Mayesero a kupereka
Kuyesa chikhulupiriro
Abale anga, phindu lake nʼchiyani ngati munthu anena kuti ali ndi chikhulupiriro koma chopanda ntchito zabwino? Kodi chikhulupiriro choterechi chingamupulumutse? Tangoganizirani, mʼbale kapena mlongo amene ali ndi usiwa, ndipo alibe chakudya cha tsiku ndi tsiku. Ngati mmodzi wa inu amuwuza kuti, “Pita ndi mtendere, ukafundidwe ndipo ukakhute,” koma osamupatsa zimene akuzisowa, phindu lake nʼchiyani pamenepa? Chomwechonso, chikhulupiriro chokha chopanda ntchito zabwino ndi chakufa. (Yakobo 2:14-17)
Kuyesa ngati chikondi cha Mulungu chikukhala mwa ife
Ngati wina ali ndi chuma ndipo nʼkuona mʼbale wake akusowa, koma wosamvera chisoni, kodi mwa iyeyo muli chikondi cha Mulungu? (1 Yohane 3:17)
Kuyesa chikondi kwa mnansi
Sindikukulamulirani, koma ndikufuna kuona ngati chikondi chanu nʼchoona pofananitsa ndi changu cha anthu ena. (2 Akorinto 8:8)
Chitsanzo cha Msamariya wachifundo
Koma Msamariya wina, ali pa ulendo wake, anafika pamene panali munthuyo; ndipo atamuona, anamva naye chisoni. Anapita panali munthu wovulalayo, nathira mafuta ndi vinyo pa zilonda zake, nʼkuzimanga. Kenaka anamukweza pa bulu wake, napita naye ku nyumba ya alendo, namusamalira. Mmawa mwake anatenga ndalama ziwiri zasiliva nazipereka kwa woyangʼanira nyumbayo, nati, ‘Musamalireni munthuyu, ndipo pobwera ndidzakubwezerani zonse zimene mugwiritse ntchito.’ (Luka 10:33-35)
Kuyesa ngati Khristu ndiye Ambuye
Yesu anayankha kuti, “Ngati ukufuna kukhala wangwiro, pita kagulitse katundu wako ndi kupereka kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Ukakachita zimenezi, ukabwere udzanditsate Ine.” Mnyamatayo atamva zimenezi, anachoka mokhumudwa, chifukwa anali ndi chuma chambiri. (Mateyu 19:21-22)
Yesu anamuyangʼana ndi kumukonda nati, “Ukusowa chinthu chimodzi. Pita, kagulitse zonse zimene uli nazo ndipo kapereke kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Ndipo ukabwere ndi kunditsata Ine.” Pa chifukwa ichi nkhope yake inagwa. Anachoka ali wachisoni, chifukwa anali ndi chuma chambiri. (Marko 10:21-22)
Yesu atamva izi, anati kwa iye, “Ukusowabe chinthu chimodzi: Gulitsa zonse zimene uli nazo ndipo uzipereke kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Kenaka ubwere, nunditsate ine.” Atamva zimenezi, anakhumudwa kwambiri chifukwa anali munthu wachuma chambiri. (Luka 18:22-23)
Maganizo pa kupereka
Maganizo a Mulungu
“Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira Iye asatayike koma akhale ndi moyo wosatha. (Yohane 3:16)
Tikudziwa ndipo timadalira chikondi chimene Mulungu ali nacho pa ife. Mulungu ndiye chikondi. Aliyense amene amakhala moyo wachikondi, ali mwa Mulungu ndipo Mulungu amakhala mwa iye. (1 Yohane 4:16)
Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera kumwamba, kwa Atate mwini kuwala, amene sasintha ngati mthunzi woyendayenda. (Yakobo 1:17)
Maganizo athu
Kodi maganizo oyenera ndi otani?
Mwachikondi
Ngati ndipereka zanga zonse kwa osauka ndi kupereka thupi langa kuti alitenthe, koma ngati ndilibe chikondi, ine sindipindula kanthu. (1 Akorinto 13:3)
Mosangalala
Munthu aliyense apereke chimene watsimikiza mu mtima mwake kuti apereka, osati monyinyirika kapena mokakamizidwa, pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwera. (2 Akorinto 9:7)
Kodi timapereka bwanji mwachikondi?
Pereka kwa Ambuye ngati chizindikiro cha chikondi ndi kupembedza
“Uza Aisraeli kuti abweretse chopereka kwa Ine. Iwe ulandire choperekacho mʼmalo mwanga kuchokera kwa munthu amene akupereka mwakufuna kwake. (Eksodo 25:2)
“Pamene ukuchita kalembera wa Aisraeli, munthu aliyense ayenera kupereka kwa Yehova chowombolera moyo wake pamene akuwerengedwa. Motero mliri sudzabwera pa iwo pamene ukuwawerenga. Izi ndi zimene aliyense wolembedwa mu kawundula ayenera kupereka: theka la sekeli, kutanthauza ndalama zolemera magalamu asanu ndi limodzi malingana ndi kawerengedwe ka ndalama za ku Nyumba ya Mulungu. Paja sekeli imodzi ikulingana ndi magera makumi awiri. Theka la sekeli chidzakhala chopereka cha kwa Yehova. Aliyense wolembedwa mu kawundula amene ali ndi zaka makumi awiri kapena kupitirira ayenera kupereka chopereka kwa Yehova. (Eksodo 30:12-14)
Kuchokera pa zomwe muli nazo, mutenge chopereka cha Yehova. Aliyense amene ali ndi mtima wofuna kupereka abweretse kwa Yehova zopereka izi: Golide, siliva ndi mkuwa; (Eksodo 35:5)
...ndipo aliyense amene anakhudzidwa mu mtima mwake nafuna kupereka, anabwera kudzapereka chopereka kwa Yehova cha ntchito yokonza tenti ya msonkhano, cha ntchito zonse za mʼtentimo ndi cha zovala zopatulika. Onse amene anali ndi mtima wofuna, amuna ndi amayi omwe anabwera kudzapereka zodzikometsera zagolide za mtundu uliwonse: zomangira zovala, ndolo, mphete ndi zokometsera. Onse anapereka golide wawo monga nsembe yoweyula pamaso pa Yehova. Aliyense amene anali ndi nsalu ya mtundu wa mtambo, yapepo kapena yofiira kapena yofewa, yosalala, kapena ubweya wambuzi, zikopa za nkhosa zonyika mu utoto wofiira kapena zikopa anazibweretsa. Onse amene anapereka chopereka cha siliva kapena mkuwa anabweretsa monga chopereka kwa Yehova. Ndipo aliyense amene anali ndi matabwa a mtengo wa mkesha kuti awagwiritse ntchito mbali ina iliyonse ya ntchitoyo, anabweretsa. Mayi aliyense waluso analuka ndi manja ake ndi kubweretsa chomwe analuka cha mtundu wa mtambo, chapepo kapena chofiira kapena chofewa, chosalala. Ndipo amayi onse amene anali ndi mtima wofuna ndipo anali ndi luso analuka ubweya wa mbuzi. Atsogoleri anabweretsa miyala ya onikisi ndi miyala yokongola yoyika pa efodi ndi chovala chapachifuwa. Anabweretsanso zonunkhiritsa ndiponso mafuta owunikira a olivi ndi odzozera ndi zofukizira zonunkhira. Aisraeli onse aamuna ndi aakazi amene anali ndi mtima wofuna, anabweretsa kwa Yehova chopereka chaufulu ku ntchito yonse ya Yehova imene analamulira kudzera mwa Mose kuti achite. (Eksodo 35:21-29)
Munthuyo atenge mtanda umodzi pa mtanda wa buledi wa mtundu uliwonse kuti ukhale nsembe yopereka kwa Yehova. Tsono mtanda umenewo ndi wake wa wansembe amene awaze magazi a nsembe yachiyanjano. (Levitiko 7:14)
“Kenaka Yehova anati kwa Aaroni, ona, Ine mwini ndikukuyika kuti ukhale woyangʼanira zopereka zobwera kwa Ine; zopereka zonse zopatulika za Aisraeli zimene amapereka kwa ine ndi kuzipereka kwa iwe ndi ana ako aamuna ngati gawo lanu la nthawi zonse. Uzilandiranso gawo la zopereka zopatulika kwambiri zomwe sizinawotchedwe pa moto. Kuchokera pa mphatso zonse zimene amabweretsa kwa Ine ngati zopatulika kwambiri, nsembe zachakudya kapena nsembe zopepesera machimo, gawo limenelo ndi lako ndi ana ako aamuna. Muzidya zimenezo ngati zinthu zopatulika kwambiri; mwamuna aliyense adyeko. Uzitenge kukhala zopatulika. “Izinso ndi zako: chilichonse chopatulidwa kuchokera ku mphatso zoweyula za Aisraeli ndapereka kwa iwe ndi ana ako aamuna ndi aakazi ngati gawo lako la nthawi zonse. Aliyense wa mʼnyumba mwako amene ali woyeretsedwa monga mwa mwambo angathe kudyako. “Ndikukupatsani mafuta onse abwino kwambiri a olivi ndi vinyo yense watsopano wabwino kwambiri ndi tirigu yense zomwe Aisraeli amapereka kwa Yehova ngati zipatso zoyamba pa zokolola zawo. Zipatso zonse zoyamba kucha za mʼdziko lawo zomwe amapereka kwa Yehova zidzakhala zako. Aliyense mʼnyumba mwako amene ali woyeretsedwa angathe kudyako. “Chilichonse mu Israeli chomwe chapatulidwira Yehova ndi chako. Chilichonse choyamba kubadwa kwa munthu kaya nyama, chomwe chaperekedwa kwa Yehova ndi chako. Koma uyenera kuwombola mwana aliyense wamwamuna ndi mwana aliyense woyamba wa nyama zodetsedwa. Pamene zili ndi mwezi umodzi wa kubadwa, uziwombole pa mtengo wowombolera wa ndalama zisanu zasiliva, monga mwa ndalama za ku malo wopatulika. “Koma usawombole ana oyamba kubadwa a ngʼombe, nkhosa kapena mbuzi. Iwo ndi opatulika. Uwaze magazi a nyamazi pa guwa lansembe ndi kutentha mafuta ake ngati nsembe yotentha ndi moto kuti likhale fungo lokoma kwa Yehova. Nyama yake ikhale yanu monga momwe chimakhalira chidale cha nsembe yoweyula ndi ntchafu za miyendo ya kumanja, zonsezi ndi zako. Zonse zimene mwazichotsa ku zopereka zoyera zomwe Aisraeli anapereka kwa Yehova ndazipereka kwa iwe ndi ana ako aamuna ndi aakazi ngati gawo lanu nthawi zonse. Ili ndi pangano losatha la mchere pamaso pa Yehova kwa iwe ndi ana ako.” Ndipo Yehova anati kwa Aaroni, “Iweyo sudzakhala ndi cholowa mʼdziko lawo, ndiponso sudzalandira gawo lililonse pakati pawo. Ine ndine gawo lako ndi cholowa chako pakati pa Aisraeli. “Taonani, ndawapatsa Alevi chakhumi chonse mu Israeli ngati cholowa chawo chifukwa cha ntchito ya ku tenti ya msonkhano. Kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo Aisraeli asamapite pafupi ndi tenti ya msonkhano. Ngati atero adzasenza zotsatira za tchimo lawo ndipo adzafa. Alevi ndi amene azidzagwira ntchito ya ku tenti ya msonkhano ndipo adzalangidwa chilichonse chikalakwika. Ili ndi lamulo losatha kwa mibado yawo yonse. Iwowo sadzalandira cholowa pakati pa Aisraeli. Mʼmalo mwake, ndikuwapatsa Aleviwo chakhumi ngati cholowa chawo chimene Aisraeli amapereka kwa Yehova. Nʼchifukwa chake zokhudza iwo ndinati: ‘Sadzakhala ndi cholowa pakati pa Aisraeli.’ ” (Numeri 18:8-24)
Mfumu Davide inapereka zinthu zimenezi kwa Yehova, monga anachitira ndi siliva ndi golide zochokera ku mayiko ena onse monga Edomu ndi Mowabu, Aamoni ndi Afilisti, ndi Aamaleki. (1 Mbiri 18:11)
Anthu ambiri anabweretsa zopereka kwa Yehova ku Yerusalemu ndi mphatso zamtengowapatali kwa Hezekiya mfumu ya Yuda. Kuyambira nthawi imeneyo Hezekiya ankalemekezedwa kwambiri ndi mitundu ina yonse. (2 Mbiri 32:23)
Mfumu Davide inapereka zinthu zimenezi kwa Yehova, monga anachitira ndi siliva ndi golide zochokera ku mayiko onse amene anawagonjetsa: (2 Samueli 8:11)
“Pereka nsembe zachiyamiko kwa Mulungu, kwaniritsa malonjezo ako kwa Wammwambamwamba. (Masalimo 50:14)
Ine ndidzabwera ku Nyumba yanu ndi nsembe zopsereza ndi kukwaniritsa malumbiro anga. (Masalimo 66:13)
Chifukwa cha Nyumba yanu ku Yerusalemu, mafumu adzabweretsa kwa Inu mphatso. (Masalimo 68:29)
Chitani malumbiro kwa Yehova Mulungu wanu ndipo muwakwaniritse; anthu onse omuzungulira abweretse mphatso kwa Iye amene ayenera kuopedwa. (Masalimo 76:11)
Pakuti pa phiri langa lopatulika, phiri lalitali la ku Israeli, akutero Ambuye Yehova, Aisraeli onse adzanditumikira, ndipo kumeneko Ine ndidzawalandira. Kumeneko ndidzayembekeza zopereka zanu ndi mphatso zanu zopambana, pamodzi ndi nsembe zanu zonse zopatulika. (Ezekieli 20:40)
“Imirira, puntha, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni, pakuti ndidzakupatsa nyanga zachitsulo; ndidzakupatsa ziboda zamkuwa ndipo udzaphwanya mitundu yambiri ya anthu.” Phindu lawo lolipeza molakwikalo udzalipereka kwa Yehova, chuma chawo kwa Yehova wa dziko lonse lapansi. (Mika 4:13)
Zonse zimene tili nazo zimachokera kwa Ambuye ndipo timazibwezera kwa Iye
“Koma ine ndine yani, ndipo anthu anga ndani, kuti tikupatsani mowolowamanja motere? Zinthu zonse zimachokera kwa Inu, ndipo ife takupatsani zomwe zimachokera mʼdzanja lanu. Ife ndife anthu osadziwika ndiponso alendo pamaso panu, monga analili makolo athu. Masiku anthu pa dziko lapansi ali ngati chithunzithunzi, wopanda chiyembekezo. Inu Yehova Mulungu wathu, zinthu zonse zimene tapereka kumangira Nyumba yanu zachokera mʼdzanja lanu ndipo zonsezi ndi zanu. (1 Mbiri 29:14-16)
Chitsanzo cha Mwana Khristu
Atabadwa Yesu mʼBetelehemu wa ku Yudeya, mʼnthawi ya mfumu Herode, Anzeru a kummawa anabwera ku Yerusalemu (Mateyu 2:1)
Chitsanzo cha kusapereka kwa Ambuye
Simunabweretse kwa Ine nkhosa za nsembe zopsereza, kapena kundilemekeza ndi nsembe zanu. Ine sindinakulemetseni pomakupemphani zopereka za chakudya kapena kukutopetsani pomakupemphani nsembe zofukiza. Simunandigulire bango lonunkhira kapena kundipatsa Ine mafuta okwanira a nsembe zanu. Koma inu mwandilemetsa Ine ndi machimo anu ndipo mwanditopetsa Ine ndi zolakwa zanu. (Yesaya 43:23-24)
Pereka mosangalala pogonjera Ambuye/pereka mwaufulu
...zinthu zagolide ndi zinthu zasiliva, ndiponso zinthu zonse zimene anthu aluso adzagwiritse ntchito. Tsopano ndani amene akufuna kudzipatulira yekha kwa Yehova lero?” Tsono atsogoleri a mabanja, akuluakulu a mafuko a Israeli, olamulira asilikali 1,000, ndi olamulira asilikali 100, ndiponso akuluakulu onse amene amayangʼanira ntchito ya mfumu anapereka mwaufulu. Iwo anapereka ku ntchito ya Nyumba ya Mulungu matani 170 a golide, matani 340 a siliva, matani 620 a mkuwa ndi matani 3,400 a chitsulo. Aliyense amene anali ndi miyala yokongola anayipereka ku nyumba yosungiramo chuma cha Nyumba ya Yehova ndipo amene ankayangʼanira anali Yehieli Mgeresoni. Anthu anakondwa chifukwa cha kupereka mwaufulu kwa atsogoleri awo, pakuti anapereka kwa Yehova mwaufulu ndiponso ndi mtima wonse. Nayenso mfumu Davide anakondwera kwambiri. (1 Mbiri 29:5-9)
“Koma ine ndine yani, ndipo anthu anga ndani, kuti tikupatsani mowolowamanja motere? Zinthu zonse zimachokera kwa Inu, ndipo ife takupatsani zomwe zimachokera mʼdzanja lanu. Ife ndife anthu osadziwika ndiponso alendo pamaso panu, monga analili makolo athu. Masiku anthu pa dziko lapansi ali ngati chithunzithunzi, wopanda chiyembekezo. Inu Yehova Mulungu wathu, zinthu zonse zimene tapereka kumangira Nyumba yanu zachokera mʼdzanja lanu ndipo zonsezi ndi zanu. Mulungu wanga, ine ndikudziwa kuti mumayesa mtima ndipo mumakondwera ndi anthu angwiro. Zinthu zonsezi ndapereka mwaufulu ndi cholinga chabwino. Ndipo tsopano ndaona ndi chimwemwe momwe anthu anu amene ali pano akuperekera mwaufulu kwa Inu. (1 Mbiri 29:14-17)
Ndipo tsopano, abale, tikufuna kuti mudziwe za chisomo chimene Mulungu wapereka ku mipingo ya ku Makedoniya. Pakati pa mayesero owawitsa, chimwemwe chawo chosefukira ndi umphawi wawo otheratu, anapereka mowolowamanja kwambiri. Motero ndikuchitira umboni kuti anapereka mmene akanathera, ndipo mwinanso kuposera mmene akathera kupereka. Anapereka mosakakamizidwa, ndipo anatipempha motiwumiriza kuti tiwapatse mwayi woti nawonso athandize anthu oyera mtima a ku Yudeya. Iwo anachita moposera mmene ife timayembekezera. Choyamba anadzipereka kwa Ambuye ndipo kenaka kwa ife monga mwa chifuniro cha Mulungu. (2 Akorinto 8:1-5)
Maganizo ndi ofunika kuposa kuchuluka kwa zoperekedwa
“Tsoka kwa inu, aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi, achiphamaso! Mumapereka chakhumi cha timbewu tonunkhira ndi cha timbewu tokometsera chakudya. Koma mwasiya zofunikira kwambiri za mʼmalamulo monga chilungamo, chifundo ndi kukhulupirika. Muyenera kuchita zomalizirazi komanso osasiya zoyambazo. (Mateyu 23:23)
