsulo chotchinjiriza pa chifuwa. (Aefeso 6:14)
Musanamizane wina ndi mnzake, popeza munavula munthu wakale pamodzi ndi zochita zake (Akolose 3:9)
Mupewe choyipa cha mtundu wina uliwonse. (1 Atesalonika 5:22)
Tikudziwanso kuti Malamulo sakhazikitsidwa chifukwa cha anthu olungama, koma ophwanya lamulo ndi owukira, osaopa Mulungu ndi ochimwa, wopanda chiyero ndi osapembedza; amene amapha abambo awo ndi amayi awo, kapena anthu ena. Malamulo amayikidwa chifukwa cha anthu achigololo ndi ochita zadama ndi amuna anzawo, anthu ogulitsa akapolo, abodza ndi olumbira zabodza, ndi ochita chilichonse chotsutsana ndi chiphunzitso choona. (1 Timoteyo 1:9-10)
Phunzitsa akapolo kuti azigonjera ambuye awo mu zinthu zonse ndi kuwakondweretsa. Asamatsutsane nawo kapena kumawabera, koma adzionetse kuti ndi odalirika, motero pa zochita zawo zonse adzaonetsa ubwino wa chiphunzitso cha Mulungu, Mpulumutsi wathu. (Tito 2:9-10)
Koma monga amene anakuyitanani ndi woyera, inunso khalani oyera mtima mʼmakhalidwe anu wonse. Pakuti, kwalembedwa kuti, “Khalani oyera mtima, chifukwa Ine ndine Woyera.” (1 Petro 1:15-16)
Ngati mumva zowawa, zisakhale chifukwa cha kupha munthu, kapena kuba, kapena kuchita choyipa, kapena kulowerera za anthu ena, (1 Petro 4:15)
Kumafunika kwa atsogoleri
Boma
Koma sankhani amuna odziwa ntchito yawo, anthu owopa Mulungu, anthu odalirika amene amadana ndi kupeza phindu mwachinyengo. Tsono muwayike kuti akhale oyangʼanira anthu motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 100, ena a anthu 50 ndi ena a anthu khumi. Tsono amenewa aziweruza anthu nthawi zonse. Mlandu uliwonse waukulu azibwera nawo kwa inu, koma mlandu waungʼono aziweruza okha. Izi zidzachititsa kuti ntchito yanu ipepuke, popeza mudzagwira ntchito mothandizana. (Eksodo 18:21-22)
Kukoma mtima ndi kukhulupirika ndizo zimasunga mfumu; chilungamo chimalimbikitsa mpando wake waufumu. (Miyambo 20:28)
Wolamulira amene samvetsa zinthu ndiye amakhala wankhanza koma amene amadana ndi phindu lopeza mwachinyengo adzakhala ndi moyo wautali. (Miyambo 28:16)
“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Tsono pakwana, inu akalonga a Israeli. Lekani nkhanza zanu ndi kupondereza anthu anga. Muzitsata chilungamo ndi kuchita zokomera anthu. Musapirikitse anthu anga mʼdzikomo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. Miyeso yanu yoyezera zinthu monga efa ndi bati zizikhala zokhulupirika. (Ezekieli 45:9-10)
Mpingo
Momwemonso atumiki, akhale anthu oyenera ulemu, woona mtima, osakhala okonda zoledzeretsa, osakonda kupeza zinthu mwachinyengo. (1 Timoteyo 3:8)
Popeza mkulu wa mpingo amayendetsa ntchito za banja la Mulungu, ayenera kukhala wopanda cholakwa, asakhale womva zayekha, kapena wopsa mtima msanga, kapena womwa zoledzeretsa, kapena wandewu, kapena wopeza phindu mwachinyengo. (Tito 1:7)
Ine ndikupempha akulu a mpingo amene ali pakati panu, monga inenso mkulu mnzawo, mboni ya zowawa za Khristu ndiponso amene ndidzalandira nawo ulemerero umene uti udzaonetsedwe. Wetani gulu la Mulungu limene lili mʼmanja mwanu, muziliyangʼanira. Muzichita osati mowumirizidwa, koma mwakufuna kwanu, monga momwe Mulungu akufunira kuti mutero. Musachite chifukwa chadyera la ndalama, koma ndi mtima ofuna kutumikira. (1 Petro 5:1-2)
Kuona mtima kumafunika pa kupereka
Ndipo inu mumati, ‘Ndi zotopetsa zimenezi!’ Ndipo mumandinyogodola Ine,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Pamene inu mubweretsa nyama zakuba, zolumala kapena zodwala ndi kupereka nsembe, kodi Ine ndizilandire kuchokera mʼmanja mwanu?” Akutero Yehova. “Atembereredwe munthu wachinyengo amene ali ndi nyama yayimuna yabwino mʼgulu la ziweto zake ndipo analumbira kuyipereka, koma mʼmalo mwake nʼkupereka nsembe kwa Ambuye nyama yosayenera. Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Pakuti ndine mfumu yayikulu, dzina langa liyenera kuopedwa pakati pa anthu a mitundu yonse.’ ” (Malaki 1:13-14)
Kusapereka moyenera kumaonedwa ngati kuba
“Kodi munthu angathe kuba za Mulungu? Komatu inu mumandibera. “Koma inu mukufunsa kuti, ‘Kodi timakuberani motani?’ “Pa zakhumi ndi pa zopereka. Mtundu wanu wonse ndinu otembereredwa, chifukwa mukundibera. (Malaki 3:8-9)
Kuona mtima kuli ndi mtengo kuposa chuma
Ndi wabwino munthu wosauka amene amayenda mu ungwiro, aposa munthu wopusa woyankhula zokhota. (Miyambo 19:1)
Chimene munthu amafuna ndi chikondi chosatha; nʼkwabwino kukhala wosauka kusiyana ndi kukhala wabodza. (Miyambo 19:22)
Pamene olungama apambana pamakhala chikondwerero chachikulu; koma pamene anthu oyipa apatsidwa ulamuliro, anthu amabisala. (Miyambo 28:12)
Zitsanzo za anthu oona mtima
Pamenepo Mose anakwiya kwambiri ndipo anati kwa Yehova, “Musalandire chopereka chawo. Sindinatenge kalikonse kwa iwo ngakhale bulu, ndiponso sindinalakwire wina aliyense wa iwo.” (Numeri 16:15)
Ine ndili pano. Ngati ndinalakwa chilichonse nditsutseni pamaso pa Yehova ndi wodzozedwa wake. Kodi ndinalanda ngʼombe ya yani? Kodi ndinalanda bulu wa yani? Kodi ndani amene ndinamudyera masuku pa mutu? Kodi ndinazunza yani? Kodi ndinalandira kwa yani chiphuphu choti nʼkundidetsa mʼmaso? Ngati ndinachita chilichonse cha izi, ine ndidzakubwezerani.” Iwo anayankha kuti, “Inu simunatidyere masuku pamutu kapena kutizunza. Simunalande kanthu kalikonse ka munthu.” Samueli anawawuza kuti, “Yehova ndiye mboni pakati pa inu ndi ine, ndiponso wodzozedwa wake ndi mboni kuti lero simunapeze chilichonse mʼdzanja langa.” Iwo anati, “Inde, Yehova ndiye mboni.” (1 Samueli 12:3-5)
“Ngati ndachita zinthu mwachiphamaso, kapena kufulumira kukachita zachinyengo, Pamenepo ena adye zimene ndinadzala, ndipo zomera zanga zizulidwe. (Yobu 31:5, 8)
Chifukwa cha ichi, anzake ndi akalonga anayesa kupeza zifukwa zomutsutsira Danieli pa kayendetsedwe ka ntchito za dzikolo, koma sanapeze cholakwa chilichonse. Iwo sanapeze chinyengo mwa iye, chifukwa anali wokhulupirika ndipo sankachita chinyengo kapena kutayirira ntchito. (Danieli 6:4)
Mulungu wanga anatumiza mngelo wake, ndipo anatseka pakamwa pa mikango. Iyo sinandivulaze chifukwa Mulungu anaona kuti ndine wosalakwa ndi kutinso sindinakulakwireni inu mfumu.” (Danieli 6:22)
Aisraeli otsala sadzachitanso zolakwika; sadzayankhulanso zonama, ngakhale chinyengo sichidzatuluka mʼkamwa mwawo. Adzadya ndi kugona ndipo palibe amene adzawachititse mantha.” (Zefaniya 3:13)
Chitsanzo cha kuyesa kuona mtima kwa anthu
Tonse ndife ana a munthu mmodzi. Ndife antchito anu okhulupirika osati akazitape.” Pa tsiku lachitatu Yosefe anawawuza kuti, “Popeza ine ndimaopa Mulungu, ndipo inuyo ngati mukufuna kukhala ndi moyo muchite izi: Ngati muli anthu achilungamo, mmodzi wa inu atsale mʼndende, pamene ena nonse mupite kwanu kuti muwatengere chakudya anthu akwanu kuli njalako. Mukabwere naye kuno mngʼono wanu wotsirizayo kuti titsimikizire zimene munanena kuti musafe.” Ndipo anachita zomwezo. (Genesis 42:11, 18-20)
Koma tinamuwuza kuti, ‘Ndife anthu woona mtima osati akazitape. Ife tonse tinalipo ana aamuna khumi ndi awiri, abambo mmodzi. Mmodzi anamwalira, ndipo wamngʼono ali ndi abambo athu ku Kanaani.’ ” Ndipo nduna ija inati kwa ife, “Kuti ndidziwedi kuti ndinu anthu owona mtima muchite izi: Mmodzi mwa inu atsale ndi ine kuno, ndipo enanu mutenge chakudya ndi kubwerera kwanu kumene kuli njalako. Koma mundibweretsere wotsirizayo kuti ndidziwedi kuti sindinu akazitape koma anthu achilungamo. Kenaka ndidzakubwezerani mʼbale wanuyu ndipo mukhoza kuchita malonda mʼdzikoli.” (Genesis 42:31-34)
Anthu opembedza amadana ndi kusaona mtima
Munthu wolungama amadana ndi zabodza, koma zochita za munthu woyipa zimanyansa ndiponso zimachititsa manyazi. (Miyambo 13:5)
Nʼchifukwa chiyani Mulungu amafuna kuona mtima kwathunthu?
Sitingakhale osaona mtima ndi kukonda Mulungu
Amene amayenda molungama amaopa Yehova, koma amene njira zake ndi zoyipa amanyoza Yehova. (Miyambo 14:2)
Sitingakhale osaona mtima ndi kukonda mnansi wathu
Munthu wonama amadana ndi amene anawapweteka, ndipo pakamwa poshashalika pamabweretsa chiwonongeko. (Miyambo 26:28)
Malamulo awa: “Usachite chigololo,” “Usaphe,” “Usabe,” “Usasirire,” ndi malamulo ena onse amene alipo, akhazikika pa lamulo limodzi ili, “Konda mnansi wako monga iwe mwini.” Chikondi sichichitira mnzake zoyipa. Chifukwa chake chikondi ndicho chokwaniritsa lamulo. (Aroma 13:9-10)
Kuona mtima kumapangitsa uthenga wabwino kukhulupirika
...kuti mukhale wopanda cholakwa ndi angwiro, ana a Mulungu wopanda cholakwika mu mʼbado uno wachinyengo ndi wosocheretsa. Mukatero mudzawala pakati pawo ngati nyenyezi zakumwamba (Afilipi 2:15)
Kuona mtima kumathandiza kutsogolera moyo wathu
Usiyiretu kuyankhula zokhotakhota; ndipo ulekeretu kuyankhula zinthu zonyansa. Maso ako ayangʼane patsogolo; uziyangʼana kutsogolo molunjika. Uzilingalira bwino kumene kupita mapazi ako ndipo njira zako zonse zidzakhala zosakayikitsa. (Miyambo 4:24-26)
Ngakhale kusaona mtima kochepa kwambiri kumawononga
“Amene akhulupirika pa zinthu zochepa akhoza kukhulupirikanso pa zinthu zambiri, ndipo amene sakhulupirika pa zinthu zochepa adzakhala wosakhulupirika pa zinthu zambiri. (Luka 16:10)
Kodi tingapewe bwanji mayesero a kusaona mtima?
Mwa chisomo ndi mphamvu ya Ambuye
Tembenuzani mtima wanga kuti uzikonda malamulo anu, osati chuma. (Masalimo 119:36)
“Inu Yehova, ndikukupemphani zinthu ziwiri musandimane zimenezo ndisanafe: Choyamba, mundichotsere kutali nane mabodza ndi chinyengo. Chachiwiri, ndisakhale mʼmphawi kapena munthu wachuma. Koma muzindidyetsa chakudya chondikwanira tsiku ndi tsiku (Miyambo 30:7-8)
Choncho ine ndikuti, mulole kuti Mzimu akutsogolereni ndipo simudzachita zofuna za thupi lanu la uchimo. Pakuti thupi lanu la uchimo limalakalaka zimene ndi zotsutsana ndi Mzimu, ndi Mzimu zimene ndi zotsutsana ndi thupi lanu la uchimo. Ziwirizi zimadana, kotero kuti simungachite zimene mukufuna. (Agalatiya 5:16-17)
Potsatira lamulo lagolide
Nʼchifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu akuchitireni, yambani ndinu kuwachitira, pakuti izi ndi zimene malamulo ndi aneneri amaphunzitsa. (Mateyu 7:12)
Musamangofuna zokomera inu nokha koma aliyense azifuna zokomeranso ena. (Afilipi 2:4)
Poopa Ambuye moyenera
Chifukwa cha chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika, munthu amakhululukidwa machimo ake; chifukwa cha kuopa Yehova munthu amapewa zoyipa. (Miyambo 16:6)
Kudzipatula kwa anthu osaona mtima
Ine sindikhala pansi pamodzi ndi anthu achinyengo, kapena kufunsa nzeru kwa achiphamaso. (Masalimo 26:4)
Ndi wodala munthu amakhulupirira Yehova; amene sayembekezera kwa odzikuza, kapena kwa amene amatembenukira kwa milungu yabodza. (Masalimo 40:4)
Maso anga adzakhala pa okhulupirika mʼdziko, kuti akhale pamodzi ndi ine; iye amene mayendedwe ake ndi wosalakwa adzanditumikira. Aliyense wochita chinyengo sadzakhala mʼnyumba mwanga. Aliyense woyankhula mwachinyengo sadzayima pamaso panga. (Masalimo 101:6-7)
Mwana wanga, ngati anthu oyipa afuna kukukopa usamawamvere. Akadzati, “Tiye kuno; tikabisale kuti tiphe anthu, tikabisalire anthu osalakwa; tiwameze amoyo ngati manda, ndi athunthu ngati anthu otsikira mʼdzenje. Motero tidzapeza zinthu zosiyanasiyana zamtengowapatali ndi kudzaza nyumba zathu ndi zolanda; Bwera, chita nafe maere, ndipo tidzagawana chuma chathu tonse.” Mwana wanga, usayende nawo pamodzi, usatsagane nawo mʼnjira zawozo. Iwowatu amangofuna zoyipa zokhazokha, amathamangira kukhetsa magazi. (Miyambo 1:10-16)
Woyenda ndi munthu wakuba ndi mdani wa moyo wake womwe; amalumbira koma osawulula kanthu. (Miyambo 29:24)
Ndakulemberani mʼkalata yanga kuti musayanjane nawo anthu achigololo. Pamenepatu sindikutanthauzatu anthu a dziko lapansi lino amene ndi achigololo, kapena aumbombo, kapena opeza ndalama mwachinyengo, kapena opembedza mafano. Kukanatero mukanangochoka mʼdziko lapansi lino. Koma tsopano ndikukulemberani kuti musayanjane ndi aliyense amene adzitcha mʼbale koma ndi wachigololo, kapena waumbombo, kapena wopembedza mafano, kapena wonamizira anzake, woledzera kapena wopeza ndalama mwachinyengo. Munthu wotere ngakhale kudya, osadya naye pamodzi. (1 Akorinto 5:9-11)
Musasocheretsedwe, “Kukhala mʼmagulu oyipa kumawononga makhalidwe abwino.” (1 Akorinto 15:33)
Popereka
Iye amene wakhala akuba asabenso, koma agwire ntchito ndi kuchita kenakake kaphindu ndi manja ake, kuti akhale ndi kenakake kogawana ndi amene akusowa. (Aefeso 4:28)
Pokhazikitsa njira yoyankhira mlandu
Labani anafunsa, “Ndikupatse chiyani?” Yakobo anayankha, “Musandipatse kanthu. Koma mungondichitira izi ndipo ndidzapitiriza kusamalira nkhosa zanu ndi kuziyangʼanira: Mundilole ndiyendeyende pakati pa ziweto zanu lero ndi kuchotsamo mwana wankhosa wamkazi aliyense wakuda, mbuzi iliyonse yamathothomathotho ndi yamawangamawanga. Zimenezi ndiye zikhale malipiro anga. Ndipo chilungamo changa chidzaoneka mʼtsogolo, pamene inu mudzabwere kudzaona malipiro angawo. Ngati mudzapeza mbuzi mʼgulu langa imene si yamawangamawanga, kapena mwana wankhosa wamkazi amene si wakuda ndiye kuti zimenezo zidzakhala kuti ndinakuberani.” (Genesis 30:31-33)
Kodi tichite chiyani tikachita zosaona mtima?