“Tsoka kwa inu Afarisi, chifukwa mumapereka kwa Mulungu chakhumi cha timbewu tonunkhira, ndi timbewu tokometsera chakudya ndi mbewu zina zonse za mʼmunda, koma mumakana chilungamo ndi chikondi cha Mulungu. Mumayenera kuchita zomalizirazi osalekanso kuchita zoyambazi. (Luka 11:42)
“Anthu awiri anapita ku Nyumba ya Mulungu kukapemphera, wina Mfarisi ndi winayo wolandira msonkho. Mfarisiyo anayimirira ndipo anapemphera za iye mwini kuti, ‘Mulungu, ine ndikuyamika kuti sindili ngati anthu ena onse, achifwamba, ochita zoyipa, achigololo, sindilinso ngati wolandira msonkhoyu. Ine ndimasala kudya kawiri pa Sabata ndipo ndimapereka chakhumi pa zonse ndimapeza.’ “Koma wolandira msonkhoyo ali chiyimire potero, sanathe nʼkomwe kuyangʼana kumwamba; koma anadziguguda pachifuwa ndipo anati, ‘Mulungu, chitireni chifundo, ine wochimwa.’ “Ine ndikukuwuzani kuti munthu wolandira msonkhoyu, osati Mfarisiyu, anapita kwawo atalungamitsidwa pamaso pa Mulungu. Chifukwa chake, aliyense wodzikweza adzachepetsedwa, ndipo wodzichepetsa adzakwezedwa.” (Luka 18:10-14)
Kupereka ndi maganizo oyenera/Ambuye amalandira mphatso
Nayenso Abele anatenga ana ankhosa oyamba kubadwa pamodzi ndi mafuta ake nakazipereka ngati nsembe kwa Yehova. Yehova anakondwera ndi Abele ndi nsembe yake. (Genesis 4:4)
Ndi chikhulupiriro Abele anapereka kwa Mulungu nsembe yoposa imene Kaini anapereka. Ndi chikhulupiriro anatchedwa munthu wolungama Mulungu atayamikira zopereka zake. Ngakhale iye anafa, akuyankhulabe chifukwa cha chikhulupiriro chakecho. (Ahebri 11:4)
Ndalandira zonse ndipo ndili nazo zokwanira zoposa zosowa zanga popeza ndalandira kwa Epafrodito mphatso zochuluka zimene munatumiza. Ndizo zopereka za fungo labwino, nsembe zolandiridwa zokondweretsa Mulungu. (Afilipi 4:18)
Kupereka ndi maganizo olakwika/Ambuye amakana mphatso
Patapita nthawi, Kaini anatenga zipatso za ku munda nakazipereka kwa Yehova monga nsembe. Nayenso Abele anatenga ana ankhosa oyamba kubadwa pamodzi ndi mafuta ake nakazipereka ngati nsembe kwa Yehova. Yehova anakondwera ndi Abele ndi nsembe yake. Koma sanakondwere ndi Kaini ndi nsembe yake. Kotero Kaini anakwiya kwambiri ndipo nkhope yake inagwa. (Genesis 4:3-5)
“Bwerani ku Beteli mudzachimwe; ndi ku Giligala kuti mudzapitirize kuchimwa. Bweretsani nsembe zanu mmawa uliwonse, bweretsani chakhumi chanu masiku atatu aliwonse. Wotchani buledi wokhala ndi yisiti ngati nsembe yachiyamiko ndi kumanyadira poyera za zopereka zanu zaufulu. Inu Aisraeli, zinyadireni nsembezo, pakuti izi ndi zimene mumakonda kuchita,” akutero Ambuye Yehova. “Ndine amene ndinakusendetsani milomo mʼmizinda yanu yonse, ndipo munasowa chakudya mʼmizinda yanu. Komatu inu simunabwerere kwa Ine,” akutero Yehova. (Amosi 4:4-6)
Ngakhale mupereke nsembe zopsereza ndi nsembe zachakudya, Ine sindidzazilandira. Ngakhale mupereke nsembe zabwino zachiyanjano, Ine sindidzaziyangʼana nʼkomwe. Koma chiweruzo cholungama chiyende ngati madzi, chilungamo ngati mtsinje wosaphwa! (Amosi 5:22, 24)
“Kodi pa zaka makumi anayi zimene munakhala mʼchipululu muja munkandibweretsera nsembe ndi zopereka, inu nyumba ya Israeli? Inu mwanyamula kachisi wa mfumu yanu, ndi nyenyezi ija Kaiwani, mulungu wanu, mafano amene munadzipangira. Nʼchifukwa chake Ine ndidzakupititsani ku ukapolo, kutali kupitirira ku Damasiko,” akutero Yehova, amene dzina lake ndi Mulungu Wamphamvuzonse. (Amosi 5:25-27)
China chimene mumachita ndi ichi: Mumakhathamiritsa guwa lansembe la Yehova ndi misozi. Mumalira ndi kufuwula kwambiri chifukwa Iye amakana kuyangʼana nsembe zanu, kapena kulandira mokondwera nsembe za mʼmanja mwanu. Inu mukufunsa kuti, “Chifukwa chake nʼchiyani?” Chifukwa chake nʼchakuti Yehova ndi mboni ya pangano limene unachita ndi mkazi wa unyamata wako, chifukwa sunakhulupirike kwa iye, ngakhale kuti iyeyo ndiye mnzako, ndi mkazi wako mwapangano. (Malaki 2:13-14)
Kunamiza Mzimu Woyera
Koma munthu wina dzina lake Hananiya, pamodzi ndi mkazi wake Safira, anagulitsanso munda wawo. Mogwirizana ndi mkazi wakeyo anapatulapo pa ndalamazo nazisunga, ndipo anatenga zotsalazo ndi kukapereka kwa atumwi. Koma Petro anamufunsa kuti, “Hananiya, chifukwa chiyani Satana anadzaza chotere mu mtima wako kuti unamize Mzimu Woyera ndipo wapatula ndi kusunga ndalama? Kodi sunali wako usanagulitse? Ndipo utagulitsa ndalamazo sizinali mʼmanja mwako kodi? Nʼchiyani chinakuchititsa zimenezi? Iwe sunanamize anthu koma Mulungu.” Hananiya atamva mawu amenewa anagwa pansi namwalira. Onse amene anamva zimene zinachitikazi anachita mantha kwambiri. Kenaka anyamata anafika, nakulunga thupi lake, ndipo anamunyamula ndi kukamuyika mʼmanda. Patapita maora atatu mkazi wake analowa, wosadziwa zimene zinachitika. Petro anamufunsa iye kuti, “Tandiwuza, kodi izi ndi ndalama zonse zimene iwe ndi Hananiya munalandira mutagulitsa munda?” Mkaziyo anati, “Inde ndi zimenezo.” Petro anati kwa iye, “Bwanji inu munapangana kuyesa Mzimu wa Ambuye? Taona! Anthu amene anakayika mwamuna wako mʼmanda ali pa khomo, ndipo adzakunyamula iwenso.” Nthawi yomweyo anagwa pansi pa mapazi a Petro ndipo anamwalira. Ndipo anyamata aja analowa, napeza kuti wafa kale, anamunyamula ndi kukamuyika pafupi ndi mwamuna wake. (Machitidwe a Atumwi 5:1-10)
Kulungamitsa tchimo
“Ndinayenera kupereka nsembe zachiyanjano. Lero ndakwaniritsa malumbiro anga. (Miyambo 7:14)
Ubwino wa kupereka
Ubwino kwa wopereka
Pa zonse zimene ndinachita, ndinakuonetsani kuti pogwira ntchito molimbika motere tiyenera kuthandiza ofowoka, pokumbukira mawu a Ambuye Yesu akuti, ‘Kupereka kumadalitsa kuposa kulandira.’ ” (Machitidwe a Atumwi 20:35)
Kuyandikira kwambiri Ambuye
Pakuti kumene kuli chuma chako, mtima wako udzakhala komweko. (Mateyu 6:21)
Popeza kumene kuli chuma chanu, mtima wanunso udzakhala komweko.” (Luka 12:34)
Kuwonjezeka kumwamba
Koma mudziwunjikire chuma kumwamba kumene njenjete ndi dzimbiri siziwononga ndipo mbala sizithyola ndi kuba. (Mateyu 6:20)
Yesu anayankha kuti, “Ngati ukufuna kukhala wangwiro, pita kagulitse katundu wako ndi kupereka kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Ukakachita zimenezi, ukabwere udzanditsate Ine.” (Mateyu 19:21)
Gulitsani zonse zimene muli nazo, ndipo ndalama zake mupereke kwa osauka. Dzipezereni zikwama zandalama zimene sizidzatha, ndi kudzikundikira chuma chomwe sichidzatha kumwamba, kumene mbala sizingafikeko, ndipo dzimbiri silingawononge. (Luka 12:33)
“Yankhula ndi Alevi ndi kunena nawo kuti, ‘Pamene mulandira chakhumi kuchoka kwa Aisraeli chimene ndimakupatsani ngati cholowa chanu, muyenera kupereka chakhumi cha choperekacho kwa Yehova. (Numeri 18:26)
Yesu atamva izi, anati kwa iye, “Ukusowabe chinthu chimodzi: Gulitsa zonse zimene uli nazo ndipo uzipereke kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Kenaka ubwere, nunditsate ine.” (Luka 18:22)
Osati ndikufuna mphatso zanu, koma ndikufuna kuti pa zimene muli nazo pawonjezerekepo phindu. (Afilipi 4:17)
Anthu onse amene ali ndi chuma uwalamule kuti asanyade kapena kuyika mitima yawo pa chuma chimene nʼchosadalirika. Koma chiyembekezo chawo chikhale mwa Mulungu amene amatipatsa mowolowamanja zonse zotisangalatsa. Uwalamule kuti azichita zabwino, kuti azikhala olemera pa ntchito zabwino, owolowamanja ndi okonda kugawana zinthu zawo ndi anzawo. Potero adzadziwunjikira chuma chokhalitsa ngati maziko okhazikika a nthawi zakutsogolo, kuti akalandire moyo, umene ndi moyo weniweni. (1 Timoteyo 6:17-19)
Kuwonjezeka pa dziko lapansi
Kumapeto kwa zaka zitatu zilizonse muzibweretsa zakhumi zonse pa zokolola za chaka chimenecho ndi kuzisunga mʼmidzi yanu, kuti Alevi (amene alibe gawo lawo la chuma kapena cholowa chawochawo), alendo, ana ndi akazi amasiye, amene akukhala mʼmizinda yanu akhoza kubwera kudzadya ndi kukhuta. Ndipo kuti akutero Yehova Mulungu wanu akudalitseni pa ntchito zanu zonse. (Deuteronomo 14:28-29)
...ndipo Azariya, mkulu wa ansembe, ochokera ku banja la Zadoki anayankha kuti, “Kuyambira pamene anthu anayamba kubweretsa zopereka zawo ku Nyumba ya Yehova ife takhala ndi zokwanira kudya ndi zina zambiri zosunga, chifukwa Yehova wadalitsa anthu ake, ndipo mulu umenewu ndiye zotsala.” (2 Mbiri 31:10)
Uzilemekeza Yehova ndi chuma chako chonse; zokolola zonse zoyamba kucha uzilemekeza nazonso Yehova. Ukatero nkhokwe zako zidzadzaza ndi zinthu zambiri, ndiponso mitsuko yako idzadzaza ndi vinyo. (Miyambo 3:9-10)
Munthu wina amapatsako anzake zinthu mwaufulu nʼkumangolemererabe; wina amamana chomwe akanatha kupereka, koma kumanka nasawukabe. Munthu wopereka mowolowamanja adzalemera; iye amene amathandiza ena iyenso adzathandizidwa. (Miyambo 11:24-25)
Ponya chakudya chako pa madzi, udzachipezanso patapita masiku ambiri. (Mlaliki 11:1)
Perekani ndipo mudzapatsidwa. Adzakupatsani mʼthumba mwanu muyeso wabwino, wotsenderezeka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Pakuti muyeso umene mumagwiritsa ntchito, ndi omwewo adzakuyeserani.” (Luka 6:38)
Takumbukirani mawu awa: Amene adzala pangʼono, adzakololanso pangʼono, ndipo amene adzala zochuluka, adzakololanso zochuluka. Munthu aliyense apereke chimene watsimikiza mu mtima mwake kuti apereka, osati monyinyirika kapena mokakamizidwa, pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwera. Ndipo Mulungu akhoza kukudalitsani kwambiri, kuti inuyo nthawi zonse mukhale ndi zinthu zokukwanirani, ndiponso ndi zina zochuluka kuti muthandize pa ntchito zonse zabwino. Paja analemba kuti, “Wopereka mphatso zake mowolowamanja kwa osauka, chilungamo chake chimanka mpaka muyaya.” Tsono Mulungu amene amapereka mbewu kwa wofesa, ndiponso chakudya kuti adye, adzaperekanso mbewu mʼnkhokwe zanu ndi kuzichulukitsa. Iye adzachulukitsanso zipatso za chilungamo chanu. Adzakulemeretsani pa zonse kuti mukhale owolowamanja pa nthawi zonse. Ndipo kuwolowamanja kwanu kudzera mwa ife, kudzakhala kuthokoza kwa Mulungu. (2 Akorinto 9:6-11)
Ndipo Mulungu wanga adzakwaniritsa zosowa zanu monga mwa chuma chake chaulemerero mwa Khristu Yesu. (Afilipi 4:19)
Kuyesa Ambuye kuti awonjezere chuma
Bweretsani chakhumi chathunthu ku nyumba yosungira, kuti mukhale chakudya mʼnyumba mwanga.” Akutero Yehova Wamphamvuzonse, “Tandiyesani, ndipo muone ngati sindidzatsekula zipata zakumwamba, ndi kukugwetserani madalitso ochuluka amene mudzasowe malo owayikamo. (Malaki 3:10)
Kuwonjezeka kwa madalitso
Zabwino za zipatso zanu zoyambirira kucha ndiponso mphatso zanu zonse zapadera zidzakhala za ansembe. Inu muziwapatsa chigawo choyamba cha ufa wanu kuti pa nyumba panu pakhale madalitso. (Ezekieli 44:30)
Kumeneko wantchito wa Kenturiyo, amene amamukhulupirira kwambiri, anadwala ndipo anali pafupi kufa. Kenturiyo anamva za Yesu ndipo anatumiza ena a akulu Ayuda kwa Iye kuti abwere adzachiritse wantchito wakeyo. Iwo atafika kwa Yesu, anamudandaulira kwambiri, nati, “Munthuyu ayenera kuthandizidwa chifukwa amakonda mtundu wathu ndipo anatimangira sunagoge wathu.” (Luka 7:2-5)
Ku Yopa kunali wophunzira wina dzina lake Tabita (mʼChigriki amati Dorika) amene nthawi zonse ankachita zachifundo ndiponso kuthandiza osauka. Nthawi imeneyi anadwala ndipo anamwalira, anasambitsa thupi lake, namugoneka mʼchipinda chammwamba. Petro anatulutsa anthu onse mʼchipindamo; ndipo anagwada pansi ndi kupemphera. Anatembenukira mtembo uja nati, “Tabita, dzuka,” Tabita anatsekula maso ake, ndipo ataona Petro anakhala pansi. (Machitidwe a Atumwi 9:36-37, 40)
Ku Kaisareya kunali munthu wina dzina lake Korneliyo, mkulu wa asilikali 100 wa gulu la Italiya. Iye ndi banja lake lonse amapembedza ndi kuopa Mulungu. Iye amathandiza osowa mowolowamanja ndipo amapemphera kwa Mulungu nthawi zonse. Tsiku lina, nthawi ili ngati 3 koloko masana, anaona masomphenya. Anaona bwino ndithu mngelo wa Mulungu, amene anabwera kwa iye ndi kuti, “Korneliyo.” Korneliyo anamuyangʼanitsitsa mngeloyo mwa mantha. Iye anafunsa kuti, “Nʼchiyani kodi Ambuye?” Mngelo anayankha kuti, “Mapemphero ako ndi zachifundo zako zafika pamaso pa Mulungu ngati chikumbutso. Ndipo anati, ‘Korneliyo, Mulungu wamva mapemphero ako ndipo wakumbukira mphatso zako kwa osauka. (Machitidwe a Atumwi 10:1-4, 31)
Kuchuluka kopereka
Chakhumi
Lamulo lisanabwere
Ndipo adalitsike Mulungu Wammwambamwamba amene anapereka adani ako mʼdzanja lako.” Ndipo Abramu anamupatsa iye chakhumi cha zonse anali nazo. (Genesis 14:20)
Pamenepo Yakobo analumbira kwa Yehova nati, “Ngati inu Mulungu mukhala ndi ine, kundiyangʼanira pa ulendo wangawu ndi kundipatsa chakudya ndi chovala; ngati inu mudzandibweretsa kwathu mu mtendere, ndiye kuti mudzakhala Mulungu wanga, ndipo mwala uwu ndawuyimikawu udzakhala Nyumba ya Mulungu. Ine ndidzakupatsani chakhumi cha zinthu zonse zimene mudzandipatse.” (Genesis 28:20-22)
Pansi pa lamulo
“ ‘Chakhumi chilichonse chochokera mʼdziko, kaya ndi tirigu wochokera mʼnthaka kapena chipatso cha mʼmitengo ndi za Yehova. Chimenecho ndi chopatulika kwa Yehova. Ngati munthu afuna kuwombola chakhumi chilichonse, awonjezere pamtengo wake chimodzi mwa zigawo zisanu za mtengowo. Chakhumi cha ngʼombe ndi nkhosa, kapena kuti nyama iliyonse ya khumi imene mʼbusa wayiwerenga idzakhala yopatulikira kwa Yehova. (Levitiko 27:30-32)
Kusapereka chakhumi kunkaonedwa ngati kubera Mulungu
“Kodi munthu angathe kuba za Mulungu? Komatu inu mumandibera. “Koma inu mukufunsa kuti, ‘Kodi timakuberani motani?’ “Pa zakhumi ndi pa zopereka. Mtundu wanu wonse ndinu otembereredwa, chifukwa mukundibera. (Malaki 3:8-9)
Chakhumi chinkadyedwa pamaso pa Ambuye
Muzionetsetsa kuti mukupatula chakhumi pa zokolola zanu chaka chilichonse. Muzidyera chakhumi cha tirigu wanu, vinyo wanu watsopano ndi mafuta, ndi ana oyamba kubadwa a ngʼombe zanu pamaso pa Yehova Mulungu wanu pa malo amene adzasankhe ngati kokhalako dzina lake, kuti muphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu. Koma ngati malo amenewa ali kutali kwambiri ndipo kuti inu mwadalitsidwa ndi Yehova Mulungu wanu, ndipo simungathe kunyamula chakhumi chanu (chifukwa chakuti malo amene Yehova adzasankha kukayikako dzina lake ali kutali kwambiri), ndiye musinthitse chakhumi chanucho ndi siliva, ndipo mutenge silivayo ndi kupita naye kumalo kumene Yehova Mulungu wanu adzasankhe. Gwiritsani ntchito silivayo kugula chilichonse chimene muchifuna monga ngʼombe, nkhosa, vinyo kapena zakumwa zina zosasitsa, kapena china chilichonse chimene muchifuna. Ndipo inu ndi anthu a pa banja panu mudzazidyera komweko pamaso pa Yehova Mulungu wanu ndi kukondwera. (Deuteronomo 14:22-26)
Chakhumi chinkaperekedwa kuthandiza Alevi ndi osauka