Kubwezeretsa ubale wathu ndi Ambuye
“ ‘Pamene munthu wazindikira kuti wachimwa motere, awulule tchimo limene wachitalo. Pambuyo pake, munthuyo abwere kwa Yehova ndi mwana wankhosa wamkazi kapena mbuzi kuti ikhale chopereka chopepesera tchimo ndipo wansembe achite mwambo wopepesera tchimo lomwe wachitalo. Tsono wansembe achite mwambo wopepesera tchimo la munthuyo. (Levitiko 5:5-6)
Yehova anawuza Mose kuti, “Ngati munthu wina aliyense achimwa, nachita zinthu mosakhulupirika kwa Yehova chifukwa cha kunyenga mnzake pokana kumubwezera zimene anamusungitsa, kapena kumubera kapenanso kumulanda, kapena ndi kunama kuti sanatole chinthu chimene chinatayika, kapena kulumbira mwachinyengo pa chinthu chilichonse chimene munthu akachita amachimwa nacho, ndi wopalamula ndithu, ndipo ayenera kubweza zimene anabazo, zimene analanda mwachinyengozo, zimene anamusungitsazo, zimene anatolazo kapena zimene analumbira monyengazo. Pa tsiku limene apezeke kuti wapalamuladi, iye ayenera kumubwezera mwini wake zinthu zonsezi ndi kuwonjezerapo chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse. Kenaka wansembe achite mwambo wopepesera tchimo la munthuyo pamaso pa Yehova, ndipo adzakhululukidwa chilichonse chomwe anachita kuti akhale wopalamula.” (Levitiko 6:1-5, 7)
Koma tikavomereza machimo athu, Iye ndi wokhulupirika ndi wolungama ndipo adzatikhululukira machimo athu, nadzatiyeretsa ndi kutichotsera chosalungama chilichonse. (1 Yohane 1:9)
Kubwezeretsa ubale wathu ndi munthu amene tinamulakwira
Wobisa machimo ake sadzaona mwayi, koma aliyense amene awulula ndi kuleka machimowo, adzalandira chifundo. (Miyambo 28:13)
Choncho, ululiranani machimo anu ndi kupemphererana wina ndi mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama ndi lamphamvu ndipo limagwira ntchito. (Yakobo 5:16)
Kubweza chilichonse chakuba
“Ngati munthu aba ngʼombe kapena nkhosa ndi kuyipha kapena kuyigulitsa, iye abweze ngʼombe zisanu pa ngʼombe imodzi ndi nkhosa zinayi pa nkhosa imodzi. “Ngati mbala ipezeka ikuthyola nyumba ndipo imenyedwa nʼkufa, amene wapha mbalayo sanalakwe. Koma akayipha dzuwa litatuluka, woyiphayo ali ndi mlandu wakupha. “Mbala iyenera kubweza ndithu koma ngati ilibe kalikonse igulitsidwe, kulipira zomwe yabazo. “Ngati chiweto chobedwacho chipezeka chamoyo mʼmanja mwake, kaya ndi ngʼombe kapena bulu kapena nkhosa, mbalayo ibwezere ziweto ziwiri pa chiweto chobedwacho. (Eksodo 22:1-4)
“Ngati munthu asungitsidwa ndi mnzake ndalama kapena katundu, ndipo zinthu zija nʼkubedwa mʼnyumba mwake, wakubayo ngati agwidwa, ayenera kubwezera kawiri chobedwacho. Koma ngati mbalayo sipezeka, mwini nyumbayo ayenera kukaonekera ku bwalo lamilandu kuti akamve ngati anaba katundu wa mnzakeyo. Ngati pali kukangana kokhudza ngʼombe, bulu, nkhosa, zovala kapena kanthu kalikonse kotayika, ndipo mmodzi ndikunena kuti chinthucho nʼchake, awiriwo abwere nawo mlandu wawowo pamaso pa Mulungu ndipo amene mlandu umugomere adzayenera kumulipira mnzakeyo kawiri. (Eksodo 22:7-9)
“Ngati munthu abwereka chiweto cha mnzake ndipo chiweto chija nʼkuvulala kapena kufa chikanali ndi iyebe, wobwerekayo ayenera kulipira. (Eksodo 22:14)
Yehova anawuza Mose kuti, “Ngati munthu wina aliyense achimwa, nachita zinthu mosakhulupirika kwa Yehova chifukwa cha kunyenga mnzake pokana kumubwezera zimene anamusungitsa, kapena kumubera kapenanso kumulanda, kapena ndi kunama kuti sanatole chinthu chimene chinatayika, kapena kulumbira mwachinyengo pa chinthu chilichonse chimene munthu akachita amachimwa nacho, ndi wopalamula ndithu, ndipo ayenera kubweza zimene anabazo, zimene analanda mwachinyengozo, zimene anamusungitsazo, zimene anatolazo kapena zimene analumbira monyengazo. Pa tsiku limene apezeke kuti wapalamuladi, iye ayenera kumubwezera mwini wake zinthu zonsezi ndi kuwonjezerapo chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse. (Levitiko 6:1-5)
Yehova anati kwa Mose, “Uza Aisraeli kuti, ‘Pamene mwamuna kapena mayi walakwira mnzake mwa njira iliyonse, ndiye kuti ndi wosakhulupirika pamaso pa Yehova. Munthuyo ndi wochimwa ndithu ndipo ayenera kuwulula tchimo limene anachitalo. Ayenera kubweza zonse zimene anawononga, ndipo awonjezerepo chimodzi mwa magawo asanu ndi kuzipereka kwa munthu amene anamulakwirayo. Ngati wolakwiridwayo alibe mʼbale komwe kungapite zinthu zobwezedwazo, zinthuzo zikhale za Yehova ndipo azipereke kwa wansembe, pamodzi ndi nkhosa yayimuna ya nsembe yopepesera tchimo lake. (Numeri 5:5-8)
Davide anapsa mtima kwambiri chifukwa cha munthuyo ndipo anati kwa Natani, “Pali Yehova, munthu amene anachita zimenezi ayenera kufa basi! Iye ayenera kulipira mwana wankhosa wamkaziyo kanayi, chifukwa anachita chinthu chimenechi ndipo analibe chifundo.” (2 Samueli 12:5-6)
Paja anthu sayinyoza mbala ikaba chifukwa chakuti ili ndi njala. Komabe ngati mbalayo igwidwa iyenera kulipira kasanu nʼkawiri, ngakhale kulandidwa katundu wa mʼnyumba mwake. (Miyambo 6:30-31)
Ndipo ngati ndiwuza munthu woyipa kuti, ‘Udzafa ndithu,’ tsono iye nʼkutembenuka kuleka machimo ake ndi kuyamba kuchita zimene Yehova afuna, monga kubweza chimene anatenga ngati chikole cha ngongole, kubweza chimene anaba, kutsatira malamulo omwe amapereka moyo ndi kuleka kuchita zoyipa, iye adzakhala ndithu ndi moyo; sadzafa. Ndidzakhululuka machimo ake onse anachita. Iye wachita zimene ndi zolungama ndi zoyenera ndipo iye adzakhala ndi moyo ndithu. (Ezekieli 33:14-16)
Koma Zakeyu anayimirira ndipo anati kwa Ambuye, “Taonani Ambuye! Theka la chuma changa ndipereka kwa osauka ndipo ngati ndinamubera wina aliyense pa chilichonse, ndidzamubwezera mochulukitsa kanayi.” (Luka 19:8)
Madalitso ndi matemberero