“Taonani, ndawapatsa Alevi chakhumi chonse mu Israeli ngati cholowa chawo chifukwa cha ntchito ya ku tenti ya msonkhano. Kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo Aisraeli asamapite pafupi ndi tenti ya msonkhano. Ngati atero adzasenza zotsatira za tchimo lawo ndipo adzafa. Alevi ndi amene azidzagwira ntchito ya ku tenti ya msonkhano ndipo adzalangidwa chilichonse chikalakwika. Ili ndi lamulo losatha kwa mibado yawo yonse. Iwowo sadzalandira cholowa pakati pa Aisraeli. Mʼmalo mwake, ndikuwapatsa Aleviwo chakhumi ngati cholowa chawo chimene Aisraeli amapereka kwa Yehova. Nʼchifukwa chake zokhudza iwo ndinati: ‘Sadzakhala ndi cholowa pakati pa Aisraeli.’ ” (Numeri 18:21-24)
Kumapeto kwa zaka zitatu zilizonse muzibweretsa zakhumi zonse pa zokolola za chaka chimenecho ndi kuzisunga mʼmidzi yanu, kuti Alevi (amene alibe gawo lawo la chuma kapena cholowa chawochawo), alendo, ana ndi akazi amasiye, amene akukhala mʼmizinda yanu akhoza kubwera kudzadya ndi kukhuta. Ndipo kuti akutero Yehova Mulungu wanu akudalitseni pa ntchito zanu zonse. (Deuteronomo 14:28-29)
Mukatha kupatula chakhumi pa zonse zimene mwakolola mʼchaka chachitatu chimene ndi chaka chakhumi, muzichipereka kwa wansembe, mlendo, ana ndi akazi amasiye, kuti pamenepo adye mʼmizinda yanu nakhuta. (Deuteronomo 26:12)
Iyo inalamula anthu amene amakhala mu Yerusalemu kupereka gawo lawo kwa ansembe ndi Alevi kuti iwowo adzipereke ku malamulo a Yehova. Lamuloli atangolilengeza, Aisraeli anapereka mowolowamanja zipatso zoyamba kucha za tirigu, vinyo watsopano, mafuta ndi uchi ndi zonse zomwe nthaka yawo inabereka. Anabweretsa zochuluka kwambiri, chakhumi cha chilichonse. Aisraeli ndi Ayuda amene amakhala mʼmizinda ya Yuda anabweretsanso chakhumi cha ngʼombe zawo ndi nkhosa ndi chakhumi cha zinthu zoyera zoperekedwa kwa Yehova Mulungu wawo, ndipo anaziyika mʼmilumilu. Anayamba kuchita izi mwezi wachitatu ndipo anatsiriza mwezi wachisanu ndi chiwiri. Hezekiya ndi akuluakulu ake atabwera ndi kuona miluyo, anatamanda Yehova ndi kudalitsa anthu ake, Aisraeli. Hezekiya anafunsa ansembe ndi Alevi za miluyi; ndipo Azariya, mkulu wa ansembe, ochokera ku banja la Zadoki anayankha kuti, “Kuyambira pamene anthu anayamba kubweretsa zopereka zawo ku Nyumba ya Yehova ife takhala ndi zokwanira kudya ndi zina zambiri zosunga, chifukwa Yehova wadalitsa anthu ake, ndipo mulu umenewu ndiye zotsala.” Hezekiya analamula kuti akonze zipinda zosungiramo za mʼNyumba ya Yehova, ndipo izi zinachitika. Ndipo iwo mokhulupirika anabweretsa zopereka, chakhumi ndi mphatso zopatulika. Konaniya Mlevi ndiye amayangʼanira zinthu zimenezi ndipo mʼbale wake Simei ndiye anali wachiwiri wake. (2 Mbiri 31:4-12)
“Ndiponso ku zipinda za Nyumba ya Mulungu wathu, kwa ansembe tidzaperekanso mtanda wathu wa buledi wa ufa ndi mphatso zina monga zipatso za mtengo uliwonse, vinyo ndi mafuta. Tidzaperekanso kwa alevi chakhumi cha mbewu zathu pakuti alevi ndiwo amasonkhanitsa chakhumi mʼmidzi yathu yonse. Wansembe, mdzukulu wa Aaroni azikhala pamodzi ndi Alevi pamene akulandira chakhumi. Ndipo Alevi azibwera ndi chakhumicho ku nyumba ya Mulungu wathu, kuzipinda zosungiramo chuma.” (Nehemiya 10:37-38)
Ndinapezanso kuti Alevi sankalandira magawo awo amene amayera kulandira. Chotsatira chake Alevi onse pamodzi ndi oyimba nyimbo amene ankagwira ku Nyumba ya Mulungu anathawa, aliyense kupita ku munda wake. Choncho ndinadzudzula akuluakulu aja ndipo ndinawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani Nyumba ya Mulungu yasiyidwa?” Ndipo ine ndinawayitanitsa pamodzi ndi kuwayika mʼmalo awo. (Nehemiya 13:10-11)
Alevi ankayenera kupereka chakhumi kuchokera pa chakhumi chimene analandira
“Yankhula ndi Alevi ndi kunena nawo kuti, ‘Pamene mulandira chakhumi kuchoka kwa Aisraeli chimene ndimakupatsani ngati cholowa chanu, muyenera kupereka chakhumi cha choperekacho kwa Yehova. (Numeri 18:26)
Chakhumi mu Chipangano Chatsopano
Kuposa kwa unsembe wa Melekizedeki
Melikizedeki ameneyu anali mfumu ya ku Salemu, ndiponso wansembe wa Mulungu Wammwambamwamba. Anakumana ndi Abrahamu pamene ankabwerera kuchokera ku nkhondo atagonjetsa mafumu aja, Melikizedeki anakumana naye namudalitsa. Ndipo Abrahamu anamupatsa chakhumi cha zonse anafunkha. Choyamba dzina la Melikizedeki likutanthauza, “Mfumu ya chilungamo,” kenakanso, “Mfumu ya Salemu,” kutanthauza, “Mfumu ya mtendere.” Mukuona tsono kuti munthuyo anali wamkulu ndithu, pakuti Abrahamu kholo lathu anamupatsa chakhumi cha zimene anafunkha. Tsono lamulo likuti, ana a Levi amene amakhala ansembe azilandira chakhumi kuchokera kwa Aisraeli, abale awo ngakhale kuti abale awowo ndi ochokera kwa Abrahamu. Melikizedeki sanali wochokera kwa Levi, komabe analandira chakhumi kuchokera kwa Abrahamu nadalitsa Abrahamuyo amene analandira malonjezo a Mulungu. Mosakayika konse, munthu amene amadalitsa ndi wamkulu kuposa amene akudalitsidwayo. Ansembe amene amalandira chakhumi amafa, choncho Melikizedeki ndi wamkulu kuwaposa iwo chifukwa Malemba amamuchitira umboni kuti ndi wamoyo. Wina angathe kunena kuti Levi, amene amalandira chakhumi, anapereka chakhumicho kudzera mwa Abrahamu, (Ahebri 7:1-2, 4-9)
Chakhumi mʼnyumba yosungiramo
Hezekiya analamula kuti akonze zipinda zosungiramo za mʼNyumba ya Yehova, ndipo izi zinachitika. Ndipo iwo mokhulupirika anabweretsa zopereka, chakhumi ndi mphatso zopatulika. Konaniya Mlevi ndiye amayangʼanira zinthu zimenezi ndipo mʼbale wake Simei ndiye anali wachiwiri wake. (2 Mbiri 31:11-12)
Wansembe, mdzukulu wa Aaroni azikhala pamodzi ndi Alevi pamene akulandira chakhumi. Ndipo Alevi azibwera ndi chakhumicho ku nyumba ya Mulungu wathu, kuzipinda zosungiramo chuma.” (Nehemiya 10:38)
Tsiku limenelo panasankhidwa anthu oyangʼanira zipinda zosungiramo zopereka zaufulu, zipatso zoyamba kucha, zopereka za chakhumi. Anthuwo ankasonkhanitsa zopereka kuchokera ku minda ya midzi yonse kuti azipereke kwa ansembe ndi Alevi malingana ndi malamulo. Izi zinali chomwechi chifukwa Ayuda ankakondwera ndi utumiki wa ansembe ndi Alevi. (Nehemiya 12:44)
Pambuyo pake Ayuda anayambanso kubwera ndi zopereka zawo za chakhumi cha tirigu, vinyo ndi mafuta kuti ziperekedwe ku nyumba yosungiramo chuma. (Nehemiya 13:12)
Kupereka molingana ndi mmene Mulungu wakudalitsira
Pamenepo muzichita Chikondwerero cha Masabata pamaso pa Yehova Mulungu wanu popereka chopereka chaufulu mofanana ndi madalitso amene Yehova Mulungu wakupatsani (Deuteronomo 16:10)
Amuna onse azionekera pamaso pa Yehova Mulungu katatu pa chaka ku malo amene Iye adzasankha. Pa Chikondwerero cha Buledi wopanda Yisiti, pa Chikondwerero cha Masabata ndi pa Chikondwerero cha Misasa. Munthu aliyense asadzapite pamaso pa Yehova wopanda kanthu mʼmanja mwake. (Deuteronomo 16:16)
Pa tsiku loyamba la sabata lililonse, aliyense wa inu azipatula ndalama molingana ndi zomwe wapezera. Asunge, kuti ndikabwera pasadzakhalenso msonkhamsonkha. (1 Akorinto 16:2)
Zitsanzo za kupereka molingana ndi kuthekera
Anapereka kwa msungichuma wa ntchitoyo molingana ndi mmene aliyense chuma chake chinalili: golide wa makilogalamu 500, siliva makilogalamu 2,800 ndi zovala za ansembe zokwanira 100. (Ezara 2:69)
Ophunzirawo, aliyense monga mwakupata kwake, anatsimikiza kuthandiza abale okhala ku Yudeya. (Machitidwe a Atumwi 11:29)
Chovomerezeka ndi chimene chaperekedwa molingana ndi kuthekera kwa munthu
Ndipo ngati mtima ofunitsitsa ulipo, mphatsoyo imalandiridwa molingana ndi zimene munthuyo ali nazo, osati zimene alibe. (2 Akorinto 8:12)
Kupereka modzipereka
Yesu anakhala pansi moyangʼanana ndi pamene amaperekera zopereka ndipo amaona anthu akupereka ndalama zawo mʼthumba la Nyumba ya Mulungu. Anthu ambiri olemera anaponya ndalama zambiri. Koma mkazi wamasiye, wosauka anabwera ndi kuyikamo tindalama tiwiri ta kopala, tongokwanira theka la ndalama. Yesu anayitana ophunzira ake nati, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti mayi wosauka wamasiyeyu waponya zambiri mʼthumbali kuposa ena onsewa. Iwo apereka molingana ndi chuma chawo; koma iye, mwaumphawi wake, wapereka zonse anali nazo ngakhale zoti akanagulira chakudya.” (Marko 12:41-44)
Yesu atayangʼana, anaona olemera akuyika mphatso zawo mu chosungira ndalama za mʼNyumba ya Mulungu. Iye anaonanso mkazi wamasiye wosauka akuyikamo timakopala tiwiri. Iye anati, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti mkazi wamasiye wosaukayu wapereka zambiri kuposa ena onsewa. Anthu onsewa atapa mphatso zawo kuchokera pa zochuluka zimene ali nazo; koma uyu, mwa umphawi wake, wapereka zonse zimene ali nazo.” (Luka 21:1-4)
Ndipo tsopano, abale, tikufuna kuti mudziwe za chisomo chimene Mulungu wapereka ku mipingo ya ku Makedoniya. Pakati pa mayesero owawitsa, chimwemwe chawo chosefukira ndi umphawi wawo otheratu, anapereka mowolowamanja kwambiri. Motero ndikuchitira umboni kuti anapereka mmene akanathera, ndipo mwinanso kuposera mmene akathera kupereka. Anapereka mosakakamizidwa, ndipo anatipempha motiwumiriza kuti tiwapatse mwayi woti nawonso athandize anthu oyera mtima a ku Yudeya. (2 Akorinto 8:1-4)
Usapereke chinthu chimene sichikukuwonongetsa kanthu
Arauna anati, “Nʼchifukwa chiyani mbuye wanga mfumu mwabwera kwa mtumiki wanu?” Davide anayankha kuti, “Kudzagula malo ako opunthira tirigu kuti ndimangire Yehova guwa lansembe kuti mliri uli pa anthuwa usiye.” Arauna anati kwa Davide, “Mbuye wanga mfumu mutenge chilichonse chimene chikukondweretseni ndi kuchipereka nsembe. Nazi ngʼombe zazimuna za nsembe yopsereza, nazi zopunthira tirigu ndi magoli angʼombe kuti zikhale nkhuni. Inu mfumu, Arauna akupereka zonsezi kwa inu mfumu.” Arauna anatinso kwa iye, “Yehova Mulungu wanu akuvomerezeni.” Koma mfumu inayankha Arauna kuti, “Ayi, Ine ndikunenetsa kuti ndikulipira. Sindidzapereka kwa Yehova Mulungu wanga nsembe yopsereza imene sindinavutikire.” Kotero Davide anagula malo wopunthira tiriguwo ndi ngʼombe ndipo anapereka kwa Araunayo masekeli asiliva makumi asanu. (2 Samueli 24:21-24)
Davide anati kwa Arauna, “Undipatse malo ako opunthira tirigu kuti ndimangire Yehova guwa lansembe, kuti mliri uli pa anthuwa usiye. Undigulitse ine pa mtengo woyenera ndithu.” Arauna anati kwa Davide, “Tengani! Mbuye wanga mfumu achite chomukomera. Taonani ine ndidzapereka ngʼombe zazimuna za nsembe yopsereza, zopunthira tirigu zidzakhala nkhuni ndipo tiriguyu adzakhala chopereka chachakudya. Ndidzapereka zonsezi.” Koma mfumu Davide inayankha Arauna kuti, “Ayi, ine ndikuti ndipereka mtengo wathunthu. Sindingatenge chinthu chako ndi kuchipereka kwa Yehova, kapena kupereka nsembe imene sindinayigule.” (1 Mbiri 21:22-24)
Temberero popereka chakuba kapena cholakwika
“Mwana amalemekeza abambo ake, ndipo wantchito amaopa abwana ake. Ngati Ine ndine abambo anu, ulemu wanga uli kuti? Ngati ndine mbuye wanu, nanga kundiopa kuli kuti?” Akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Ndinu, inu ansembe, amene mumanyoza dzina langa. “Komatu mukufunsa kuti, ‘Kodi timanyoza dzina lanu bwanji?’ “Inu mwanyoza dzina langa popereka chakudya chodetsedwa pa guwa langa lansembe. “Komatu mukufunsa kuti, ‘Kodi ife takunyozani bwanji?’ “Mwandinyoza ponena kuti tebulo la Yehova ndi lonyozeka. Mukamapereka nsembe nyama zosaona, kodi sicholakwa? Mukamapereka nsembe nyama zachilema kapena zodwala, kodi sicholakwa? Kayeseni kuzipereka kwa bwanamkubwa wanu! Kodi akasangalatsidwa nanu? Kodi akazilandira? Akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Tsopano tayesani kupempha Mulungu kuti akuchitireni chifundo. Kodi ndi zopereka zotere mʼmanja mwanu, Iye angakulandireni?” Akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Ndikulakalaka mmodzi wa inu akanatseka zitseko za Nyumba ya Mulungu, kuti musayatsemo moto pachabe pa guwa langa lansembe! Ine sindikukondwera nanu,” akutero Yehova Wamphamvuzonse, “ndipo Ine sindidzalandira zopereka za mʼmanja mwanu. Dzina langa lidzalemekezedwa pakati pa mitundu ya anthu, kuchokera kummawa mpaka kumadzulo. Mʼmalo monse adzapereka nsembe zofukiza ndi zopereka zangwiro mʼdzina langa, chifukwa dzina langa lidzakhala lalikulu pakati pa mitundu ya anthu,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Koma inu mumalinyoza ponena kuti tebulo la Ambuye, ‘ndi lodetsedwa,’ ndipo chakudya chake, ‘nʼchonyozeka!’ Ndipo inu mumati, ‘Ndi zotopetsa zimenezi!’ Ndipo mumandinyogodola Ine,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Pamene inu mubweretsa nyama zakuba, zolumala kapena zodwala ndi kupereka nsembe, kodi Ine ndizilandire kuchokera mʼmanja mwanu?” Akutero Yehova. “Atembereredwe munthu wachinyengo amene ali ndi nyama yayimuna yabwino mʼgulu la ziweto zake ndipo analumbira kuyipereka, koma mʼmalo mwake nʼkupereka nsembe kwa Ambuye nyama yosayenera. Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Pakuti ndine mfumu yayikulu, dzina langa liyenera kuopedwa pakati pa anthu a mitundu yonse.’ ” (Malaki 1:6-14)
Njira yoperekera
“Mwana amalemekeza abambo ake, ndipo wantchito amaopa abwana ake. Ngati Ine ndine abambo anu, ulemu wanga uli kuti? Ngati ndine mbuye wanu, nanga kundiopa kuli kuti?” Akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Ndinu, inu ansembe, amene mumanyoza dzina langa. “Komatu mukufunsa kuti, ‘Kodi timanyoza dzina lanu bwanji?’ “Inu mwanyoza dzina langa popereka chakudya chodetsedwa pa guwa langa lansembe. “Komatu mukufunsa kuti, ‘Kodi ife takunyozani bwanji?’ “Mwandinyoza ponena kuti tebulo la Yehova ndi lonyozeka. Mukamapereka nsembe nyama zosaona, kodi sicholakwa? Mukamapereka nsembe nyama zachilema kapena zodwala, kodi sicholakwa? Kayeseni kuzipereka kwa bwanamkubwa wanu! Kodi akasangalatsidwa nanu? Kodi akazilandira? Akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Tsopano tayesani kupempha Mulungu kuti akuchitireni chifundo. Kodi ndi zopereka zotere mʼmanja mwanu, Iye angakulandireni?” Akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Ndikulakalaka mmodzi wa inu akanatseka zitseko za Nyumba ya Mulungu, kuti musayatsemo moto pachabe pa guwa langa lansembe! Ine sindikukondwera nanu,” akutero Yehova Wamphamvuzonse, “ndipo Ine sindidzalandira zopereka za mʼmanja mwanu. Dzina langa lidzalemekezedwa pakati pa mitundu ya anthu, kuchokera kummawa mpaka kumadzulo. Mʼmalo monse adzapereka nsembe zofukiza ndi zopereka zangwiro mʼdzina langa, chifukwa dzina langa lidzakhala lalikulu pakati pa mitundu ya anthu,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Koma inu mumalinyoza ponena kuti tebulo la Ambuye, ‘ndi lodetsedwa,’ ndipo chakudya chake, ‘nʼchonyozeka!’ Ndipo inu mumati, ‘Ndi zotopetsa zimenezi!’ Ndipo mumandinyogodola Ine,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Pamene inu mubweretsa nyama zakuba, zolumala kapena zodwala ndi kupereka nsembe, kodi Ine ndizilandire kuchokera mʼmanja mwanu?” Akutero Yehova. “Atembereredwe munthu wachinyengo amene ali ndi nyama yayimuna yabwino mʼgulu la ziweto zake ndipo analumbira kuyipereka, koma mʼmalo mwake nʼkupereka nsembe kwa Ambuye nyama yosayenera. Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Pakuti ndine mfumu yayikulu, dzina langa liyenera kuopedwa pakati pa anthu a mitundu yonse.’ ” (Malaki 1:6-14)
Chitsanzo cha kupereka
Choyamba
“Muzidzala mbewu zanu mʼmunda ndi kumakolola mbewuzo kwa zaka zisanu ndi chimodzi. Koma chaka chachisanu ndi chiwiri muzisiya osalima mindayo kuti anthu osauka pakati panu azipezamo chakudya, ndipo nyama zakuthengo zizidya zotsalazo. Muzichita chimodzimodzi ndi minda ya mpesa ndi mitengo ya olivi. (Eksodo 23:10-11)
“Mwana aliyense woyamba kubadwa ndi wanga, pamodzi ndi ziweto zoyamba kubadwa zazimuna kuchokera ku ngʼombe kapena nkhosa. (Eksodo 34:19)
“Muzibwera ndi zipatso zoyambirira kucha zabwino kwambiri ku nyumba ya Yehova Mulungu wanu. “Musamaphike kamwana kambuzi mu mkaka wa mayi wake.” (Eksodo 34:26)
Ziwirizi ungathe kubwera nazo kwa Yehova ngati chopereka cha zokolola zoyambirira. Koma usazitenthe pa guwa kuti zikhale fungo lokomera Yehova. (Levitiko 2:12)
“ ‘Pa tsiku la zipatso zoyambirira kucha, pamene mukupereka chopereka cha chakudya chatsopano kwa Yehova, pa nthawi ya chikondwerero cha Masabata, muzichita msonkhano wopatulika ndipo musagwire ntchito zolemetsa. (Numeri 28:26)
Mukalowa ndi kukhazikika mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ngati cholowa chanu, mutengeko zina mwa zipatso zoyamba pa zonse zimene mudzakola mʼnthaka ya dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ndi kuziyika mʼdengu. Mukatero mupite kumalo kumene Yehova Mulungu wanu adzakhazikitsako dzina lake (Deuteronomo 26:1-2)
Uzilemekeza Yehova ndi chuma chako chonse; zokolola zonse zoyamba kucha uzilemekeza nazonso Yehova. (Miyambo 3:9)
Mwamsanga
“Musachedwe kupereka kwa Ine zokolola zanu zochuluka ndi vinyo wanu wochuluka. “Mundipatse ana anu achisamba aamuna. (Eksodo 22:29)
Mukalumbira kupereka kanthu kwa Yehova Mulungu wanu, musamachedwetse kupereka, chifukwa Yehova Mulungu wanu adzakufunsanibe kanthuko ndipo mudzapezeka wochimwa. (Deuteronomo 23:21)
Pamene ulumbira kwa Mulungu usachedwe kukwaniritsa chimene walumbiracho. Iye sakondweretsedwa ndi chitsiru; kwaniritsa lumbiro lako. (Mlaliki 5:4)
Mokonzekeratu
Munthu aliyense apereke chimene watsimikiza mu mtima mwake kuti apereka, osati monyinyirika kapena mokakamizidwa, pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwera. (2 Akorinto 9:7)
Nthawi zonse
Pa tsiku loyamba la sabata lililonse, aliyense wa inu azipatula ndalama molingana ndi zomwe wapezera. Asunge, kuti ndikabwera pasadzakhalenso msonkhamsonkha. (1 Akorinto 16:2)
Payekha
Muziwombola mwana woyamba kubadwa wa bulu popereka mwana wankhosa. Mukapanda kumuwombola mupheni. Muziwombola ana anu onse aamuna. “Palibe ndi mmodzi yemwe adzaonekere pamaso panga wopanda kanthu mʼdzanja lake. (Eksodo 34:20)
Aliyense wa inu adzabweretse mphatso molingana ndi momwe Yehova Mulungu wanu wakudalitsirani. (Deuteronomo 16:17)
Anthu onse a mʼdzikomo azidzapereka zimenezi kwa mfumu ya Israeli. (Ezekieli 45:16)
Ophunzirawo, aliyense monga mwakupata kwake, anatsimikiza kuthandiza abale okhala ku Yudeya. (Machitidwe a Atumwi 11:29)
Pa tsiku loyamba la sabata lililonse, aliyense wa inu azipatula ndalama molingana ndi zomwe wapezera. Asunge, kuti ndikabwera pasadzakhalenso msonkhamsonkha. (1 Akorinto 16:2)
Kusunga mwachinsinsi
Pa tsiku loyamba la sabata lililonse, aliyense wa inu azipatula ndalama molingana ndi zomwe wapezera. Asunge, kuti ndikabwera pasadzakhalenso msonkhamsonkha. (1 Akorinto 16:2)
Popanda kunyada
“Samalani kuti musachite ntchito zanu zolungama pamaso pa anthu kuti akuoneni. Popeza ngati mutero simudzalandira mphotho yochokera kwa Atate anu akumwamba. “Pamene mupereka zachifundo, musachite modzionetsera monga amachita achiphamaso mʼmasunagoge ndi pa misewu kuti atamidwe ndi anthu. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti iwowo alandiriratu mphotho yawo yonse. Koma pamene mupereka zachifundo, dzanja lanu lamanzere lisadziwe chimene dzanja lanu lamanja likuchita, kotero kuti kupereka kwanu kukhale mwachinsinsi. Ndipo Atate anu amene amaona zochitika mwachinsinsi, adzakupatsani mphotho. (Mateyu 6:1-4)
Kuchokera pansi pa mtima
“Uza Aisraeli kuti abweretse chopereka kwa Ine. Iwe ulandire choperekacho mʼmalo mwanga kuchokera kwa munthu amene akupereka mwakufuna kwake. (Eksodo 25:2)
Kuchokera pa zomwe muli nazo, mutenge chopereka cha Yehova. Aliyense amene ali ndi mtima wofuna kupereka abweretse kwa Yehova zopereka izi: Golide, siliva ndi mkuwa; (Eksodo 35:5)
...ndipo aliyense amene anakhudzidwa mu mtima mwake nafuna kupereka, anabwera kudzapereka chopereka kwa Yehova cha ntchito yokonza tenti ya msonkhano, cha ntchito zonse za mʼtentimo ndi cha zovala zopatulika. Onse amene anali ndi mtima wofuna, amuna ndi amayi omwe anabwera kudzapereka zodzikometsera zagolide za mtundu uliwonse: zomangira zovala, ndolo, mphete ndi zokometsera. Onse anapereka golide wawo monga nsembe yoweyula pamaso pa Yehova. Aliyense amene anali ndi nsalu ya mtundu wa mtambo, yapepo kapena yofiira kapena yofewa, yosalala, kapena ubweya wambuzi, zikopa za nkhosa zonyika mu utoto wofiira kapena zikopa anazibweretsa. Onse amene anapereka chopereka cha siliva kapena mkuwa anabweretsa monga chopereka kwa Yehova. Ndipo aliyense amene anali ndi matabwa a mtengo wa mkesha kuti awagwiritse ntchito mbali ina iliyonse ya ntchitoyo, anabweretsa. Mayi aliyense waluso analuka ndi manja ake ndi kubweretsa chomwe analuka cha mtundu wa mtambo, chapepo kapena chofiira kapena chofewa, chosalala. Ndipo amayi onse amene anali ndi mtima wofuna ndipo anali ndi luso analuka ubweya wa mbuzi. Atsogoleri anabweretsa miyala ya onikisi ndi miyala yokongola yoyika pa efodi ndi chovala chapachifuwa. Anabweretsanso zonunkhiritsa ndiponso mafuta owunikira a olivi ndi odzozera ndi zofukizira zonunkhira. Aisraeli onse aamuna ndi aakazi amene anali ndi mtima wofuna, anabweretsa kwa Yehova chopereka chaufulu ku ntchito yonse ya Yehova imene analamulira kudzera mwa Mose kuti achite. (Eksodo 35:21-29)
Yowasi anati kwa ansembe, “Tolerani ndalama zonse zimene zimaperekedwa monga chopereka chopatulika ku Nyumba ya Yehova, ndalama zonse zamsonkho wa munthu aliyense, ndalama zomwe munthu amapereka akalonjeza ndiponso ndalama zimene munthu amapereka mwaufulu ku Nyumba ya Yehova. (2 Mafumu 12:4)
Malamulo a kupereka
Kuyangʼanira ndi kuyankha mlandu
Abale awo Alevi, motsogozedwa ndi Ahiya, anali oyangʼanira chuma cha nyumba ya Mulungu ndi zinthu zoperekedwa kwa Mulungu. (1 Mbiri 26:20)
Selomiti ndi abale ake amayangʼanira zinthu zonse zoperekedwa kwa Mulungu ndi mfumu Davide, atsogoleri a mabanja amene anali olamulira ankhondo 1,000, olamulira ankhondo 100, ndi olamulira ankhondo ena. (1 Mbiri 26:26)
Kore mwana wa Imuna Mlevi, mlonda wa Chipata Chakummawa, amayangʼanira zopereka zaufulu kwa Mulungu, ankagawa zopereka za kwa Yehova ndiponso mphatso zopatulika. Edeni, Miniyamini, Yesuwa, Semaya, Amariya, Sekaniya amamuthandiza mokhulupirika mʼmizinda yonse a ansembe kugawira kwa ansembe anzawo monga mwa magulu awo, aakulu ndi aangʼono omwe. (2 Mbiri 31:14-15)
Tsiku limenelo panasankhidwa anthu oyangʼanira zipinda zosungiramo zopereka zaufulu, zipatso zoyamba kucha, zopereka za chakhumi. Anthuwo ankasonkhanitsa zopereka kuchokera ku minda ya midzi yonse kuti azipereke kwa ansembe ndi Alevi malingana ndi malamulo. Izi zinali chomwechi chifukwa Ayuda ankakondwera ndi utumiki wa ansembe ndi Alevi. (Nehemiya 12:44)
Ndipo ndinasankha wansembe Selemiya, mlembi Zadoki, ndi Mlevi wotchedwa Pedaya kukhala oyangʼanira zipinda zosungiramo. Ndinasankhanso Hanani mwana wa Zakuri mwana wa Mataniya kukhala wowathandizira chifukwa ndinaona kuti anthu awa anali odalirika. Ntchito yawo inali yogawira abale awo zinthu zofunika. (Nehemiya 13:13)
Ndipo tikumutumiza pamodzi ndi mʼbale amene mipingo yonse yamuyamikira chifukwa cha utumiki wake wa Uthenga Wabwino. Chowonjezera china nʼchakuti anasankhidwa ndi mipingo kuti atiperekeze pamene ife tikukapereka zopereka, zimene tikuchita pofuna kupereka ulemu kwa Ambuye mwini ndi kuonetsa kufunitsitsa kwathu pothandiza. Tikufuna kupewa kutikayikira kulikonse za mmene tikuyendetsera mphatso zochulukazi. Pakuti tikuyesetsa kuchita zolondola, osati pamaso pa Ambuye pokha komanso pamaso pa anthu. (2 Akorinto 8:18-21)
Izi anazichitadi ndipo anatuma Barnaba ndi Saulo kukapereka mphatsozo kwa akulu a mpingo. (Machitidwe a Atumwi 11:30)
Pamenepo, ndikadzafika, ndidzawapatsa makalata a umboni anthu amene mudzawasankhe ndi kuwatuma kuti akapereka mphatso zanu ku Yerusalemu. Ngati kutaoneka kuti nʼkoyenera kuti ndipite nawo, adzapita nane limodzi. (1 Akorinto 16:3-4)
Zitsanzo zimene sanafunse kuyankha mlandu
Koma sanawafunse kuti afotokoze kagwiritsidwe ntchito ka ndalama zolipira amene ankagwira ntchito, chifukwa anthuwo ankagwira ntchitoyo mokhulupirika kwambiri. (2 Mafumu 12:15)
Koma anthu amene apatsidwa ndalama zolipira antchito okonza Nyumbayo asawafunse za kagwiritsidwe ntchito ka ndalamazo, popeza ndi anthu wokhulupirika.” (2 Mafumu 22:7)
Komwe tingapereke
Banja
Ngati wina sasamalira abale ake, makamaka a mʼbanja mwake mwenimweni, ameneyo wakana chikhulupiriro ndipo ndi woyipa kuposa wosakhulupirira. (1 Timoteyo 5:8)
Makolo
Pakuti Mulungu anati, ‘Lemekeza abambo ako ndi amayi ako’ ndipo ‘aliyense amene atemberera abambo ake kapena amayi ake ayenera kuphedwa.’ Koma inu mumati, ngati munthu anena kwa abambo ake kapena amayi ake kuti, ‘Thandizo lililonse mukalirandira kuchokera kwa ine ndi mphatso yoperekedwa kwa Mulungu,’ iye sakulemekeza nayo abambo ake ndipo ndi khalidwe lotere inu mumapeputsa nalo Mawu a Mulungu chifukwa cha mwambo wanu. (Mateyu 15:4-6)
Ndipo anawawuzanso kuti, “Inu muli ndi njira yabwino yokankhira kumbali malamulo a Mulungu kuti mukatsatire miyambo yanuyo! Pakuti Mose anati, ‘Lemekeza abambo ako ndi amayi ako,’ ndipo, ‘aliyense amene atemberera abambo ake kapena amayi ake ayenera kuphedwa.’ Koma inu mumati, ngati munthu anena kwa abambo ake kapena amayi ake kuti, ‘Thandizo lililonse mukanayenera kulandira kuchokera kwa ine ndi Korobani’ (kutanthauza kuti, mphatso yoperekedwa kwa Mulungu), pamenepo inu simumalola kuti achitire kanthu kalikonse abambo kapena amayi ake. Potero mumachepetsa mawu a Mulungu kukhala wopanda mphamvu ndi miyambo yanu imene mumapatsirana. Ndipo mumachita zinthu zina zambiri monga zimenezi.” (Marko 7:9-13)
Akazi amasiye
Koma ngati mkazi wamasiye ali ndi ana ndi zidzukulu, anawo ayambe aphunzira kukwaniritsa udindo wawo pa banja lawo moopa Mulungu, potero akubweza zabwino kwa makolo awo ndi agogo awo. Pakuti zimenezi ndiye zimakondweretsa Mulungu. (1 Timoteyo 5:4)
Ngati mayi aliyense wokhulupirira ali ndi akazi amasiye amene akuwasamalira, apitirizebe kuwasamalira ndipo asalemetse mpingo, kuti mpingo uthandize akazi amasiye amene ali okhaokha. (1 Timoteyo 5:16)
Chitsanzo cha kupereka kwa banja
Ine ndizidzakupatsani zakudya kumeneko chifukwa zaka zisanu za njala zikubwera ndithu. Kupanda kutero, inu ndi mabanja anu pamodzi ndi anthu anu onse mudzasowa chakudya.’ (Genesis 45:11)
Yosefe anaperekanso chakudya kwa abambo ake, kwa abale ake ndi kwa onse a mʼnyumba ya abambo ake monga mwa chiwerengero cha ana awo. (Genesis 47:12)
Chitsanzo cha kupereka kwa banja
Zotsala za nsembe ya chakudyazo ndi za Aaroni pamodzi ndi ana ake. Chimenechi ndi chigawo chopatulika kwambiri chifukwa chatapidwa pa chopereka chotentha pa moto cha Yehova. (Levitiko 2:3)
Munthuyo atenge mtanda umodzi pa mtanda wa buledi wa mtundu uliwonse kuti ukhale nsembe yopereka kwa Yehova. Tsono mtanda umenewo ndi wake wa wansembe amene awaze magazi a nsembe yachiyanjano. (Levitiko 7:14)
Mumupatse wansembe ntchafu ya kumanja ya nsembe yanu yachiyanjano kuti ikhale chopereka chanu kwa iye. Mwana wa Aaroni amene amapereka magazi ndi mafuta a nsembe yachiyanjano, adzitenga ntchafu ya kumanja kukhala gawo lake. Choncho pa zopereka zachiyanjano za Aisraeli, Ine ndatengapo chidale chomwe amaweyula ndi ntchafu zimene amapereka nsembe ndipo ndazipereka kwa wansembe Aaroni ndi ana ake. Izi ndizo gawo lawo nthawi zonse pa zopereka za Aisraeli.” (Levitiko 7:32-34)
Mose anawuza Aaroni ndi ana ake otsalawo, Eliezara ndi Itamara kuti, “Tengani zopereka zachakudya zopanda yisiti zimene zatsala pa nsembe zopsereza za kwa Yehova ndipo muzidye pafupi ndi guwa pakuti ndi zopatulika kwambiri. Muzidye pa malo wopatulika chifukwa zimenezi ndi gawo lako ndi la ana ako pa zopereka zopsereza kwa Yehova. Izitu ndi zimene Yehova anandilamulira. Koma iwe pamodzi ndi ana ako aamuna ndi aakazi muzidya chidale chimene chinaweyulidwa ndi ntchafu zimene zinaperekedwa nsembe. Muzidye pamalo woyeretsedwa. Zimenezi zaperekedwa kwa iwe ndi ana ako monga gawo lanu pa zopereka zachiyanjano zimene apereka Aisraeli. (Levitiko 10:12-14)
Ngati wolakwiridwayo alibe mʼbale komwe kungapite zinthu zobwezedwazo, zinthuzo zikhale za Yehova ndipo azipereke kwa wansembe, pamodzi ndi nkhosa yayimuna ya nsembe yopepesera tchimo lake. Zopereka zonse zopatulika zomwe Aisraeli abwera nazo kwa wansembe zikhale za wansembeyo. Mphatso zilizonse zopatulika ndi za munthuyo, koma zomwe wapereka kwa wansembe ndi za wansembeyo.’ ” (Numeri 5:8-10)
“Kenaka Yehova anati kwa Aaroni, ona, Ine mwini ndikukuyika kuti ukhale woyangʼanira zopereka zobwera kwa Ine; zopereka zonse zopatulika za Aisraeli zimene amapereka kwa ine ndi kuzipereka kwa iwe ndi ana ako aamuna ngati gawo lanu la nthawi zonse. Uzilandiranso gawo la zopereka zopatulika kwambiri zomwe sizinawotchedwe pa moto. Kuchokera pa mphatso zonse zimene amabweretsa kwa Ine ngati zopatulika kwambiri, nsembe zachakudya kapena nsembe zopepesera machimo, gawo limenelo ndi lako ndi ana ako aamuna. Muzidya zimenezo ngati zinthu zopatulika kwambiri; mwamuna aliyense adyeko. Uzitenge kukhala zopatulika. “Izinso ndi zako: chilichonse chopatulidwa kuchokera ku mphatso zoweyula za Aisraeli ndapereka kwa iwe ndi ana ako aamuna ndi aakazi ngati gawo lako la nthawi zonse. Aliyense wa mʼnyumba mwako amene ali woyeretsedwa monga mwa mwambo angathe kudyako. “Ndikukupatsani mafuta onse abwino kwambiri a olivi ndi vinyo yense watsopano wabwino kwambiri ndi tirigu yense zomwe Aisraeli amapereka kwa Yehova ngati zipatso zoyamba pa zokolola zawo. Zipatso zonse zoyamba kucha za mʼdziko lawo zomwe amapereka kwa Yehova zidzakhala zako. Aliyense mʼnyumba mwako amene ali woyeretsedwa angathe kudyako. “Chilichonse mu Israeli chomwe chapatulidwira Yehova ndi chako. Chilichonse choyamba kubadwa kwa munthu kaya nyama, chomwe chaperekedwa kwa Yehova ndi chako. Koma uyenera kuwombola mwana aliyense wamwamuna ndi mwana aliyense woyamba wa nyama zodetsedwa. Pamene zili ndi mwezi umodzi wa kubadwa, uziwombole pa mtengo wowombolera wa ndalama zisanu zasiliva, monga mwa ndalama za ku malo wopatulika. “Koma usawombole ana oyamba kubadwa a ngʼombe, nkhosa kapena mbuzi. Iwo ndi opatulika. Uwaze magazi a nyamazi pa guwa lansembe ndi kutentha mafuta ake ngati nsembe yotentha ndi moto kuti likhale fungo lokoma kwa Yehova. Nyama yake ikhale yanu monga momwe chimakhalira chidale cha nsembe yoweyula ndi ntchafu za miyendo ya kumanja, zonsezi ndi zako. Zonse zimene mwazichotsa ku zopereka zoyera zomwe Aisraeli anapereka kwa Yehova ndazipereka kwa iwe ndi ana ako aamuna ndi aakazi ngati gawo lanu nthawi zonse. Ili ndi pangano losatha la mchere pamaso pa Yehova kwa iwe ndi ana ako.” (Numeri 18:8-19)