Madalitso olonjezedwa kwa oona mtima
Dalitso la ubale wapafupi ndi Ambuye
Salimo la Davide. Yehova, ndani angathe kukhala mʼmalo anu opatulika? Kodi ndani angathe kukhala mʼphiri lanu loyera? Munthu wa makhalidwe abwino, amene amachita zolungama, woyankhula choonadi chochokera mu mtima mwake, ndipo mʼkamwa mwake simutuluka mawu osinjirira, amene sachitira choyipa mnansi wake kapena kufalitsa mbiri yoyipa ya munthu mnzake, amene sapereka ulemu kwa munthu woyipa. Koma amalemekeza amene amaopa Yehova, amene amakwaniritsa zomwe walonjeza ngakhale pamene zikumupweteka, (Masalimo 15:1-4)
Ndani angakwere phiri la Yehova? Ndani angathe kuyima pa malo ake opatulika? Iye amene ali ndi mʼmanja moyera ndi mtima woyera, amene sapereka moyo wake kwa fano kapena kulumbira mwachinyengo. (Masalimo 24:3-4)
Yehova ali pafupi ndi onse amene amamuyitana, onse amene amamuyitana Iye mʼchoonadi. (Masalimo 145:18)
Makhalidwe ochitira ena chifundo ndi owonetsa kukhulupirika asakuchokere. Uwamangirire mʼkhosi mwako ngati mkanda ndi kuwalemba pa mtima pako. Ukatero udzapeza kuyanja ndi mbiri yabwino pamaso pa Mulungu ndi anthu. (Miyambo 3:3-4)
Pakuti Yehova amanyansidwa ndi munthu woyipa koma amayanjana nawo anthu olungama. (Miyambo 3:32)
Pakamwa pa bodza pamamunyansa Yehova, koma amakondwera ndi anthu oyankhula zoona. (Miyambo 12:22)
“Kodi kukhala ndi nyumba ya mkungudza wambiri zingachititse iwe kukhala mfumu? Ganiza za abambo ako. Suja anali ndi zonse zakudya ndi zakumwa. Abambo ako ankaweruza molungama ndi mosakondera, ndipo zonse zinkawayendera bwino. Iye ankateteza anthu osauka ndi osowa, ndipo zonse zinkamuyendera bwino. Kodi zimenezi sindiye tanthauzo la kudziwa Ine?” akutero Yehova. “Koma maso ako ndi mtima sizili penanso, koma zili pa phindu lachinyengo, pa zopha anthu osalakwa ndi pa kuzunza ndi pakulamulira mwankhanza.” (Yeremiya 22:15-17)
Dalitso la chitetezo
Anthu olungama zinthu zimawayendera bwino chifukwa Yehova amakhala nawo. Paja Yehova ndiye chishango cha amene amayenda mwangwiro, (Miyambo 2:7)
Munthu woyenda mwangwiro amayenda mosatekeseka; koma amene amayenda njira yokhotakhota adzadziwika. (Miyambo 10:9)
Dalitso la kupatsidwa zosowa
Angathe kuti ndi amene amachita zolungama ndi kuyankhula zoona, amene amakana phindu lolipeza monyenga ndipo salola manja ake kulandira ziphuphu, amene amatseka makutu ake kuti angamve mawu opangana kupha anzawo ndipo amatsinzina kuti angaone zoyipa. Munthu wotere ndiye adzakhale pa nsanja, kothawira kwake kudzakhala mʼmalinga a mʼmapiri. Azidzalandira chakudya chake ndipo madzi sadzamusowa. (Yesaya 33:15-16)
Dalitso pa banja
Munthu wolungama amakhala ndi makhalidwe abwino; odala ndi ana ake amene amatsanzira moyo wake. (Miyambo 20:7)
Dalitso la chimwemwe
Chuma chochipeza mwachinyengo sichipindulitsa, koma chilungamo chimapulumutsa ku imfa. (Miyambo 10:2)
Dalitso la moyo
Musamakhale ndi miyeso iwiri yosiyana mʼthumba mwanu, wolemera ndi wopepuka. Musamakhale ndi milingo iwiri yosiyana mʼnyumba mwanu, waukulu ndi waungʼono. Muyenera kukhala ndi miyeso ndi milingo yoyenera ndi yosanyenga kuti mukhalitse mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani. (Deuteronomo 25:13-15)
Aliyense wa inu amene amakonda moyo wake ndi kukhumba kuti aone masiku abwino ambiri, asunge lilime lake ku zoyipa ndi milomo yake kuti isayankhule zonama. (Masalimo 34:12-13)
Mawu woona amakhala mpaka muyaya koma mawu abodza sakhalitsa. (Miyambo 12:19)
Ndipo ngati ndiwuza munthu woyipa kuti, ‘Udzafa ndithu,’ tsono iye nʼkutembenuka kuleka machimo ake ndi kuyamba kuchita zimene Yehova afuna, monga kubweza chimene anatenga ngati chikole cha ngongole, kubweza chimene anaba, kutsatira malamulo omwe amapereka moyo ndi kuleka kuchita zoyipa, iye adzakhala ndithu ndi moyo; sadzafa. Ndidzakhululuka machimo ake onse anachita. Iye wachita zimene ndi zolungama ndi zoyenera ndipo iye adzakhala ndi moyo ndithu. (Ezekieli 33:14-16)
Dalitso la ulemu wa anthu
Makhalidwe ochitira ena chifundo ndi owonetsa kukhulupirika asakuchokere. Uwamangirire mʼkhosi mwako ngati mkanda ndi kuwalemba pa mtima pako. Ukatero udzapeza kuyanja ndi mbiri yabwino pamaso pa Mulungu ndi anthu. (Miyambo 3:3-4)
Dalitso la kulemera
Munthu wolungama amakhala ndi chuma chambiri, zimene woyipa amapindula nazo zimamugwetsa mʼmavuto. (Miyambo 15:6)
Dalitso kwa atsogoleri
Wolamulira amene samvetsa zinthu ndiye amakhala wankhanza koma amene amadana ndi phindu lopeza mwachinyengo adzakhala ndi moyo wautali. (Miyambo 28:16)
Matemberero osungidwa kwa osaona mtima
Temberero la kudedwa/kupatulidwa kwa Mulungu
Musamakhale ndi miyeso iwiri yosiyana mʼthumba mwanu, wolemera ndi wopepuka. Musamakhale ndi milingo iwiri yosiyana mʼnyumba mwanu, waukulu ndi waungʼono. Muyenera kukhala ndi miyeso ndi milingo yoyenera ndi yosanyenga kuti mukhalitse mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani. Pakuti Yehova Mulungu wanu amanyansidwa ndi aliyense wochita za chinyengo zoterezi. (Deuteronomo 25:13-16)
Mumawononga iwo amene amanena mabodza; anthu akupha ndi achinyengo, Yehova amanyansidwa nawo. (Masalimo 5:6)
Pakuti Yehova amanyansidwa ndi munthu woyipa koma amayanjana nawo anthu olungama. (Miyambo 3:32)
Pali zinthu zisanu ndi chimodzi zimene Yehova amadana nazo, zinthu zisanu ndi ziwiri zimene zimamunyansa: mboni yonama yoyankhula mabodza komanso munthu amene amayambitsa mikangano pakati pa abale. (Miyambo 6:16, 19)
Pakamwa pa bodza pamamunyansa Yehova, koma amakondwera ndi anthu oyankhula zoona. (Miyambo 12:22)
Mboni yonama sidzalephera kulangidwa, ndipo iye amene amanena mabodza adzawonongeka. (Miyambo 19:9)