Pa gawo la ankhondowo, mutengeko gawo la Yehova, pa zofunkha 500 zilizonse mutengeko chimodzi, pa akapolo, ngʼombe, bulu ndi nkhosa. Utenge zimenezo pa theka la gawo la ankhondowo ndipo upereke kwa wansembe Eliezara kuti zikhale zopereka zanu kwa Yehova. Kuchokera pa theka la gawo la Aisraeli, utengeko cholanda chimodzi pa makumi asanu aliwonse, pa anthu, ngʼombe, abulu, nkhosa, mbuzi kapena zoweta zina. Uzipereke kwa Alevi amene ntchito yawo ndi yosamalira tenti ya Yehova.” (Numeri 31:28-30)
Anthu amene abwera kudzapereka nsembe ya ngʼombe kapena nkhosa, azipereka kwa wansembe gawo lake motere: mwendo wakutsogolo, nyama yamʼmasaya ndi zamʼkati. Muziwapatsa zamasika zoyamba za tirigu wanu, vinyo watsopano ndi mafuta, ndi ubweya woyamba pometa nkhosa zanu, (Deuteronomo 18:3-4)
Musamange ngʼombe pakamwa pamene ikupuntha tirigu. (Deuteronomo 25:4)
“Tilonjezanso kuti tidzabwera ndi zipatso zoyamba kucha za mʼminda yathu ndi zipatso zoyamba kucha za mtengo uliwonse wa zipatso chaka ndi chaka kuti tidzapereke ku Nyumba ya Mulungu wathu.” “Tidzabweranso nawo ku Nyumba ya Mulungu, kwa ansembe amene amatumikira ku Nyumba ya Mulungu ana athu aamuna oyamba kubadwa ndi ana angʼombe oyamba kubadwa monga zalembedwera mu Malamulo. Tidzaperekanso ana oyamba kubadwa a ziweto zathu ndi ana ankhosa oyamba kubadwa.” (Nehemiya 10:35-36)
Choncho mu nthawi ya Zerubabeli ndi Nehemiya, Aisraeli onse anakapereka mphatso tsiku ndi tsiku kwa anthu oyimba nyimbo ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu. Ankayikanso padera chigawo cha zopereka cha Alevi. Nawonso Alevi ankayika padera chigawo cha zopereka cha ansembe, zidzukulu za Aaroni. (Nehemiya 12:47)
Iwo azidzadya nsembe ya chakudya, nsembe yopereka chifukwa cha tchimo ndi nsembe yopepesera machimo. Zinthu zonse zoperekedwa kwa Yehova mu Israeli zidzakhala zawo. Zabwino za zipatso zanu zoyambirira kucha ndiponso mphatso zanu zonse zapadera zidzakhala za ansembe. Inu muziwapatsa chigawo choyamba cha ufa wanu kuti pa nyumba panu pakhale madalitso. (Ezekieli 44:29-30)
Ogwira ntchito a Chipangano Chatsopano
“Musatenge ndalama zagolide kapena zasiliva kapena zakopala mʼzikwama mwanu; musatenge thumba la paulendo, kapena malaya awiri kapena nsapato kapena ndodo; pakuti wantchito ayenera kulandira chakudya chake. (Mateyu 10:9-10)
Zomwe anawalangiza ndi izi: “Musatenge kanthu ka paulendo koma ndodo yokha; osatenga buledi, thumba, kapena ndalama. (Marko 6:8)
Yesu atawayitana khumi ndi awiriwo pamodzi, Iye anawapatsa mphamvu ndi ulamuliro wotulutsa ziwanda zonse ndi kuchiritsa matenda. Ndipo Iye anawatumiza kukalalikira za ufumu wa Mulungu ndi kukachiritsa odwala. Iye anawawuza kuti, “Musatenge kanthu paulendo. Musatenge ndodo, thumba, buledi, ndalama, ndi malaya apadera. (Luka 9:1-3)
Zitatha izi Ambuye anasankha enanso 72 ndi kuwatumiza awiriawiri patsogolo pake ku mzinda uliwonse ndi kumalo kumene Iye anatsala pangʼono kupitako. Musatenge chikwama kapena thumba kapena nsapato; ndipo musalonjere wina aliyense pa njira. “Mukamalowa mʼnyumba, poyamba nenani kuti, ‘Mtendere pa nyumba ino.’ Ngati mʼnyumbamo muli munthu wofuna mtendere, mtendere wanuwo udzakhala pa iyeyo; ngati mulibemo, mtendere wanuwo udzabwerera kwa inu. Khalani mʼnyumba yomweyo, idyani ndi kumwa chilichonse chimene akupatsani, pakuti wantchito ayenera kulandira malipiro ake. Musachoke kumene mwafikirako ndi kupita ku nyumba zina. (Luka 10:1, 4-7)
Koma munthu amene akuphunzira mawu, agawireko mphunzitsi wake zinthu zonse zabwino zimene iye ali nazo. (Agalatiya 6:6)
Akulu ampingo amene amayangʼanira bwino zochitika za mu mpingo, ndi oyenera ulemu wowirikiza, makamaka amene ntchito yawo ndi kulalikira ndi kuphunzitsa. Pakuti Mawu a Mulungu amati, “Musamange ngʼombe pakamwa pamene ikupuntha tirigu,” ndi “Wantchito ngoyenera kulandira malipiro ake.” (1 Timoteyo 5:17-18)
Uyesetse chilichonse ungathe kuthandiza Zena katswiri wa malamulo ndi Apolo, kuti apitirize ulendo wawo, ndipo uwonetsetse asasowe kanthu. (Tito 3:13)
Wokondedwa, ndiwe wokhulupirika pa zimene ukuchitira abale, ngakhale kuti iwowo ndi alendo. Iwo anafotokozera mpingo za chikondi chako. Chonde uwathandize kupitiriza ulendo mʼnjira yokondweretsa Mulungu. Pakuti ananyamuka ulendo wawo chifukwa cha dzina la Ambuye, osalandira thandizo kwa osakhulupirira. Ife tiyenera kumathandiza anthu oterewa, kuti tigwirizane nawo pa ntchito ya choonadi. (3 Yohane 1:5-8)
Yesu ankathandizidwa ndi mphatso pa nthawi ya utumiki wake pa dziko lapansi
Yohana mkazi wa Kuza, woyangʼanira mʼnyumba ya Herode; Suzana; ndi ena ambiri analinso. Akazi awa ankawathandiza ndi chuma chawo. (Luka 8:3)
Ogwira ntchito achikhristu amene sanagwiritse ntchito ufulu wawo wothandizidwa
Kodi kapena ine ndekha ndi Barnaba ndiye tikuyenera kugwira ntchito kuti tipeze zotisowa? Ndani angagwire ntchito ya usilikali namadzipezera yekha zofunika zonse? Kodi ndani amadzala mpesa koma wosadyako zipatso zake? Ndani amaweta nkhosa koma wosamwako mkaka wake? Kodi moti zimene ndikunenazi ndimaganizo a umunthu chabe? Kodi Malamulo sakunena chimodzimodzinso? Popeza analemba mʼMalamulo a Mose kuti, “Musamange ngʼombe pakamwa pamene ikupuntha tirigu.” Kodi pamene Mulungu ananena zimenezi ankalabadira za ngʼombe zokha? Ndithu Iyeyo amanena za ifenso, kodi si choncho? Inde, izi anazilemba chifukwa cha ife, pakuti wolima ndiponso wopuntha, onsewo amagwira ntchito mwachiyembekezo chodzagawana zokololazo. Ngati tidzala mbewu yauzimu pakati panu, kodi ndi chovuta kwambiri kuti tikolole zosowa zathu kuchokera kwa inu? Ngati ena ali ndi ufulu wothandizidwa ndi inu, kodi ife sitikuyenera kukhala nawo ufulu ochulukirapo? Koma ife sitinagwiritse ntchito ufulu umenewu. Mʼmalo mwake timangodzichitira chilichonse posafuna kutsekereza ena kumva Uthenga Wabwino wa Khristu. Kodi simukudziwa kuti wogwira ntchito mʼNyumba ya Mulungu amapeza chakudya chawo mʼNyumbamo, ndipo kuti otumikira pa guwa lansembe amagawana zimene zaperekedwa pa guwa lansembelo. Chomwechonso Ambuye akulamula kuti wolalikira Uthenga Wabwino azilandira thandizo lawo polalikira Uthenga Wabwinowo. Koma ine sindinagwiritse ntchito ufulu woterewu. Sindikulemba izi ndi chiyembekezo choti mundichitire zoterezi. Kuli bwino ndife kusiyana nʼkuti wina alande zomwe ndimazinyadira. (1 Akorinto 9:6-15)
Ngati ndikugwira ntchitoyi mwakufuna kwanga, ndili ndi mphotho; koma ngati si mwakufuna kwanga, ndiye kuti ntchitoyi ndi Ambuye anandipatsa. Tsono mphotho yanga ndi chiyani? Ndi iyi: kuti polalikira Uthenga Wabwino ndiwupereke kwaulere komanso kuti ndisagwiritse ntchito ufulu wanga polalikira uthengawo. (1 Akorinto 9:17-18)
Kodi linali tchimo kwa ine kudzichepetsa nʼcholinga chakuti ndikukwezeni pamene ndinkalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu kwa inu mwaulere? Ndinkalanda mipingo ina pomalandira thandizo kwa iwo kuti ndikutumikireni. Ndipo pamene ndinali pakati panu, nditasowa kanthu, sindinalemetse munthu aliyense, pakuti abale ena amene anachokera ku Makedoniya anandipatsa zonse zimene ndinkazisowa. Ndayesetsa kuti ndisakhale cholemetsa kwa inu mʼnjira ina iliyonse, ndipo ndidzapitiriza kutero. (2 Akorinto 11:7-9)
Ndakonzeka tsopano kudzakuyenderani kachitatu, ndipo sindidzakhala cholemetsa kwa inu chifukwa ndikungofuna inuyo osati zinthu zanu. Pakuti ana sasamalira makolo koma makolo ndiwo asamalira ana. Motero ndidzakondwera kukupatsani zanga zonse zimene ndili nazo ndi kudziperekanso ine mwini chifukwa cha inu. Kodi ine ndikamakukondani kwambiri chotere, inuyo mudzandikonda pangʼono? Ena mwa inu amavomereza kuti sindinali cholemetsa. Komabe ena amaganiza kuti ndine wochenjera, ndipo ndinakuchenjererani. Kodi ndinakudyerani masuku pamutu kudzera mwa wina aliyense amene ndinamutumiza kwa inu? Ndinamupempha Tito kuti abwere kwanuko ndipo ndinamutumiza pamodzi ndi mʼbale wathu. Kodi kapena Tito anakudyerani masuku pamutu? Kodi iye ndi ine sitinachite zinthu mofanana ndi Mzimu mmodzi yemweyo? (2 Akorinto 12:14-18)
Monga mukudziwa kuti sitinagwiritse ntchito mawu oshashalika kapena mtima wofuna phindu, Mulungu ndiye mboni yathu. Abale, pakuti mukumbukira kugwira ntchito kwathu kwambiri ndi kuvutika; ife tinagwira ntchito usana ndi usiku ndi cholinga chakuti tisakhale cholemetsa, kwa aliyense pamene ife tinkalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu kwa inu. (1 Atesalonika 2:5, 9)
...ndipo sitinadye chakudya cha aliyense osalipira. Komatu tinkagwira ntchito mwamphamvu usiku ndi usana kuti tisakhale cholemetsa kwa aliyense. Sitinachite zimenezi chifukwa choti tinalibe mphamvu zolamula kuti mutithandize koma kuti tikhale chitsanzo choti mutsatire. (2 Atesalonika 3:8-9)
Ogwira ntchito achikhristu sayenera kutumikira ndi zolinga zoyipa za ndalama
Ine ndikupempha akulu a mpingo amene ali pakati panu, monga inenso mkulu mnzawo, mboni ya zowawa za Khristu ndiponso amene ndidzalandira nawo ulemerero umene uti udzaonetsedwe. Wetani gulu la Mulungu limene lili mʼmanja mwanu, muziliyangʼanira. Muzichita osati mowumirizidwa, koma mwakufuna kwanu, monga momwe Mulungu akufunira kuti mutero. Musachite chifukwa chadyera la ndalama, koma ndi mtima ofuna kutumikira. (1 Petro 5:1-2)
Ambiri amayesa kupeza ndalama podzionetsa ngati opembedza
Kusiyana ndi ena ambiri, ife sitilalikira Mawu a Mulungu kuti tipeza phindu. Mʼmalo mwake, ife mwa Khristu timayankhula pamaso pa Mulungu moona mtima, monga anthu otumidwa ndi Mulungu. (2 Akorinto 2:17)
Paja pali anthu ambiri osaweruzika, makamaka mʼgulu la anthu a mdulidwe, oyankhula nkhani zopanda pake ndi kusocheretsa anzawo. Ayenera kuletsedwa kuyankhula chifukwa akusokoneza mabanja athunthu pophunzitsa zinthu zomwe sayenera kuwaphunzitsa. Iwo amachita izi kuti apeze ndalama mwachinyengo. (Tito 1:10-11)
Koma panalinso aneneri onama pakati pa Aisraeli, monga padzakhalanso aphunzitsi onyenga pakati panu. Iwo adzalowetsa mwamseri ziphunzitso zonama ndi zowononga, nadzakana Ambuye amene anawawombola, ndipo motero adzadziyitanira okha chiwonongeko mwadzidzidzi. Pofuna kupeza chuma, aphunzitsiwa adzakudyerani chuma chanu pokuwuzani nkhani zopeka. Chiweruzo chawo chinakonzedwa kale, ndipo chikuwadikira. (2 Petro 2:1, 3)
Ophunzira analimbikitsidwa kukonzekera
Kenaka Yesu anawafunsa iwo kuti, “Ine nditakutumizani wopanda chikwama cha ndalama, thumba kapena nsapato, kodi inu munasowa kanthu?” Iwo anayankha kuti, “Palibe chimene tinasowa.” Iye anawawuza kuti, “Koma tsopano ngati muli ndi chikwama cha ndalama, chitengeni, ndiponso thumba. Ndipo ngati mulibe lupanga, gulitsani mkanjo wanu ndi kugula. (Luka 22:35-36)
Malo opatulika/Nyumba ya Mulungu
Kumanga chihema
Zopereka zimene ulandire kwa anthuwo ndi izi: Golide, siliva ndi mkuwa. Nsalu zobiriwira, zapepo, zofiira, nsalu zofewa, ubweya wambuzi; zikopa za nkhosa zazimuna za utoto wofiira ndi zikopa za akatumbu; matabwa amtengo wa mkesha; mafuta anyale a olivi, zonunkhiritsa mafuta odzozera ndi zopangira lubani wonunkhira; miyala yokongola ya mtundu wa onikisi ndi ina yabwino yoyika pa efodi ndi pa chovala cha pachifuwa. “Iwo andipangire malo wopatulika, ndipo Ine ndidzakhala pakati pawo. (Eksodo 25:3-8)
Anapereka kuposa zofunikira
Iwo analandira kuchokera kwa Mose zopereka zonse Aisraeli anabweretsa kuti agwirire ntchito yomanga malo wopatulika. Ndipo anthu anapitirira kupereka zopereka zaufulu mmawa uliwonse. Kotero amisiri onse amene amagwira ntchito yonse ya malo wopatulika anasiya ntchitoyo ndipo anati kwa Mose, “Anthu akubweretsa kuposa zimene zikufunika kugwirira ntchito imene Yehova analamulira kuti ichitike.” Choncho Mose analamulira ndipo analengeza mu msasa onse, “Mwamuna kapena mayi aliyense asaperekenso chopereka chilichonse cha ku malo wopatulika.” Choncho anthu analetsedwa kubweretsa zambiri, chifukwa zimene anali nazo zinali zoposera zimene zimafunika kugwirira ntchito yonse. (Eksodo 36:3-7)
Kumanga Nyumba ya Mulungu
Ine ndapereka ku ntchito ya Nyumba ya Mulungu zinthu zanga zonse, golide wopangira zinthu zagolide, siliva wopangira zinthu zasiliva ndi zitsulo zopangira zinthu zazitsulo, mkuwa wopangira zinthu zamkuwa ndi matabwa opangira zinthu zamatabwa komanso miyala yokongola ya onikisi yokongoletsera, miyala ya maonekedwe osiyanasiyana, ndi miyala yonse yosalala ndi miyala ya marabulo, zonsezi ndapereka zochuluka. Kupatulapo izi, ine modzipereka ku Nyumba ya Mulungu wanga, tsopano ndikupereka chuma changachanga cha golide ndi siliva ku Nyumba ya Mulungu wanga, kuwonjezera pa zimene ndapereka ku ntchito ya Nyumba ya Mulungu woyerayu: Matani 100 agolide (golide wa ku Ofiri) ndi matani 240 a siliva woyengeka bwino wokutira makoma a nyumba, zinthu zagolide ndi zinthu zasiliva, ndiponso zinthu zonse zimene anthu aluso adzagwiritse ntchito. Tsopano ndani amene akufuna kudzipatulira yekha kwa Yehova lero?” Tsono atsogoleri a mabanja, akuluakulu a mafuko a Israeli, olamulira asilikali 1,000, ndi olamulira asilikali 100, ndiponso akuluakulu onse amene amayangʼanira ntchito ya mfumu anapereka mwaufulu. Iwo anapereka ku ntchito ya Nyumba ya Mulungu matani 170 a golide, matani 340 a siliva, matani 620 a mkuwa ndi matani 3,400 a chitsulo. Aliyense amene anali ndi miyala yokongola anayipereka ku nyumba yosungiramo chuma cha Nyumba ya Yehova ndipo amene ankayangʼanira anali Yehieli Mgeresoni. (1 Mbiri 29:2-8)
Nyumba ya Mulungu inawononga ndalama zambiri
Molamulidwa ndi mfumu, anakumba ndi kusema miyala ikuluikulu kwambiri yoti akamangire maziko a Nyumba ya Mulungu. (1 Mafumu 5:17)
Kukonza Nyumba ya Mulungu