Ine ndinakwiya kwambiri chifukwa cha tchimo lawo ladyera; ndinawalanga ndi kuwafulatira mokwiya, koma iwo anapitirirabe kuchita ntchito zawo zoyipa. (Yesaya 57:17)
Koma zoyipa zanu zakulekanitsani ndi Mulungu wanu; ndipo wakufulatirani chifukwa cha machimo anu, kotero Iye sadzamva. Pakuti manja anu ali psuu ndi magazi. Munayipitsa zala zanu ndi zamphulupulu. Pakamwa panu payankhula zabodza, ndipo lilime lanu lanena zinthu zoyipa. Palibe amene akuyimba mnzake mlandu molungama, palibe amene akupita ku mlandu moona mtima. Iwo amadalira mawu opanda pake ndipo amayankhula mabodza; amalingalira za mphulupulu ndipo amachita zoyipa. (Yesaya 59:2-4)
Temberero la chilango/chiweruzo
“Ndi wotembereredwa munthu amene amasuntha mwala wa malire wa mnzake.” (Deuteronomo 27:17)
Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu; onse amene amalumbira mʼdzina la Mulungu adzalemekeza Mulunguyo, koma pakamwa pa anthu onama padzatsekedwa. (Masalimo 63:11)
Pakamwa pa bodza pamamunyansa Yehova, koma amakondwera ndi anthu oyankhula zoona. (Miyambo 12:22)
Maganizo a anthu oyipa amamunyansa Yehova, koma mawu a anthu oyera mtima amamusangalatsa. (Miyambo 15:26)
Mboni yonama sidzalephera kulangidwa; ndipo iye amene amanena mabodza sadzapulumuka. (Miyambo 19:5)
Chakudya chochipeza mwachinyengo chimukomera munthu, koma pa mapeto pake chimasanduka ngati mchenga mʼkamwa mwake. (Miyambo 20:17)
Ine ndinakwiya kwambiri chifukwa cha tchimo lawo ladyera; ndinawalanga ndi kuwafulatira mokwiya, koma iwo anapitirirabe kuchita ntchito zawo zoyipa. (Yesaya 57:17)
Nyumba zawo zadzaza ndi chuma chochipeza mwa chinyengo ngati zikwere zodzaza ndi mbalame. Nʼchifukwa chake asanduka otchuka ndi olemera. Ndipo ananenepa ndi kukhala ndi matupi osalala. Ntchito zawo zoyipa nʼzopanda malire; saweruza mwachilungamo nkhani ya ana amasiye kuti iyende bwino, sateteza ufulu wa anthu osauka. Kodi Ine ndingaleke kuwalanga chifukwa cha zimenezi? Kodi ndisawulipsire mtundu woterewu? Akutero Yehova. (Yeremiya 5:27-29)
“Amapinda lilime lawo ngati uta. Mʼdzikomo mwadzaza ndi mabodza okhaokha osati zoonadi. Amapitirirabe kuchita zoyipa; ndipo sandidziwa Ine.” Akutero Yehova. “Aliyense achenjere ndi abwenzi ake; asadalire ngakhale abale ake. Aliyense amafuna kumudyera mʼbale wake masuku pa mutu. Choncho aliyense amachitira bwenzi lake ugogodi. Aliyense amamunamiza mʼbale wake ndipo palibe amene amayankhula choonadi. Anapazoloweza pakamwa pawo kunena zabodza; amalimbika kuchita machimo. Iwe wakhalira mʼchinyengo ndipo ukukana kundidziwa Ine,” akutero Yehova. Nʼchifukwa chake Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Taonani, Ine ndidzawasungunula ngati chitsulo ndi kuwayesa. Kodi ndingachite nawonso bwanji chifukwa cha machimo awo? Lilime lawo lili ngati muvi wakuthwa; limayankhula zachinyengo. Aliyense ndi pakamwa pake amayankhula mawu achikondi kwa mnansi wake, koma mu mtima mwake amakonzekera zomuchita chiwembu. Kodi ndilekerenji kuwalanga chifukwa cha zimenezi? akutero Yehova. ‘Kodi ndisawulipsire mtundu wotere wa anthu?’ ” (Yeremiya 9:3-9)
“ ‘Koma Ine ndachita kuwomba mʼmanja kuti phuu nʼkudabwa chifukwa cha phindu lachinyengo limene mwapeza ndiponso chifukwa cha kuphana kumene kumachitika pakati panu. Kodi mtima wako udzakhala wolimbabe kapena manja ako adzakhalabe amphamvu ndikadzatsiriza kukulanga iwe? Ine Yehova ndayankhula, ndipo ndidzazichitadi. Ndidzakubalalitsani pakati pa anthu a mitundu ina ndi kukumwazirani ku mayiko onse. Umu ndi mmene ndidzachotsere zoyipa zako. (Ezekieli 22:13-15)
Atsogoleri ake ali ngati mimbulu yokhadzula nyama; amakhetsa magazi ndi kupha anthu kuti apeze phindu loyipa. Aneneri ake amabisa zonsezi monga muja amachitira anthu popaka njereza. Amazimphimba ndi zabodza zimene aona mʼmasomphenya awo ndi zonama za mʼmawula awo. Iwo amati, ‘Ambuye Yehova akuti,’ pamene Ine Yehova sindinayankhule. Anthu a mʼdzikomo amasautsa anzawo ndi kulanda anthu osowa. Amazunza anthu osauka ndi amphawi. Amavutitsa alendo posawachitira zinthu mwachilungamo. “Ndinafunafuna munthu pakati pawo woti amange linga, woti ayimirire dziko pamaso panga kundipepesa kuti ndisaliwononge, koma sindinamupeze. Nʼchifukwa chake ndawakwiyira kwambiri. Ndawawonongeratu ndi mkwiyo wanga woyaka ngati moto. Ndawalanga molingana ndi zimene anachita. Akutero Ambuye Yehova.” (Ezekieli 22:27-31)
Atsogoleri a Yuda ali ngati anthu amene amasuntha miyala ya mʼmalire. Ndidzawakhutulira ukali wanga ngati madzi a chigumula. (Hoseya 5:10)
Imvani izi, inu amene mumapondereza anthu osowa ndipo simulabadira anthu osauka a mʼdzikomu. Mumanena kuti, “Kodi chikondwerero cha mwezi watsopano chidzatha liti kuti tigulitse zinthu? Ndipo tsiku la Sabata litha liti kuti tigulitse tirigu, kuti tichepetse miyeso, kukweza mitengo kuti tibere anthu ndi miyeso ya chinyengo, tigule osauka ndi ndalama zasiliva ndi osowa powapatsa nsapato, tigulitse ngakhale mungu wa tirigu?” Yehova amene Yakobo amamunyadira, walumbira kuti: Ine sindidzayiwala chilichonse chimene anachita. “Kodi dziko silidzagwedezeka chifukwa cha zimenezi, ndi onse okhala mʼmenemo kulira mwachisoni? Dziko lonse lidzavunduka ngati mtsinje wa Nailo; lidzagwedezeka kenaka nʼkukhala bata ngati mtsinje wa ku Igupto. “Tsiku limenelo,” Ambuye Yehova akunena kuti, “Ndidzadetsa dzuwa masana ndi kugwetsa mdima pa dziko lapansi dzuwa likuswa mtengo. Maphwando anu achipembedzo ndidzawasandutsa kulira kwa chisoni ndipo kuyimba kwanu konse ndidzakusandutsa maliro. Ndidzakuvekani chiguduli nonsenu ndi kumeta mipala mitu yanu. Nthawi imeneyo idzakhala ngati yolira mwana wamwamuna mmodzi yekhayo, ndipo tsikulo lidzakhala lowawa mpaka kutha kwake. (Amosi 8:4-10)