Yowasi anati kwa ansembe, “Tolerani ndalama zonse zimene zimaperekedwa monga chopereka chopatulika ku Nyumba ya Yehova, ndalama zonse zamsonkho wa munthu aliyense, ndalama zomwe munthu amapereka akalonjeza ndiponso ndalama zimene munthu amapereka mwaufulu ku Nyumba ya Yehova. Wansembe aliyense alandire ndalamazo kuchokera kwa abwenzi ake, ndipo zigwiritsidwe ntchito yokonzera chilichonse chimene chipezeke kuti ndi chowonongeka mʼnyumbayo.” Koma pofika chaka cha 23 cha ufumu wa Yowasi, ansembewo anali asanakonze nyumbayo. Choncho Mfumu Yowasi inayitanitsa wansembe Yehoyada ndi ansembe ena ndipo inafunsa kuti, “Chifukwa chiyani simukukonza malo owonongeka a mʼnyumbayi? Musasungenso ndalama zina zochokera kwa abwenzi anu, koma muzipereke kuti akonzere nyumbayi.” Ansembe anavomera kuti salandiranso ndalama kuchokera kwa anthu ndipo kuti sindiwo amene ati akonzenso nyumbayo. Koma wansembe Yehoyada anatenga bokosi ndipo anabowola chivundikiro chake. Anayika bokosilo pambali pa guwa lansembe, kudzanja lamanja la aliyense amene akulowa mʼNyumba ya Yehovayo. Ansembe amene ankalondera pa khomopo ankaponya mʼbokosi ndalama zonse zimene ankabwera nazo ku nyumba ya Yehova. Nthawi zonse akaona kuti mʼbokosimo muli ndalama zambiri, mlembi wa mfumu ndi mkulu wa ansembe ankabwera ndipo ankawerenga ndalama zomwe anthu ankabwera nazo ku Nyumba ya Yehova ndi kuziyika mʼmatumba. Ankati akadziwa kuti ndalamazo zilipo zingati, ankazipereka kwa anthu amene ankayangʼanira ntchito yokonza nyumbayo. Ndalamazo ankalipira anthu amene ankagwira ntchito yokonza Nyumba ya Yehova, amisiri a matabwa ndi amisiri omanga nyumba, (2 Mafumu 12:4-11)
“Pita kwa mkulu wa ansembe Hilikiya ndipo ukamuwuze kuti awerenge ndalama zimene anthu abwera nazo ku Nyumba ya Yehova, zimene alonda a pa khomo anasonkhanitsa kwa anthu. Ndalamazo azipereke kwa anthu amene asankhidwa kuti ayangʼanire ntchito ya Nyumba ya Yehova. Ndipo anthu amenewa azilipira antchito amene akukonzanso Nyumba ya Yehova, amisiri a matabwa, amisiri omanga ndi amisiri a miyala. Iwo akagulenso matabwa ndi miyala yosemedwa kuti akonzere Nyumba ya Yehova. (2 Mafumu 22:4-6)
Patapita nthawi Yowasi anatsimikiza zokonzanso Nyumba ya Yehova. Iye anayitanitsa pamodzi ansembe ndi Alevi ndipo anawawuza kuti, “Pitani ku mizinda ya Yuda ndi kukasonkhetsa ndalama za pa chaka kwa Aisraeli onse zokonzera Nyumba ya Mulungu wanu. Chitani zimenezi tsopano.” Koma Alevi sanachite zimenezi mwachangu. Choncho mfumu inayitanitsa Yehoyada, mkulu wa ansembe ndipo inati kwa iye, “Kodi nʼchifukwa chiyani simunawuze Alevi kuti asonkhetse ndalama ku Yuda ndi Yerusalemu, msonkho umene anakhazikitsa Mose mtumiki wa Yehova ndiponso gulu lonse la Aisraeli mu tenti yaumboni?” Ana a mkazi woyipa, Ataliya, anathyola chitseko cha Nyumba ya Mulungu ndipo anagwiritsa ntchito zinthu zopatulika popembedza Baala. Mfumu italamulira, bokosi linapangidwa ndipo linayikidwa panja pa chipata cha Nyumba ya Yehova. Ndipo analengeza kwa anthu a mu Yuda ndi mu Yerusalemu kuti abweretse kwa Yehova msonkho umene Mose mtumiki wa Mulungu analamulira Aisraeli mʼchipululu. Akuluakulu onse ndi anthu onse anabweretsa zopereka zawo mokondwera ndipo anaziponya mʼbokosi mpaka linadzaza. Nthawi ina iliyonse imene Alevi abweretsa bokosilo kwa akuluakulu a mfumu ndipo akaona kuti muli ndalama zambiri, mlembi waufumu ndi nduna yayikulu ya mkulu wa ansembe amabwera ndi kuchotsa ndalama mʼbokosi muja ndipo amalitenga kukaliyika pamalo pake. Iwo amachita izi nthawi ndi nthawi ndipo anapeza ndalama zambiri. Mfumu pamodzi ndi Yehoyada anapereka ndalamazo kwa anthu oyangʼanira ntchito ku Nyumba ya Yehova. Analemba ntchito amisiri a miyala ndi a matabwa kuti akonzenso Nyumba ya Yehova. Analembanso ntchito amisiri a zitsulo ndi mkuwa kuti akonze Nyumba ya Mulungu. Anthu amene ankagwira ntchito anali odziwa bwino, ndipo ntchitoyo inagwiridwa bwino ndi manja awo. Iwo anamanganso Nyumba ya Mulungu motsatira mapangidwe ake oyamba ndipo anayilimbitsa. (2 Mbiri 24:4-13)
Mʼchaka cha 18 cha ulamuliro wa Yosiya, atayeretsa dziko ndi Yerusalemu, Yosiya anatuma Safani mwana wa Azariya ndi Maaseya, wolamulira mzinda pamodzi ndi Yowa mwana wa Yowahazi mlembi wolemba mbiri, kuti akonze Nyumba ya Yehova Mulungu wake. Iwo anapita kwa Hilikiya, mkulu wa ansembe ndipo anamupatsa ndalama zimene zinaperekedwa mʼNyumba ya Mulungu, zimene Alevi amene anali alonda apakhomo analandira kuchokera kwa anthu a ku Manase, Efereimu ndi onse otsala a ku Israeli ndiponso anthu onse ochokera ku Yuda ndi Benjamini ndi okhala mu Yerusalemu. Ndipo anazipereka mʼmanja mwa anthu amene anasankhidwa kuti ayangʼanire ntchito ya Nyumba ya Yehova. Anthu amenewa ankalipira antchito amene ankakonzanso Nyumba ya Mulungu. Iwo anaperekanso ndalama kwa amisiri a matabwa ndi amisiri omanga nyumba kuti agule miyala yosema ndi matabwa a phaso la nyumba ndi nsichi zomangira zomwe mfumu ya Yuda inalekerera kuti zigwe ndi kuwonongeka. (2 Mbiri 34:8-11)
Kumanganso Nyumba ya Mulungu
Atafika ku Nyumba ya Yehova mu Yerusalemu, ena mwa atsogoleri a mabanja anapereka zopereka zaufulu zothandizira kumanganso Nyumba ya Mulungu pamalo pake pakale. Anapereka kwa msungichuma wa ntchitoyo molingana ndi mmene aliyense chuma chake chinalili: golide wa makilogalamu 500, siliva makilogalamu 2,800 ndi zovala za ansembe zokwanira 100. (Ezara 2:68-69)
Mumange mizere itatu ya miyala yayikulu ndi mzere umodzi wa matabwa, ndalama zake zolipirira ntchitoyo zichokere mʼthumba la ufumu. (Ezara 6:4)
Kuwonjezera pamenepo, ndikukhazikitsa lamulo lonena za mmene mudzachitire ndi akuluakulu a Ayuda powathandiza kumanganso Nyumba ya Mulunguyo: Anthuwa muwalipire msanga kuchokera mʼthumba la ufumu, kuchotsa pa msonkho wa dera la Patsidya pa Yufurate. (Ezara 6:8)
Kusamalira Nyumba ya Mulungu
“Ife tikulonjeza kuti sitidzapereka ana athu aakazi kuti akwatiwe ndi amuna a mayiko ena kapena kutenga ana awo aakazi kuti akwatiwe ndi ana athu aamuna. Choncho Israeli, kuphatikiza zidzukulu za Alevi, azipititsa zopereka za tirigu, vinyo ndi mafuta ku zipinda zosungiramo katundu wopatulika, komanso kokhala ansembe amene akutumikira pamodzi ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu ndi anthu oyimba nyimbo. “Kwambiri ife sitidzaleka kusamala Nyumba ya Mulungu.” (Nehemiya 10:30, 39)
Magulu ena
Amene amapempha mphatso
Wina akakupempha kanthu umupatse, ndipo wofuna kubwereka usamukanize. (Mateyu 5:42)
Mupatseni aliyense amene akupemphani kanthu ndipo ngati wina atenga chinthu chanu, musamulamule kuti akubwezereni. (Luka 6:30)
Anthu onse, makamaka okhulupirira
Nʼchifukwa chake ngati tapeza mpata, tiyenera kuchitira zabwino anthu onse, makamaka amene ndi a banja la okhulupirira. (Agalatiya 6:10)
Mukondane kwathunthu monga abale. Lemekezanani wina ndi mnzake kuposa inu eni. (Aroma 12:10)
Gawanani ndi anthu a Mulungu amene ali ndi chosowa. Cherezani alendo. (Aroma 12:13)
Adani
Ngati mdani wako ali ndi njala, mupatse chakudya kuti adye; ngati ali ndi ludzu mupatse madzi kuti amwe. Pochita izi, udzamusenzetsa makala a moto pa mutu pake, ndipo Yehova adzakupatsa mphotho. (Miyambo 25:21-22)
Koma, “Ngati mdani wako ali ndi njala, mupatse chakudya. Ngati ali ndi ludzu, mupatse kanthu kakumwa. Pochita ichi, udzamuwunjikira makala amoto pamutu pake.” (Aroma 12:20)
Usapereke kwa wopha munthu
Munthu amene wapalamula mlandu wopha munthu adzakhala wothawathawa mpaka imfa yake; wina aliyense asamuthandize. (Miyambo 28:17)
Kupereka kwa osauka
Malamulo a Mulungu ndi maganizo ake pa kupereka kwa osauka
Anthu osauka sadzatha mʼdziko lanu. Chomwecho ndikukulamulani kuti mukhale ofewa manja kwa abale anu ndi kwa osauka, osowa mʼdziko mwanu. (Deuteronomo 15:11)
Amene amapondereza mʼmphawi amanyoza mlengi wake, koma wochitira chifundo munthu wosowa amalemekeza Mulungu. (Miyambo 14:31)
Amene amakomera mtima osauka amachita ngati wakongoletsa Yehova, ndipo Yehovayo ndiye adzamubwezere. (Miyambo 19:17)
“Kodi si uku kusala kudya kumene Ine ndimakufuna: Kumasula maunyolo ozunzizira anthu ndi kumasula zingwe za goli, kupereka ufulu kwa oponderezedwa ndi kuphwanya goli lililonse? Anthu anjala kodi mwawagawira chakudya chanu? Osowa ndi ongoyendayenda, kodi mwawapatsa malo ogona? Munthu wausiwa kodi mwamupatsa chovala? Mukatero chipulumutso chanu chidzabwera ngati mʼbandakucha, ndipo mabala anu adzachira msangamsanga; chilungamo chanu chidzakutsogolerani ndipo ulemerero wa Yehova udzakhala chokutchinjirizani kumbuyo kwanu. Mukamadzapemphera Yehova adzakuyankhani; mukadzapempha thandizo, Iye adzati: Ine ndili pano. “Ngati muleka kuzunza anzanu, ngati musiya kuloza chala ndiponso kunena zoyipa za anzanu. Ndipo ngati mudyetsa anthu anjala, ndi kuthandiza anthu oponderezedwa, pamenepo kuwala kwanu kudzaonekera mu mdima, ndipo usiku wanu udzakhala ngati usana. (Yesaya 58:6-10)
“ ‘Tsono tchimo la mʼbale wako Sodomu linali ili: Iye ndi ana ake aakazi ankanyadira kuchuluka kwa chakudya ndi chuma chawo. Koma sanalabadireko kuthandiza osauka ndi aumphawi. (Ezekieli 16:49)
Zokonzekera za Chipangano Chakale kwa osauka
Malamulo a kukolola ndi kukunkha
“Muzidzala mbewu zanu mʼmunda ndi kumakolola mbewuzo kwa zaka zisanu ndi chimodzi. Koma chaka chachisanu ndi chiwiri muzisiya osalima mindayo kuti anthu osauka pakati panu azipezamo chakudya, ndipo nyama zakuthengo zizidya zotsalazo. Muzichita chimodzimodzi ndi minda ya mpesa ndi mitengo ya olivi. (Eksodo 23:10-11)
“ ‘Pamene mukolola zinthu mʼmunda mwanu musakolole mpaka mʼmphepete mwa munda, ndipo musatole khunkha lake. Musakolole mphesa zonse mʼmunda wanu wa mpesa kapena kutola mphesa zakugwa mʼmundamo. Zimenezi muzisiyire anthu osauka ndi alendo. Ine ndine Yehova Mulungu wako. (Levitiko 19:9-10)
“ ‘Pamene mukukolola zinthu mʼmunda mwanu, musakolole munda wanu mpaka mʼmalire mwenimweni, ndipo musatole khunkha lake. Zimenezo musiyire anthu osauka ndi alendo. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ ” (Levitiko 23:22)
Mukamakolola mʼmunda mwanu ndipo zokolola zina zikasiyidwa, musamabwerere kukazitola. Muzilekere alendo, ana ndi akazi amasiye, kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni pa zochita zanu zonse. Mukathyola zipatso mu mtengo wa olivi, musamabwererenso kachiwiri ku mtengo womwewo. Zotsalazo zilekereni alendo, ana ndi akazi amasiye. Mukakolola mphesa mʼmunda mwanu musamabwereremonso kachiwiri. Zotsalazo muzilekere alendo, ana ndi akazi amasiye. (Deuteronomo 24:19-21)
Udindo wopanda malire wopereka zosowa
Ngati pali mʼbale wanu wina wosauka mu mzinda wanu wina uliwonse mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, musawumitse mitima yanu kapena kuchita kaligwiritsa kwa mʼbale wanu wosaukayo. Koma mukhale ofewa manja ndipo mumukongoze mʼbale wanu momasuka pa chilichonse chimene akufuna. Musayesere ndi pangʼono pomwe kusunga maganizo oyipa awa mu mtima mwanu: “Chaka chachisanu ndi chiwiri, chaka chokhululukirana ngongole, chayandikira,” kuti musaonetse mtima woyipa kwa mʼbale wanu wosauka nʼkusamupatsa chilichonse. Iye angadzakunenereni inu mlandu kwa Ambuye, ndipo mudzapezeka wochimwa. Mumupatse iye mowolowamanja ndipo muchite zimenezi mosasungira kanthu kumtima. Tsono chifukwa cha zimenezi, Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani pa ntchito zanu zonse ndi pa chilichonse chimene mukhudza. (Deuteronomo 15:7-10)
Chikondwerero cha Purimu
...ngati masiku amene Ayuda anapulumutsidwa kwa adani awo, ndiponso ngati mwezi umene chisoni chawo chinasandulika chimwemwe ndi kulira kwawo kunasandulika chikondwerero. Anawalembera kuti azisunga masikuwa ngati masiku a madyerero ndi chikondwerero, masiku opatsana mphatso zachakudya kwa wina ndi mnzake komanso opereka mphatso kwa osauka. (Estere 9:22)
Chaka cha Jubili
Mupatule chaka cha makumi asanu, ndipo mulengeze kuti pakhale ufulu mʼdziko lonse kwa onse amene ali mʼmenemo. Kwa inu chakachi chidzakhala choyimba lipenga la chikondwerero. Aliyense wa inu adzayenera kubwerera pa munda wake, ndipo aliyense wa inu adzabwerera ku fuko lake. (Levitiko 25:10)
Zitsanzo za kupereka kwa osauka
...chifukwa ndinkapulumutsa mʼmphawi wofuna chithandizo, ndiponso mwana wamasiye amene analibe aliyense womuthandiza. Munthu amene anali pafupi kufa ankandidalitsa; ndinkasangalatsanso mkazi wamasiye. Chilungamo chinali ngati chovala changa; chiweruzo cholungama ndiye chinali mkanjo ndi nduwira yanga. Ndinali ngati maso kwa anthu osapenya; ndinali ngati mapazi kwa anthu olumala. Ndinali ngati abambo kwa anthu aumphawi; ndinkayimira mlendo pa mlandu wake. (Yobu 29:12-16)
“Ngati ndinawamana aumphawi zinthu zimene ankazikhumba, kapena kuwagwiritsa fuwa lamoto akazi amasiye amene amafuna thandizo kwa ine, ngati chakudya changa ndinadya ndekha, wosagawirako mwana wamasiye, chonsechotu kuyambira unyamata wanga ndinamulera monga abambo ake, ndipo moyo wanga wonse ndakhala ndikusamalira akazi amasiye, ngati ndinaona wina aliyense akuzunzika ndi usiwa, kapena munthu wosauka alibe chofunda, ndipo ngati iyeyo sananditamandepo chifukwa chomufunditsa ndi nsalu ya ubweya wankhosa, ngati ndinaopsezapo mwana wamasiye, poganiza kuti ndinali ndi mphamvu mʼbwalo la milandu, pamenepo phewa langa lipokonyeke, mkono wanga ukonyoke polumikizira pake. Popeza ine ndinaopa kwambiri chiwonongeko chochokera kwa Mulungu, ndinachitanso mantha ndi ulemerero wake, sindikanatha kuchita zinthu zimenezi. (Yobu 31:16-23)
Mtsogoleri wolungama
Iye adzateteza ozunzika pakati pa anthu ndi kupulumutsa ana a anthu osowa; adzaphwanya ozunza anzawo. (Masalimo 72:4)
Pakuti iye adzawombola wosowa amene akulira, wozunzika amene alibe wina womuthandiza. Iye adzachitira chifundo anthu ofowoka ndi anthu osowa ndi kupulumutsa osowa ku imfa. (Masalimo 72:12-13)
Mkazi wangwiro
Kodi mkazi wangwiro angathe kumupeza ndani? Ndi wokwera mtengo kuposa miyala yamtengowapatali. Iye amachitira chifundo anthu osauka ndipo amapereka chithandizo kwa anthu osowa. (Miyambo 31:10, 20)
Chipangano Chatsopano
Yohane Mʼbatizi
Gulu la anthuwo linafunsa kuti, “Nanga tsono tichite chiyani?” Yohane anayankha kuti, “Munthu amene ali ndi malaya awiri apatseko amene alibe, ndi amene ali ndi chakudya achitenso chimodzimodzi.” (Luka 3:10-11)
Yesu Khristu amadziyerekeza ndi osauka
“Pamene Mwana wa Munthu adzabwera mu ulemerero wake, pamodzi ndi angelo ake onse, adzakhala pa mpando waufumu mu ulemerero wakumwamba. Mitundu yonse ya anthu idzasonkhanitsidwa pamaso pake, ndipo adzawalekanitsa iwo wina ndi mnzake monga mʼbusa amalekanitsa nkhosa ndi mbuzi. Adzayika nkhosa ku dzanja lake lamanja ndi mbuzi ku lamanzere. “Pamenepo mfumu idzati kwa a ku dzanja lamanja, ‘Bwerani inu odalitsika ndi Atate anga; landirani ufumu umene unakonzedwa chifukwa cha inu kuyambira pachiyambi cha dziko. Pakuti ndinali ndi njala ndipo munandipatsa chakudya, ndinali ndi ludzu ndipo munandipatsa madzi akumwa, ndinali mlendo ndipo munandilandira, ndinali wausiwa ndipo munandiveka, ndinali wodwala ndipo munandisamalira, ndinali ku ndende ndipo inu munandiyendera.’ “Ndipo olungamawo adzamuyankha kuti, ‘Ambuye ndi liti tinakuonani muli ndi njala ndipo tinakudyetsani, kapena ludzu ndipo tinakupatsani madzi akumwa? Ndi liti tinakuonani muli mlendo ndipo tinakulandirani, kapena wa usiwa ndipo tinakuvekani? Ndi liti tinakuonani mutadwala kapena ku ndende ndipo tinakuyenderani?’ “Mfumu idzayankha kuti, ‘Zoonadi, ndikuwuzani kuti chilichonse chimene munachitira mmodzi wa abale anga onyozekawa munandichitira Ine.’ “Pamenepo adzanena kwa akumanzere kwake kuti, ‘Chokani kwa Ine, inu otembereredwa, pitani ku moto wosatha wokonzedwera mdierekezi ndi angelo ake. Pakuti ndinali ndi njala ndipo simunandipatse chakudya, ndinali ndi ludzu ndipo simunandipatse madzi akumwa, ndinali mlendo koma inu simunandilandire, ndinali wa usiwa koma simunandiveke, ndinali wodwala komanso ku ndende simunandisamalire.’ “Iwo adzayankha kuti, ‘Ambuye ndi liti tinakuonani muli ndi njala kapena ludzu kapena mlendo kapena wausiwa kapena wodwala kapena mʼndende, ndipo kuti sitinakuthandizeni?’ “Iye adzayankha kuti, ‘Zoonadi, ndikuwuzani kuti chilichonse chimene simunachitire mmodzi wa abale anga onyozekawa simunandichitire Ine.’ (Mateyu 25:31-45)
Yesu amaonetsa chitsanzo cha kupereka kwa osauka
Nthawi yomweyo Yudasi atangodya bulediyo, Satana analowa mwa Iye. Yesu anamuwuza Iye kuti, “Chomwe ukufuna kuchita, chita msanga.” Koma panalibe ndi mmodzi yemwe pa chakudyapo amene anamvetsa chifukwa chimene Yesu ananenera izi kwa iye. Popeza Yudasi amasunga ndalama, ena amaganiza kuti Yesu amamuwuza iye kuti akagule zomwe zimafunika pa phwando, kapena kukapereka kanthu kena kake kwa osauka. (Yohane 13:27-29)
Yemwe kale anali wonyenga amapereka kwa osauka
Iye amene wakhala akuba asabenso, koma agwire ntchito ndi kuchita kenakake kaphindu ndi manja ake, kuti akhale ndi kenakake kogawana ndi amene akusowa. (Aefeso 4:28)
Zitsanzo zina
Okhulupirira onse anali pamodzi ndipo aliyense ankapereka zinthu zake kuti zikhale za onse. Ankagulitsa minda yawo ndi katundu wawo, ndi kugawira kwa aliyense molingana ndi zosowa zake. (Machitidwe a Atumwi 2:44-45)
Mmodzi wa iwo dzina lake Agabu, anayimirira ndipo Mzimu anamutsogolera kunenera zamʼtsogolo kuti padzakhala njala yayikulu pa dziko lonse lapansi. (Izi zinachitikadi nthawi ya ulamuliro wa Klaudiyo). Ophunzirawo, aliyense monga mwakupata kwake, anatsimikiza kuthandiza abale okhala ku Yudeya. Izi anazichitadi ndipo anatuma Barnaba ndi Saulo kukapereka mphatsozo kwa akulu a mpingo. (Machitidwe a Atumwi 11:28-30)
Pa zonse zimene ndinachita, ndinakuonetsani kuti pogwira ntchito molimbika motere tiyenera kuthandiza ofowoka, pokumbukira mawu a Ambuye Yesu akuti, ‘Kupereka kumadalitsa kuposa kulandira.’ ” (Machitidwe a Atumwi 20:35)
Pakuti kunakomera a ku Makedoniya ndi a ku Akaya kupereka thandizo kwa osauka pakati pa oyera mtima mu Yerusalemu. Iwo chinawakomera kuchita ichi, ndipo ndithu anali ndi ngongole kwa iwo. Pakuti ngati a mitundu ina anagawana ndi Ayuda madalitso auzimu, iwo ali ndi ngongole kwa Ayuda kuti agawane nawo madalitso awo a ku thupi. (Aroma 15:26-27)
Chimene iwo anapempha ndi chakuti ife tipitirize kukumbukira osauka, chinthu chimene ine ndinali okonzeka kuchichita. (Agalatiya 2:10)
Madalitso ndi matemberero
Madalitso a kupereka kwa osauka
Dalitso la kudziwa Ambuye
Iye ankateteza anthu osauka ndi osowa, ndipo zonse zinkamuyendera bwino. Kodi zimenezi sindiye tanthauzo la kudziwa Ine?” akutero Yehova. (Yeremiya 22:16)
Dalitso la moyo
Iye sapondereza munthu wina aliyense, koma amabwezera wangongole nʼchigwiriro chake. Iye salanda zinthu za osauka, koma amapereka chakudya kwa anthu anjala, ndipo amapereka zovala kwa anthu ausiwa. (Ezekieli 18:7)
Iye amatsatira malangizo anga, ndipo amasunga malamulo anga mokhulupirika. Munthu ameneyo ndi wolungama; iye adzakhala ndithu ndi moyo, akutero Ambuye Yehova. (Ezekieli 18:9)
Sapondereza munthu wina aliyense. Satenga chikole akabwereketsa chinthu. Salanda zinthu za osauka. Salanda zinthu za munthu. Amapereka chakudya kwa anthu anjala. Amapereka zovala kwa anthu aumphawi. Amadziletsa kuchita zoyipa. Sakongoletsa kuti apezepo phindu. Salandira chiwongoladzanja. Amasunga malangizo anga ndi kumvera malamulo anga. Munthu wotereyo sadzafa chifukwa cha machimo a abambo ake. Adzakhala ndi moyo ndithu. (Ezekieli 18:16-17)
Dalitso pa banja
Ana ake adzakhala amphamvu mʼdziko; mʼbado wa olungama mtima udzadalitsidwa. Wopereka mphatso zake mowolowamanja kwa osauka, chilungamo chake chimanka mpaka muyaya; nyanga yake idzakwezedwa mwaulemu. (Masalimo 112:2, 9)
Dalitso la zosowa zopezeka
Amene amapereka kwa osauka sadzasowa kanthu, koma amene amatsinzina maso ake adzatembereredwa kwambiri. (Miyambo 28:27)
Dalitso la thanzi
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Wodala ndi munthu amene amaganizira anthu osauka; Yehova amamuwombola pa nthawi yamsautso. Yehova adzamuteteza ndi kusunga moyo wake; Yehova adzamudalitsa iye mʼdziko ndipo sadzamupereka ku zofuna za adani ake. Yehova adzamuthandiza pamene akudwala ndipo adzamuchiritsa pa bedi lake la matenda. (Masalimo 41:1-3)
Dalitso la mapemphero oyankhidwa ndi chitsogozo
“Kodi si uku kusala kudya kumene Ine ndimakufuna: Kumasula maunyolo ozunzizira anthu ndi kumasula zingwe za goli, kupereka ufulu kwa oponderezedwa ndi kuphwanya goli lililonse? Anthu anjala kodi mwawagawira chakudya chanu? Osowa ndi ongoyendayenda, kodi mwawapatsa malo ogona? Munthu wausiwa kodi mwamupatsa chovala? Mukatero chipulumutso chanu chidzabwera ngati mʼbandakucha, ndipo mabala anu adzachira msangamsanga; chilungamo chanu chidzakutsogolerani ndipo ulemerero wa Yehova udzakhala chokutchinjirizani kumbuyo kwanu. Mukamadzapemphera Yehova adzakuyankhani; mukadzapempha thandizo, Iye adzati: Ine ndili pano. “Ngati muleka kuzunza anzanu, ngati musiya kuloza chala ndiponso kunena zoyipa za anzanu. Ndipo ngati mudyetsa anthu anjala, ndi kuthandiza anthu oponderezedwa, pamenepo kuwala kwanu kudzaonekera mu mdima, ndipo usiku wanu udzakhala ngati usana. Yehova adzakutsogolerani nthawi zonse; adzakwaniritsa zosowa zanu mʼdziko longʼalukangʼaluka dzuwa ndipo adzalimbitsa matupi anu. Mudzakhala ngati dimba la madzi ambiri, ngati kasupe amene madzi ake saphwa. (Yesaya 58:6-11)
Dalitso la kupulumutsidwa ndi chitetezo
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Wodala ndi munthu amene amaganizira anthu osauka; Yehova amamuwombola pa nthawi yamsautso. Yehova adzamuteteza ndi kusunga moyo wake; Yehova adzamudalitsa iye mʼdziko ndipo sadzamupereka ku zofuna za adani ake. (Masalimo 41:1-2)
Dalitso la ulemu
Wopereka mphatso zake mowolowamanja kwa osauka, chilungamo chake chimanka mpaka muyaya; nyanga yake idzakwezedwa mwaulemu. (Masalimo 112:9)
Dalitso pa ntchito ndi chuma
Mumupatse iye mowolowamanja ndipo muchite zimenezi mosasungira kanthu kumtima. Tsono chifukwa cha zimenezi, Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani pa ntchito zanu zonse ndi pa chilichonse chimene mukhudza. (Deuteronomo 15:10)
Mukamakolola mʼmunda mwanu ndipo zokolola zina zikasiyidwa, musamabwerere kukazitola. Muzilekere alendo, ana ndi akazi amasiye, kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni pa zochita zanu zonse. (Deuteronomo 24:19)
Iye adzateteza ozunzika pakati pa anthu ndi kupulumutsa ana a anthu osowa; adzaphwanya ozunza anzawo. (Masalimo 72:4)
Pakuti iye adzawombola wosowa amene akulira, wozunzika amene alibe wina womuthandiza. Iye adzachitira chifundo anthu ofowoka ndi anthu osowa ndi kupulumutsa osowa ku imfa. Iye adzalanditsa iwo ku mazunzo ndi chiwawa pakuti magazi awo ndi amtengo wapatali pamaso pake. Iye akhale ndi moyo wautali; golide ochokera ku Seba apatsidwe kwa iye. Anthu amupempherere nthawi zonse ndi kumudalitsa tsiku lonse. (Masalimo 72:12-15)
Kulemera ndi chuma zili mʼnyumba yake, ndipo chilungamo chake ndi chosatha. (Masalimo 112:3)
Wopereka mphatso zake mowolowamanja kwa osauka, chilungamo chake chimanka mpaka muyaya; nyanga yake idzakwezedwa mwaulemu. (Masalimo 112:9)
Amene amakomera mtima osauka amachita ngati wakongoletsa Yehova, ndipo Yehovayo ndiye adzamubwezere. (Miyambo 19:17)
Amene amachulukitsa chuma chake polandira chiwongoladzanja chochuluka amakundikira chumacho anthu ena, amene adzachitira chifundo anthu osauka. (Miyambo 28:8)
Nʼchifukwa chake mfumu, chikukomereni kulandira malangizo anga: Lekani machimo ndipo muzichita zabwino, lekani mphulupulu zanu ndipo muzikomera mtima anthu opsinjika. Nʼkutheka kuti mtendere wanu udzapitirira.” (Danieli 4:27)
Dalitso la kubereka zipatso za uzimu
Uyesetse chilichonse ungathe kuthandiza Zena katswiri wa malamulo ndi Apolo, kuti apitirize ulendo wawo, ndipo uwonetsetse asasowe kanthu. Anthu athu aphunzire kudzipereka pogwira ntchito zabwino, nʼcholinga chakuti athandize zinthu zimene zikufunika msangamsanga. Ndipo asakhale moyo osapindulitsa. (Tito 3:13-14)
Madalitso onse
Amene ali ndi diso lachifundo adzadalitsika, pakuti iye amagawana chakudya chake ndi anthu osauka. (Miyambo 22:9)
Dalitso la chimwemwe
Wonyoza mnansi wake ndi wochimwa koma ndi wodala amene amachitira chifundo anthu osowa. (Miyambo 14:21)
Matemberero kwa amene sapereka kwa osauka
Temberero la pemphero losayankhidwa
Amene atsekera mʼkhutu mwake wosauka akamalira, nayenso adzalira koma palibe adzamuyankhe. (Miyambo 21:13)
Temberero la umphawi
Amene amapondereza anthu osauka kuti awonjezere chuma chake, ndiponso amene amapereka mphatso kwa anthu olemera onsewa adzasauka. (Miyambo 22:16)
Temberero lonse
Amene amapereka kwa osauka sadzasowa kanthu, koma amene amatsinzina maso ake adzatembereredwa kwambiri. (Miyambo 28:27)
Nkhani zina za kupereka kwa osauka
Mtima wachifundo
Kodi ine sindinalire nawo iwo amene anali pamavuto? Kodi mtima wanga sunamvere chisoni anthu osauka? (Yobu 30:25)
Fufuza zosowa za osauka
Ndinali ngati abambo kwa anthu aumphawi; ndinkayimira mlendo pa mlandu wake. (Yobu 29:16)
Munthu wopembedza ananenezedwa kuti sapereka kwa osauka
Kodi osati nʼchifukwa chakuti kuyipa kwako nʼkwakukulu? Kodi machimo ako si opanda malire? Sunawapatse madzi anthu otopa, ndipo unawamana chakudya anthu anjala, Ndipo akazi amasiye unawachotsa wopanda kanthu, ndipo unapondereza ana amasiye. (Yobu 22:5, 7, 9)
Chitsanzo cha kupereka ulemerero kwa Mulungu mʼmalo mopereka kwa osauka
Yesu ali ku Betaniya mʼnyumba Simoni Wakhate, mayi wina anabwera kwa Iye ndi botolo la mafuta onunkhira a mtengowapatali, amene anathira pa mutu pake Iye akudya pa tebulo. Ophunzira ataona izi anayipidwa nafunsa kuti, “Chifukwa chiyani akuwononga chotere? Mafuta amenewa akanatha kugulitsidwa pa mtengo waukulu, ndipo ndalama zake zikanaperekedwa kwa osauka.” Yesu podziwa izi anawawuza kuti, “Chifukwa chiyani mukumuvutitsa mayiyu? Wandichitira Ine chinthu chabwino. Osauka mudzakhala nawo nthawi zonse, koma simudzakhala ndi Ine nthawi zonse. Pamene wathira mafuta onunkhirawa pa thupi langa, wachita izi kukonzekera kuyikidwa kwanga mʼmanda. Zoonadi, ndikuwuzani kuti kulikonse kumene Uthenga Wabwinowu udzalalikidwa ku dziko lonse lapansi, zimene wachitazi zidzanenedwanso pomukumbukira.” (Mateyu 26:6-13)
Pamene Iye anali mʼBetaniya, atakhala pa tebulo akudya mʼnyumba ya munthu wodziwika kuti Simoni wakhate, anabwera mayi ndi botolo la mafuta onunkhira amtengo wapamwamba opangidwa ndi nadi. Anaphwanya botololo nakhuthula mafutawo pa mutu wa Yesu. Ena mwa iwo amene analipo, anakwiya nati kwa wina ndi mnzake, “Chifukwa chiyani akuwononga mafuta onunkhirawa? Akanatheka kugulitsidwa ndi ndalama zambiri zoposa malipiro a pa chaka ndipo ndalamazo ndi kupatsa osauka.” Ndipo anamudzudzula iye mwaukali. Yesu anati, “Musiyeni, chifukwa chiyani mukumuvutitsa? Wandichitira Ine chinthu chabwino. Anthu osauka mudzakhala nawo nthawi zonse, ndipo mukhoza kuwathandiza nthawi iliyonse mungafune. Koma simudzakhala ndi Ine nthawi zonse. (Marko 14:3-7)
Kenaka Mariya anatenga botolo la mafuta a nadi, onunkhira bwino kwambiri, amtengowapatali; Iye anadzoza mapazi a Yesu napukuta ndi tsitsi lake. Ndipo nyumba yonse inadzaza ndi fungo lonunkhira bwino la mafutawo. Koma mmodzi wa ophunzira ake, Yudasi Isikarioti, amene pambuyo pake adzamupereka anati, “Nʼchifukwa chiyani mafuta awa sanagulitsidwe ndipo ndalama zake nʼkuzipereka kwa osauka?” Mafutawo anali a mtengo wa malipiro a chaka chimodzi. Iye sananene izi chifukwa cha kuganizira osauka koma chifukwa anali mbava; ngati wosunga thumba la ndalama, amabamo zomwe ankayikamo. Yesu anayankha kuti, “Mulekeni. Mafutawa anayenera kusungidwa mpaka tsiku loyika maliro anga. Inu mudzakhala ndi osauka nthawi zonse, koma simudzakhala nane nthawi zonse.” (Yohane 12:3-8)
Kusamalira akazi amasiye nʼkofunika
Mʼmasiku amenewo pamene chiwerengero cha ophunzira chinkachuluka, Ayuda a Chihelene pakati pawo anadandaula chifukwa cha Ayuda a Chihebri chifukwa amasiye awo samawagawira chakudya cha tsiku ndi tsiku. Tsono Atumwi khumi ndi awiriwo anasonkhanitsa ophunzira onse pamodzi ndipo anati, “Nʼkosayenera kuti ife tisiye kulalikira Mawu a Mulungu ndi kuyangʼanira za chakudya. Choncho abale, sankhani pakati panu anthu asanu ndi awiri a mbiri yabwino, odzazidwa ndi Mzimu Woyera ndi anzeru. Ife tidzawapatsa udindo oyangʼanira. (Machitidwe a Atumwi 6:1-3)
Chipembedzo chimene Mulungu Atate athu amachivomereza kuti ndi changwiro ndi chopanda zolakwika ndi ichi: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye pa mavuto awo, ndi kudzisunga bwino kuopa kudetsedwa ndi dziko lapansi. (Yakobo 1:27)
Zotsatira za maganizo oyenera pa umwini: palibe wosauka
Okhulupirira onse anali a mtima umodzi, ndi maganizo amodzi. Palibe munthu amene amati zomwe anali nazo zinali zake zokha, koma amagawana chilichonse chimene anali nacho. Atumwi anapitirira kuchitira umboni mwa mphamvu zakuuka kwa Ambuye Yesu, ndipo pa iwo panali chisomo chochuluka. (Machitidwe a Atumwi 4:32-33)
Panali zokonzekera kuti osauka apereke zochepa
“ ‘Ngati munthuyo alibe mwana wankhosa, abweretse njiwa ziwiri kapena nkhunda ziwiri kwa Yehova ngati chopereka chopepesera tchimo lake. Imodzi ikhale nsembe yopepesera tchimo, ndipo inayo ikhale nsembe yopsereza. “ ‘Koma ngati munthuyo alibe njiwa ziwiri kapena nkhunda ziwiri, abweretse ufa wosalala wokwanira kilogalamu imodzi kuti ukhale chopereka chopepesera tchimo limene wachita. Asathiremo mafuta kapena lubani chifukwa ndi chopereka chopepesera tchimo. (Levitiko 5:7, 11)