Inu anthu oyipa, kodi Ine nʼkuyiwala chuma chanu chimene munachipeza mwachinyengo, ndiponso muyeso wanu woperewera umene ndi wotembereredwa? Kodi ndimutenge ngati wosalakwa munthu amene ali ndi sikelo yachinyengo, ndiponso miyeso yabodza mʼthumba lake? Anthu ake olemera amachita zachiwawa; anthu ake ndi abodza ndipo pakamwa pawo pamayankhula zachinyengo. Choncho, ndayamba kukuwonongani, kukusakazani chifukwa cha machimo anu. Mudzadya, koma simudzakhuta; mudzakhalabe ndi njala. Mudzasunga zinthu, koma sizidzasungika, chifukwa zimene mudzasunga zidzawonongedwa ndi lupanga. Mudzadzala, koma simudzakolola. Mudzayenga mafuta a olivi, koma simudzawagwiritsa ntchito. Mudzaponda mphesa, koma simudzamwa vinyo wake. Inu mwatsatira malangizo a Omuri ndiponso machitidwe onse a banja la Ahabu, ndi khalidwe lawo lonse. Choncho Ine ndidzakuperekani kuti muwonongedwe ndiponso anthu anu kuti azunguzike mitu; mudzanyozedwa ndi anthu a mitundu ina.” (Mika 6:10-16)
Yesu analowa mʼdera lina la Nyumba ya Mulungu ndipo anatulutsa kunja anthu onse amene ankachita malonda. Anagubuduza matebulo a osinthira ndalama ndi mipando ya ogulitsa nkhunda. Iye anawawuza kuti, “Zinalembedwa kuti Nyumba yanga idzatchedwa Nyumba ya mapemphero koma inu mwayisandutsa phanga la anthu achifwamba.” (Mateyu 21:12-13)
Kenaka Iye analowa mʼdera la Nyumba ya Mulungu ndi kuyamba kutulutsa kunja amene amachita malonda. Iye anawawuza kuti, “Zinalembedwa kuti Nyumba yanga idzakhala nyumba ya mapemphero, koma inu mwayisadutsa phanga la achifwamba.” (Luka 19:45-46)
Temberero la imfa/chiwonongeko
Aisraeli achimwa. Iwo aphwanya pangano limene ndinawalamula kuti asunge. Anatengako zinthu zina zofunika kuwonongedwa. Choncho anabako, ananena bodza ndi kuyika zinthu zakubazo pamodzi ndi katundu wawo. Iye amene adzagwidwe ndi zinthu zoyenera kuwonongedwazo adzawotchedwa ndi moto, pamodzi ndi banja lake lonse ndi zinthu zake zonse. Iyeyutu wachita chinthu chonyansa pakati pa Aisraeli ndi kuphwanya pangano limene anthu anga anachita ndi Ine!” Yoswa anati “Chifukwa chiyani wabweretsa mavuto awa pa ife? Yehova ndiye abweretse mavuto pa iwe lero.” Kenaka Aisraeli onse anaponya miyala Akani, namupha. Anaponyanso miyala banja lake lonse, nʼkulipha. Pambuyo pake anatentha Akani uja, banja lake ndi zonse zimene anali nazo. (Yoswa 7:11, 15, 25)
Mumawononga iwo amene amanena mabodza; anthu akupha ndi achinyengo, Yehova amanyansidwa nawo. (Masalimo 5:6)
Iwe umakonda choyipa mʼmalo mwa kuyankhula choonadi. Umakonda kunama kupambana kuyankhula zoona. Sela Umakonda mawu onse opweteka, iwe lilime lachinyengo! Zoonadi Mulungu adzakutsitsa kupita ku chiwonongeko chamuyaya: iye adzakukwatula ndi kukuchotsa mʼtenti yako; iye adzakuzula kuchoka mʼdziko la amoyo. (Masalimo 52:3-5)
Awa ndiwo mathero a anthu opeza chuma mwankhanza; chumacho chimapha mwiniwake. (Miyambo 1:19)
Munthu wachabechabe, munthu woyipa, amangoyendayenda ndi kumayankhula zoyipa, Nʼchifukwa chake tsoka lidzamugwera modzidzimutsa; adzawonongeka msangamsanga popanda chomupulumutsa. (Miyambo 6:12, 15)
Mawu woona amakhala mpaka muyaya koma mawu abodza sakhalitsa. (Miyambo 12:19)
Chuma chochipeza ndi mawu onyenga ndi chosakhalitsa ndipo chimakola anthu mu msampha wa imfa. (Miyambo 21:6)
Amene amafesa zoyipa amakolola mavuto, ndipo ndodo yaukali wake idzathyoka. (Miyambo 22:8)
Mʼmphawi usamubere chifukwa ndi osauka, ndipo usawapondereze anthu osowa mʼbwalo la milandu, pakuti Yehova adzawateteza pa mlandu wawo ndipo adzalanda moyo onse amene amawalanda iwo. (Miyambo 22:22-23)
“Koma maso ako ndi mtima sizili penanso, koma zili pa phindu lachinyengo, pa zopha anthu osalakwa ndi pa kuzunza ndi pakulamulira mwankhanza.” Nʼchifukwa chake Yehova ponena za Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda akuti, “Anthu sadzamulira maliro kapena kunena kuti, ‘Kalanga ine, mʼbale wanga! Kalanga ine mlongo wanga! Anthu ake sadzamulira maliro kuti, Kalanga ine, mbuye wathu! Taonani ulemerero wake wapita!’ Adzayikidwa ngati bulu, kuchita kumuguguza ndi kukamutaya kunja kwa zipata za Yerusalemu.” (Yeremiya 22:17-19)
“Tiyerekeze kuti munthu wolungama chotere wabala mwana chimbalangondo amene amakhalira kupha anthu ndi kuchita zinthu zina zotere. Iye nʼkumachita zinthu zimene ngakhale abambo ake sanachitepo. “Amadyera nawo ku mapiri achipembedzo. Amayipitsa mkazi wa mnzake. Iye amapondereza munthu wosauka ndi wosowa. Amalanda zinthu za osauka. Sabweza chikole cha munthu wa ngongole. Iye amatembenukira ku mafano nachita zonyansa. Iye amakongoletsa mwa katapira ndipo amalandira chiwongoladzanja chachikulu. Kodi munthu wotereyu nʼkukhala ndi moyo? Ayi ndithu! Chifukwa wachita zinthu zonyansa zonsezi, adzaphedwa ndipo adzalandira chilango chomuyenera. Koma abambo ake, popeza kuti anazunza anthu ena ndi kubera mʼbale wawo ndiponso popeza kuti sanachitire zabwino anansi ake, adzafera machimo ake omwe. (Ezekieli 18:10-13, 18)
Koma munthu wina dzina lake Hananiya, pamodzi ndi mkazi wake Safira, anagulitsanso munda wawo. Mogwirizana ndi mkazi wakeyo anapatulapo pa ndalamazo nazisunga, ndipo anatenga zotsalazo ndi kukapereka kwa atumwi. Koma Petro anamufunsa kuti, “Hananiya, chifukwa chiyani Satana anadzaza chotere mu mtima wako kuti unamize Mzimu Woyera ndipo wapatula ndi kusunga ndalama? Kodi sunali wako usanagulitse? Ndipo utagulitsa ndalamazo sizinali mʼmanja mwako kodi? Nʼchiyani chinakuchititsa zimenezi? Iwe sunanamize anthu koma Mulungu.” Hananiya atamva mawu amenewa anagwa pansi namwalira. Onse amene anamva zimene zinachitikazi anachita mantha kwambiri. Kenaka anyamata anafika, nakulunga thupi lake, ndipo anamunyamula ndi kukamuyika mʼmanda. Patapita maora atatu mkazi wake analowa, wosadziwa zimene zinachitika. Petro anamufunsa iye kuti, “Tandiwuza, kodi izi ndi ndalama zonse zimene iwe ndi Hananiya munalandira mutagulitsa munda?” Mkaziyo anati, “Inde ndi zimenezo.” Petro anati kwa iye, “Bwanji inu munapangana kuyesa Mzimu wa Ambuye? Taona! Anthu amene anakayika mwamuna wako mʼmanda ali pa khomo, ndipo adzakunyamula iwenso.” Nthawi yomweyo anagwa pansi pa mapazi a Petro ndipo anamwalira. Ndipo anyamata aja analowa, napeza kuti wafa kale, anamunyamula ndi kukamuyika pafupi ndi mwamuna wake. (Machitidwe a Atumwi 5:1-10)
Temberero pa banja
Munthu wofuna phindu mwachinyengo amavutitsa banja lake, koma wodana ndi ziphuphu adzakhala ndi moyo. (Miyambo 15:27)
Nʼchifukwa chake akazi awo ndidzawapereka kwa amuna ena ndipo minda yawo ndidzayipereka kwa amene adzawagonjetse. Kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, onse ali ndi khalidwe lofuna kupeza chuma mwakuba. Aneneri pamodzi ndi ansembe omwe, onse amachita zachinyengo. (Yeremiya 8:10)
Tsoka kwa amene amakonzekera chiwembu, kwa amene amakonzekera kuchita zoyipa usiku pa mabedi awo! Kukacha mmawa amakachitadi chifukwa ali ndi mphamvu zochitira zimenezo. Amasirira minda ndi kuyilanda, amasirira nyumba ndi kuzilanda. Amatenga nyumba ya munthu mwachinyengo, munthu mnzawo kumulanda cholowa chake. Nʼchifukwa chake Yehova akuti, “Ine ndikukonzekera kubweretsa tsoka pa anthu awa, tsoka limene simudzatha kudzipulumutsa nokha. Inu simudzayendanso monyada, pakuti idzakhala nthawi ya masautso. (Mika 2:1-3)
Temberero pa chuma
...chonsecho abambo anu akhala akundinyenga posintha malipiro anga kakhumi konse. Komabe Mulungu sanalole kuti andichitire choyipa Motero Mulungu walanda abambo anu ziweto zawo ndi kundipatsa. (Genesis 31:7, 9)
Chuma chochipeza mwachinyengo sichipindulitsa, koma chilungamo chimapulumutsa ku imfa. (Miyambo 10:2)
Chuma chochipeza mofulumira chidzatha pangʼonopangʼono koma chuma chosonkhanitsidwa pangʼonopangʼono chidzachulukirachulukira. (Miyambo 13:11)
Nyumba zawo adzazipereka kwa ena, pamodzi ndi minda yawo ndi akazi awo. Ndidzatambasula dzanja langa kukantha anthu okhala mʼdzikomo,” akutero Yehova. “Kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, onse ali ndi dyera lofuna kupeza phindu mwa kuba; aneneri pamodzi ndi ansembe omwe, onse amachita zachinyengo. (Yeremiya 6:12-13)
Munthu amene amapeza chuma mwachinyengo ali ngati nkhwali imene imafungatira mazira amene sinayikire. Pamene ali pakatikati pa moyo wake, chumacho chidzamuthera, ndipo potsiriza adzasanduka chitsiru. (Yeremiya 17:11)
“Imirira, puntha, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni, pakuti ndidzakupatsa nyanga zachitsulo; ndidzakupatsa ziboda zamkuwa ndipo udzaphwanya mitundu yambiri ya anthu.” Phindu lawo lolipeza molakwikalo udzalipereka kwa Yehova, chuma chawo kwa Yehova wa dziko lonse lapansi. (Mika 4:13)
Temberero la kunyada
Amene amafesa zoyipa amakolola mavuto, ndipo ndodo yaukali wake idzathyoka. (Miyambo 22:8)
Temberero pa omwe ali pansi pa mtsogoleri
Ngati wolamulira amvera zabodza, akuluakulu ake onse adzakhala oyipa. (Miyambo 29:12)
Temberero lamuyaya
Koma amantha, osakhulupirira, okonda zonyansa, opha anthu, achiwerewere, amatsenga, opembedza mafano ndi abodza, malo awo adzakhala nyanja yamoto ya sulufule wotentha. Iyi ndi imfa yachiwiri.” (Chivumbulutso 21:8)
Kanthu kosayeretsedwa sikadzalowamo, kuphatikizanso aliyense wochita zinthu zochititsa manyazi ndi zachinyengo, koma okhawo amene mayina awo alembedwa mʼbuku lamoyo la Mwana Wankhosa. (Chivumbulutso 21:27)
Kunja kuli agalu, amatsenga, achiwerewere, akupha anthu, opembedza mafano ndi aliyense amene amakonda bodza ndi kulichita. (Chivumbulutso 22:15)
Matemberero onse
“Ndi wotembereredwa munthu amene amasuntha mwala wa malire wa mnzake.” (Deuteronomo 27:17)
Chakudya chochipeza mwachinyengo chimukomera munthu, koma pa mapeto pake chimasanduka ngati mchenga mʼkamwa mwake. (Miyambo 20:17)
Tsoka kwa mzinda wopha anthu, mzinda wodzaza ndi mabodza, mzinda wodzaza ndi anthu olanda zinthu anzawo, mu mzinda mʼmene simusowa anthu osautsidwa nthawi zonse! (Nahumu 3:1)
Maganizo a anthu kuti Mulungu salanga kusaona mtima
“Chifukwa chiyani Wamphamvuzonse sayikiratu nthawi yoti aweruze? Chifukwa chiyani iwo amene amadziwa Iyeyo amayembekezera pachabe masiku oterewa? Anthu amasuntha miyala ya mʼmalire, kuti akuze dziko lawo; amadyetsa ziweto zimene aba. Kubuwula kwa anthu amene akufa kumamveka kuchokera mu mzinda, anthu ovulala akulirira chithandizo. Koma Mulungu sakuyimba mlandu wina aliyense. (Yobu 24:1-2, 12)
Ziphuphu
Anthu amapereka ziphuphu
Ziphuphu zimagwira ntchito
Chiphuphu chili ngati mankhwala amwayi kwa wochiperekayo; kulikonse kumene amapita zinthu zimamuyendera. (Miyambo 17:8)
Mphatso yoperekedwa mseri imathetsa mkwiyo, ndipo chiphuphu choperekedwa mobisa chimathetsa mphamvu ya ukali woopsa. (Miyambo 21:14)
Oyipa amapereka ziphuphu
Musachotse moyo wanga pamodzi ndi ochimwa, moyo wanga pamodzi ndi anthu akupha anzawo, amene mʼmanja mwawo muli ndondomeko zoyipa, dzanja lawo lamanja ladzaza ndi ziphuphu. (Masalimo 26:9-10)
Munthu woyipa amalandira chiphuphu chamseri kuti apotoze chiweruzo cholungama. (Miyambo 17:23)
Zitsanzo za amene anapereka ziphuphu
Koma ana akewo sanatengere makhalidwe ake abwino. Iwo ankapotokera ku zoyipa namatsata phindu mwachinyengo. Ankalandira ziphuphu ndi kumaweruza mwachinyengo. (1 Samueli 8:3)
Atsogoleri ako ndi owukira, anthu ogwirizana ndi mbala; onse amakonda ziphuphu ndipo amathamangira mphatso. Iwo sateteza ana amasiye; ndipo samvera madandawulo a akazi amasiye. (Yesaya 1:23)
Manja awo onse ndi aluso pochita zoyipa; wolamulira amafuna mphatso, woweruza amalandira ziphuphu, anthu amphamvu amalamula kuti zichitike zimene akuzifuna, onse amagwirizana zochita. (Mika 7:3)
Amayi aja akupita, ena mwa alonda aja anapita ku mzinda nafotokozera akulu a ansembe zonse zimene zinachitika. Akulu a ansembe atakumana ndi akuluakulu anapangana zochita. Anapatsa alonda aja ndalama zambiri, nawawuza kuti, “Muzinena kuti, ‘Ophunzira ake anabwera usiku ndipo amuba ife tili mtulo.’ Ngati nkhani iyi imupeze bwanamkubwa, ife tidzamukhazika mtima pansi ndipo simudzakhala mʼmavuto.” Pamenepo alondawo anatenga ndalamazo nachita monga mmene anawuzidwira. Ndipo mbiri iyi inawanda pakati pa Ayuda mpaka lero lino. (Mateyu 28:11-15)
Paulo atayankhula za chilungamo, za kudziretsa ndiponso za chiweruzo chimene chikubwera, Felike anachita mantha ndipo anati, “Basi tsopano! Pita. Tidzakuyitanitsa tikadzapeza mpata.” Pa nthawi imeneyi amayembekeza kuti Paulo adzamupatsa ndalama, nʼchifukwa chake amamuyitanitsa kawirikawiri ndi kumayankhula naye. (Machitidwe a Atumwi 24:25-26)
Lamulo losatenga nawo mbali mu ziphuphu
“Musamalandire chiphuphu, pakuti chiphuphu chimadetsa mʼmaso anthu oweruza ndi kusintha mawu awo kuti mlandu uyipire osalakwa. (Eksodo 23:8)
Musamakhotetse chiweruzo kapena kukondera. Musamalandire chiphuphu pakuti chiphuphu chimadetsa mʼmaso anthu a nzeru ndi kusintha mawu awo kuti mlandu uyipire osalakwa. (Deuteronomo 16:19)
Ziphuphu zimaipitsa
Kuzunza ena kumasandutsa munthu wanzeru kukhala chitsiru, ndipo chiphuphu chimawononga mtima. (Mlaliki 7:7)
Chitsanzo cha Ambuye kusalandira ziphuphu
Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wa milungu, Ambuye wa ambuye, Mulungu wamkulu, wamphamvu ndi woopsa, amene sakondera ndipo salandira ziphuphu. (Deuteronomo 10:17)
Atsogoleri sayenera kulandira ziphuphu
Tsopano kuopsa kwa Yehova kukhale pa inu. Muweruze mosamala, pakuti ndi Yehova Mulungu wathu palibe kupotoza chilungamo kapena kukondera kapenanso kulandira ziphuphu.” (2 Mbiri 19:7)
Mfumu imalimbitsa dziko poweruza mwachilungamo, koma mfumu imene imawumiriza anthu kuti ayipatse mphatso imawononga dziko. (Miyambo 29:4)
Zitsanzo za amene sanalandire ziphuphu
Ine ndili pano. Ngati ndinalakwa chilichonse nditsutseni pamaso pa Yehova ndi wodzozedwa wake. Kodi ndinalanda ngʼombe ya yani? Kodi ndinalanda bulu wa yani? Kodi ndani amene ndinamudyera masuku pa mutu? Kodi ndinazunza yani? Kodi ndinalandira kwa yani chiphuphu choti nʼkundidetsa mʼmaso? Ngati ndinachita chilichonse cha izi, ine ndidzakubwezerani.” Iwo anayankha kuti, “Inu simunatidyere masuku pamutu kapena kutizunza. Simunalande kanthu kalikonse ka munthu.” Samueli anawawuza kuti, “Yehova ndiye mboni pakati pa inu ndi ine, ndiponso wodzozedwa wake ndi mboni kuti lero simunapeze chilichonse mʼdzanja langa.” Iwo anati, “Inde, Yehova ndiye mboni.” (1 Samueli 12:3-5)
Kodi ine ndinanenapo kuti, ‘Ndiperekereni kenakake, ndilipirireni dipo kuchokera pa chuma chanu, (Yobu 6:22)
Madalitso ndi matemberero
Amene amapereka ziphuphu ndi otembereredwa
“Ndi wotembereredwa munthu amene alandira chiphuphu kuti aphe munthu wosalakwa.” (Deuteronomo 27:25)
...amene amamasula olakwa chifukwa cha chiphuphu koma amayipitsa mlandu wa munthu wosalakwa. (Yesaya 5:23)
Mwa iwe muli anthu amene amalandira ziphuphu kuti aphe anzawo; ena amachita katapira ndi kupeza phindu loposera muyeso; enanso amapeza phindu mwachinyengo poopseza anzawo. Ndipo mwandiyiwala Ine, akutero Ambuye Yehova. “ ‘Koma Ine ndachita kuwomba mʼmanja kuti phuu nʼkudabwa chifukwa cha phindu lachinyengo limene mwapeza ndiponso chifukwa cha kuphana kumene kumachitika pakati panu. Kodi mtima wako udzakhala wolimbabe kapena manja ako adzakhalabe amphamvu ndikadzatsiriza kukulanga iwe? Ine Yehova ndayankhula, ndipo ndidzazichitadi. Ndidzakubalalitsani pakati pa anthu a mitundu ina ndi kukumwazirani ku mayiko onse. Umu ndi mmene ndidzachotsere zoyipa zako. (Ezekieli 22:12-15)
Mumapondereza munthu wosauka ndi kumukakamiza kuti akupatseni tirigu. Nʼchifukwa chake, ngakhale mwamanga nyumba zamiyala yosema, inuyo simudzakhalamo. Ngakhale mwalima minda yabwino ya mphesa, inu simudzamwa vinyo wake. Pakuti Ine ndikudziwa kuchuluka kwa zolakwa zanu ndi kukula kwa machimo anu. Inu mumapondereza anthu olungama ndi kulandira ziphuphu ndipo anthu osauka simuwaweruza mwachilungamo mʼmabwalo anu amilandu. (Amosi 5:11-12)
Atsogoleri ake amalandira chiphuphu kuti aweruze, ansembe ake amalandira malipiro kuti alalikire, ndipo aneneri ake amanenera kuti alandire ndalama. Komatu amatsamira pa Yehova nʼkumanena kuti, “Kodi Yehova sali pakati pathu? Palibe tsoka limene lidzatigwere.” Choncho chifukwa cha inu, Ziyoni adzatipulidwa ngati munda, Yerusalemu adzasanduka bwinja, ndipo phiri la Nyumba ya Mulungu lidzasanduka nkhalango yowirira. (Mika 3:11-12)
Amene sapereka ziphuphu ndi odalitsika
Salimo la Davide. Yehova, ndani angathe kukhala mʼmalo anu opatulika? Kodi ndani angathe kukhala mʼphiri lanu loyera? amene amakongoletsa ndalama zake popanda chiwongoladzanja ndipo salandira chiphuphu pofuna kutsutsa anthu osalakwa. Iye amene amachita zinthu zimenezi sadzagwedezeka konse. (Masalimo 15:1, 5)
Munthu wofuna phindu mwachinyengo amavutitsa banja lake, koma wodana ndi ziphuphu adzakhala ndi moyo. (Miyambo 15:27)
Angathe kuti ndi amene amachita zolungama ndi kuyankhula zoona, amene amakana phindu lolipeza monyenga ndipo salola manja ake kulandira ziphuphu, amene amatseka makutu ake kuti angamve mawu opangana kupha anzawo ndipo amatsinzina kuti angaone zoyipa. Munthu wotere ndiye adzakhale pa nsanja, kothawira kwake kudzakhala mʼmalinga a mʼmapiri. Azidzalandira chakudya chake ndipo madzi sadzamusowa. (Yesaya 33:15-16)