“ ‘Masiku ake wodziyeretsa akatha, kaya ndi a mwana wamwamuna kapena a mwana wamkazi, abwere kwa wansembe ndi mwana wankhosa wa chaka chimodzi pa khomo la tenti ya msonkhano kuti ikhale nsembe yopsereza. Abwerenso ndi chiwunda cha nkhunda kapena njiwa kuti ikhale nsembe yopepesera machimo. Ngati mkaziyo sangathe kupeza mwana wankhosa, abwere ndi njiwa ziwiri kapena mawunda ankhunda awiri: imodzi ikhale ya nsembe yopsereza ndipo inayo ikhale ya nsembe yopepesera machimo. Tsono wansembe achite mwambo wopepesera wa mkaziyo ndipo adzayeretsedwa.’ ” (Levitiko 12:6, 8)
“Ngati munthu woti ayeretsedweyo ndi wosauka ndipo sangathe kupeza zinthu zimenezi, apereke mwana wankhosa wamwamuna monga nsembe yopepesera kupalamula ndipo ayiweyule pochita mwambo womupepesera. Aperekenso kilogalamu imodzi ya ufa wosalala osakaniza ndi mafuta kuti ikhale nsembe yachakudya, pamodzi ndi mafuta wokwanira limodzi mwa magawo atatu a lita. Aperekenso njiwa ziwiri kapena mawunda awiri zomwe iye angathe kuzipeza. Imodzi ikhale nsembe yopepesera machimo, ndi inayo ikhale ya nsembe yopsereza. (Levitiko 14:21-22)
Ndipo munthuyo apereke njiwa ziwiri kapena mawunda ankhunda awiri, molingana ndi mmene anapezeramo, imodzi ikhale ya nsembe yopepesera machimo ndipo inayo ikhale ya nsembe yopsereza, pamodzi ndi chopereka chachakudya. Akatero ndiye kuti wansembe wachita mwambo wopepesera machimo a munthu woti ayeretsedwe. “Amenewa ndi malamulo a munthu wakhate amene alibe zinthu zoti apereke pamene akuyeretsedwa. (Levitiko 14:30-32)
Ngati munthu amene anachita lumbiro ndi wosauka kwambiri kuti sangathe kulipira ndalama zimenezo, abwere ndi munthu woperekedwa uja kwa wansembe, ndipo wansembeyo ayike mtengo woti munthu wolumbirayo angathe kulipira. (Levitiko 27:8)
Makolo a Yesu anali mʼgulu limeneli
Nthawi yoyeretsedwa kwawo itatha, monga mwa lamulo la Mose, Yosefe ndi Mariya anapita naye ku Yerusalemu kukamupereka kwa Ambuye. (Monga mmene zinalembedwera mu lamulo la Ambuye kuti, “Muzikapereka kwa Ambuye mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa”), ndi kupereka nsembe posunga zimene zinanenedwa mulamulo la Ambuye: “Njiwa ziwiri kapena mawunda ankhunda awiri.” (Luka 2:22-24)
Pa kalembera, olemera ndi osauka anapereka mofanana
“Pamene ukuchita kalembera wa Aisraeli, munthu aliyense ayenera kupereka kwa Yehova chowombolera moyo wake pamene akuwerengedwa. Motero mliri sudzabwera pa iwo pamene ukuwawerenga. Izi ndi zimene aliyense wolembedwa mu kawundula ayenera kupereka: theka la sekeli, kutanthauza ndalama zolemera magalamu asanu ndi limodzi malingana ndi kawerengedwe ka ndalama za ku Nyumba ya Mulungu. Paja sekeli imodzi ikulingana ndi magera makumi awiri. Theka la sekeli chidzakhala chopereka cha kwa Yehova. Aliyense wolembedwa mu kawundula amene ali ndi zaka makumi awiri kapena kupitirira ayenera kupereka chopereka kwa Yehova. Anthu olemera asapereke koposa theka la sekeli ndipo osauka asapereke kuchepera theka la sekeli pamene mukupereka nsembe kwa Yehova yowombolera miyoyo yanu. (Eksodo 30:12-15)
Kupereka kwa osauka kungakhale umboni wa chipulumutso
Koma Zakeyu anayimirira ndipo anati kwa Ambuye, “Taonani Ambuye! Theka la chuma changa ndipereka kwa osauka ndipo ngati ndinamubera wina aliyense pa chilichonse, ndidzamubwezera mochulukitsa kanayi.” Yesu anati kwa iye, “Lero chipulumutso chafika mʼnyumba ino, chifukwa munthu uyu nayenso ndi mwana wa Abrahamu. (Luka 19:8-9)
Zitsanzo zina za kupereka (osati kwa Ambuye)
Ngamira zija zitatha kumwa, mlendo uja anatulutsa chipini chagolide cholemera theka la sekeli ndi zibangiri zagolide ziwiri zolemera masekeli 100. Kenaka wantchitoyo anatulutsa ziwiya zagolide ndi zasiliva ndi zovala nazipereka kwa Rebeka. Anaperekanso mphatso zina za mtengowapatali kwa mlongo wake ndi amayi ake a Rebeka. (Genesis 24:22, 53)
Tsono abambo awo Israeli anawawuza kuti, “Ngati pafunika kutero, ndiye muchite izi: Ikanimo zipatso zabwino kwambiri za dziko lino mʼmatumba mwanu ndi kumutengera munthuyo ngati mphatso. Mumutengere mafuta wopaka pangʼono, uchi pangʼono, mafuta wonunkhiritsa chakudya, mule, mtedza ndi alimoni. Mutenge ndalama zokwanira. Ndalama zina nʼzokamubwezera zija anakuyikirani mʼmatumba anu zija. Mwina anangolakwitsa. Choncho abale aja anatenga mphatso, ndalama zokwanira ndi Benjamininso. Iwo anafulumira kupita ku Igupto ndipo anakaonekera kwa Yosefe. (Genesis 43:11-12, 15)
Atamandike Yehova Mulungu wanu amene wakondwera nanu nakukhazikani pa mpando wake waufumu kuti mulamulire mʼmalo mwa Yehova Mulungu wanu. Chifukwa cha chikondi cha Mulungu wanu pa Israeli, ndi khumbo lake kuti akusungeni mpaka muyaya, Iye wayika inu kukhala mfumu yawo kuti mulamulire moyenera ndi mwachilungamo.” Kenaka iyo inapereka kwa mfumu makilogalamu 4,000 a golide, zonunkhira zambirimbiri ndi miyala yokongola. Nʼkale lomwe sikunaonekenso zonunkhiritsa ngati zomwe mfumu yayikazi ya ku Seba inapereka kwa mfumu Solomoni. (2 Mbiri 9:8-9)
Mfumu Solomoni inapereka kwa mfumu yayikazi ya ku Seba zonse zimene inazifuna ndi kuzipempha ndipo Solomoni anayipatsa mfumuyo zoposa zimene iyo inabweretsa kwa Solomoni. Ndipo mfumuyo inabwerera ku dziko lake pamodzi ndi atumiki ake. (2 Mbiri 9:12)
Hezekiya mfumu ya Yuda anapereka ngʼombe zamphongo 1,000 ndi nkhosa ndi mbuzi 7,000 ku msonkhanoko ndipo akuluakulu ake anapereka ngʼombe zamphongo 1,000, nkhosa ndi mbuzi 10,000. Ansembe ambiri anadziyeretsa. (2 Mbiri 30:24)
Anthu ambiri anabweretsa zopereka kwa Yehova ku Yerusalemu ndi mphatso zamtengowapatali kwa Hezekiya mfumu ya Yuda. Kuyambira nthawi imeneyo Hezekiya ankalemekezedwa kwambiri ndi mitundu ina yonse. (2 Mbiri 32:23)
Yosiya anapereka kwa anthu wamba onse ana ankhosa ndi ana ambuzi okwanira 30,000 ndi ngʼombe zazimuna 3,000, zopereka za Paska zonse zochokera pa chuma chake cha mfumu. Akuluakulu akenso anapereka mwaufulu kwa anthu ndi kwa ansembe ndi Alevi. Hilikiya, Zekariya ndi Yehieli oyangʼanira ntchito ya mʼNyumba ya Mulungu anapereka kwa ansembe zopereka za Paska 2,600 ndi ngʼombe 300. Konaniya nayenso pamodzi ndi Semaya ndi Netaneli, abale ake ndi Hasabiya, Yeiyeli ndi Yozabadi, atsogoleri a Alevi, anapereka nsembe za Paska 5,000 ndi ngʼombe 500 kwa Alevi. (2 Mbiri 35:7-9)
Ndipo kumalo kulikonse kumene otsalawo akukhala, athandizidwe ndi eni dzikolo powapatsa siliva, golide, katundu ndi ziweto ndi zopereka za ufulu zoti akapereke ku Nyumba ya Yehova imene ili ku Yerusalemu.’ ” Onse oyandikana nawo anawathandiza powapatsa ziwiya za siliva ndi zagolide, kuphatikizaponso katundu ndi ziweto, ndiponso mphatso zamtengo wapatali, kuwonjezera pa zopereka zaufulu zija. (Ezara 1:4, 6)
Atsogoleri ena a mabanja anapereka mphatso zothandizira ntchito. Bwanamkubwa anapereka ku thumba losungira chuma, ndalama zagolide za makilogalamu asanu ndi atatu, mabeseni makumi asanu ndi zovala za ansembe 530. Atsogoleri ena amabanja anapereka ku thumba losungira chuma ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndiponso ndalama za siliva zokwana makilogalamu 1,250. Anthu ena onse otsala anapereka ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndalama za siliva zokwana makilogalamu 140, ndiponso zovala za ansembe 67. (Nehemiya 7:70-72)
Ndipo mfumu inakonza phwando lalikulu, phwando la Estere, kukonzera anthu olemekezeka ndi nduna zake zonse. Analamuliranso kuti anthu mʼzigawo zonse asapereke msonkho ndipo anapereka mphatso monga mwakukoma mtima kwa mfumu. (Estere 2:18)
Mafumu a ku Tarisisi ndi a ku zilumba zakutali adzabweretsa mitulo kwa iye, mafumu a ku Seba ndi Seba adzapereka mphatso kwa iyeyo. (Masalimo 72:10)
Yeremiya asanayankhe, Nebuzaradani anamuwuzanso kuti, “Ngati supita ndiye pita, ubwerere kwa Gedaliya, mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani, amene mfumu ya ku Babuloni inamusankha kuti akhale bwanamkubwa wa Yuda. Ukakhale naye pakati pa anthu, kapena upite kulikonse ukufuna.” Ndipo mtsogoleri uja anamupatsa Yeremiya chakudya ndi mphatso zina ndi kumulola kuti apite. (Yeremiya 40:5)
Kukhazika mtima pansi anthu ena
Iye anagona pomwepo usiku umenewo. Pambuyo pake anasankhula pa chuma chimene anali nacho zinthu izi ngati mphatso za Esau, mʼbale wake: Muzikanena kuti, ‘Wantchito wanu Yakobo akubwera mʼmbuyo mwathumu.’ ” Popeza anaganiza kuti, “Ndidzamutsitsa mtima ndi mphatso ndazitsogozazi. Apo tsono ndikadzakumana naye, mwina adzandilandira bwino.” (Genesis 32:13, 20)
Esau anafunsa kuti, “Kodi gulu la ziweto ndakumana nalo lija ndi layani?” Yakobo anayankha nati, “Mbuye wanga, gulu lija ndi lanu kuti mundikomere mtima.” Koma Esau anati, “Mʼbale wanga, ine ndili nazo kale zambiri. Zinthu zakozi sunga.” Yakobo anati, “Chonde musatero. Ngati mwandikomera mtima, landirani mphatso yangayi kuchokera kwa ine. Pakuti ndi mmene mwandirandira bwinomu, ine ndikamaona nkhope yanu ndikuchita ngati ndikuona nkhope ya Mulungu. Chonde, landirani mphatso imene ndakutengeraniyi, popeza Mulungu wandikomera mtima kwambiri moti ndili ndi zonse zimene ndizifuna.” Ndipo popeza kuti Yakobo anamuwumiriza, Esau analandira. (Genesis 33:8-11)
Mphatso yoperekedwa mseri imathetsa mkwiyo, ndipo chiphuphu choperekedwa mobisa chimathetsa mphamvu ya ukali woopsa. (Miyambo 21:14)
Kukopa anthu ena
Pamenepo Sekemu anati kwa abambo ndi alongo ake a Dina, “Inu mundikomere mtima, ndipo ndidzakupatsani chilichonse munganene. Tchulani mtengo wamalowolo umene ndiyenera kupereka, ndipo ndipereka. Ndidzakupatsani chilichonse chimene mukufuna malingana inu mukandipatsa namwaliyu kuti ndimukwatire.” (Genesis 34:11-12)
Kufunafuna nzeru
Mafumu onse a dziko lapansi ankafunafuna kuonana ndi Solomoni kuti adzamve nzeru zimene Mulungu anayika mu mtima mwake. Chaka ndi chaka, aliyense amene amabwera, amabweretsa mphatso monga zipangizo zasiliva ndi golide, mikanjo, zida zankhondo ndi zokometsera zakudya komanso akavalo ndi abulu. (2 Mbiri 9:23-24)
Ndipo mfumu yayikaziyo inapatsa Solomoni golide wolemera makilogalamu 4,000, zokometsera zakudya zambirimbiri, ndiponso miyala yokongola. Sikunabwerenso zokometsera zakudya ngati zomwe mfumu yayikazi ya ku Seba inapatsa Mfumu Solomoni. (1 Mafumu 10:10)
Oyipa amakondwerera imfa ya opembedza
Anthu okhala pa dziko lapansi adzasangalala nazo zimenezi. Adzachita chikondwerero ndi kutumizirana mphatso, chifukwa aneneri awiri amenewa ankasautsa anthu okhala pa dziko lapansi. (Chivumbulutso 11:10)
Nkhani zina za kupereka
Malo operekera
“Muzibwera ndi zipatso zoyambirira kucha zabwino kwambiri ku Nyumba ya Yehova Mulungu wanu. “Musamaphike kamwana kambuzi mu mkaka wa mayi wake. (Eksodo 23:19)
“Muzibwera ndi zipatso zoyambirira kucha zabwino kwambiri ku nyumba ya Yehova Mulungu wanu. “Musamaphike kamwana kambuzi mu mkaka wa mayi wake.” (Eksodo 34:26)
Kumeneko muzipititsako zopereka zanu ndi nsembe zanu zopsereza, ndi chakhumi chanu ndi mphatso zapadera zimene munalonjeza kupereka ndi zopereka zanu zaufulu ndi ana oyamba a ngʼombe zanu ndi nkhosa zanu. (Deuteronomo 12:6)
Tsono kumalo kumene Yehova Mulungu wanu adzasankhe kuti azikhalako muzikabweretsako chilichonse chimene ndikulamulirani inu: zopereka ndi nsembe zanu zopsereza, chakhumi chanu ndi mphatso zapadera, ndi chuma chanu chonse chosankhika chimene munalonjeza kwa Yehova. (Deuteronomo 12:11)
Musamadyere mʼmizinda yanu chakhumi cha tirigu wanu ndi vinyo watsopano ndi mafuta, kapena za ana oyamba kubadwa a ngʼombe zanu ndi nkhosa zanu, kapena chilichonse chimene mwalonjeza kuchipereka, nsembe zanu zaufulu, kapena mphatso zapadera, mʼmalo mwake, muzidya pamaso pa Yehova Mulungu wanu, kumalo kumene Yehova Mulungu wanu adzasankhira inu, ana anu aamuna ndi aakazi, antchito anu aamuna ndi adzakazi anu, ndi Alevi ochokera mʼmizinda yanu, ndipo mudzasangalale pamaso pa Yehova Mulungu wanu pa chilichonse chimene mudzachikhudza. (Deuteronomo 12:17-18)
Mwina tilibe ndalama zopereka, koma tikhoza kupereka Khristu
Ndipo munthu wolumala chibadwire ankanyamulidwa tsiku ndi tsiku kukayikidwa pa khomo la Nyumbayo lotchedwa Khomo Lokongola kuti azikapempha amene amalowa ku bwalo la Nyumbayo. Ataona Petro ndi Yohane ali pafupi kulowa anawapempha ndalama. Iwo anamuyangʼanitsitsa iye. Kenaka Petro anati, “Tiyangʼane!” Munthuyo anawayangʼanitsitsa kuyembekezera kuti alandira kanthu kuchokera kwa iwo. Petro anati kwa iye, “Ine ndilibe siliva kapena golide, koma chimene ndili nacho ndikupatsa. Mʼdzina la Yesu Khristu wa ku Nazareti, yenda.” (Machitidwe a Atumwi 3:2-6)
Munthu wowolowa manja adzapemphedwa kawirikawiri
Anthu ambiri amafuna munthu wopatsa kuti awakomere mtima, ndipo munthu amene amapereka mphatso ndi bwenzi la munthu aliyense. (Miyambo 19:6)
Kupereka kungakhudzidwe ndi kusirira
Choncho ndinaganiza kuti nʼkofunika kupempha abale kuti adzakuchezereni ineyo ndisanafike, ndikuti adzatsirize kukonzekera mphatso zomwe munalonjeza kupereka mowolowamanja. Motero mphatsoyo idzakhala yokonzeratu, ndipo idzakhala mphatso yoperekedwa mowolowamanja, osati mokakamizidwa. (2 Akorinto 9:5)
Kupereka kumabweretsa kuyamika Mulungu
Ntchito imene mukugwirayi siyongothandiza kokha anthu a Mulungu kupeza zosowa, komanso ikuthandiza kuti anthu ambiri ayamike Mulungu. (2 Akorinto 9:12)
Usapereke usanayese kuyanjana
“Nʼchifukwa chake, pamene ukupereka chopereka chako pa guwa lansembe ndipo nthawi yomweyo ukumbukira kuti mʼbale wako ali nawe chifukwa, usiye choperekacho pa guwa lansembepo, choyamba pita kayanjane ndi mʼbale wako; ukatero bwera kudzapereka chopereka chakocho. (Mateyu 5:23-24)
Malemba amatilimbikitsa kupereka
Taonani, pa phiripo, mapazi a munthu amene akubweretsa nkhani yabwino, amene akulengeza za mtendere! Inu anthu a ku Yuda, chitani madyerero anu ndipo kwaniritsani malumbiro anu. Anthu oyipa sadzakuthiraninso nkhondo; iwo adzawonongedwa kotheratu. (Nahumu 1:15)
Ndipo musayiwale kumachita zabwino ndi kuthandiza ena, pakuti Mulungu amakondwera ndi nsembe zotere. (Ahebri 13:16)
Kupereka kungakhale umboni
Ndipo Yesu anati kwa iye, “Taona, usawuze wina aliyense. Koma upite kwa mkulu wa ansembe ukadzionetse wekha ndi kupereka mphatso imene Mose analamulira, kuti ukhale umboni kwa iwo.” (Mateyu 8:4)
“Wonetsetsa kuti usawuze aliyense za zimenezi. Koma pita, kadzionetse wekha kwa wansembe ndi kukapereka nsembe zimene Mose analamulira zotsimikizira kuyeretsedwa kwanu, ngati umboni kwa iwo.” (Marko 1:44)
Kenaka Yesu anamulamula kuti, “Usawuze wina aliyense, koma pita, kadzionetse kwa wansembe ndi kukapereka nsembe zimene Mose anakulamulirani za kuyeretsedwa kwanu monga umboni kwa iwo.” (Luka 5:14)
Chitsanzo cha kupereka kwa mtundu wa anthu
“Patapita zaka zambiri, ndinabwera ku Yerusalemu kudzapereka mphatso kwa anthu osauka a mtundu wanga komanso kudzapereka nsembe. (Machitidwe a Atumwi 24:17)
Zinthu zabwino kuposa nsembe
Kukonda Mulungu ndi mnansi
Kumukonda Iye; ndi mtima wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu zako zonse, ndi kukonda mnansi wako monga iwe mwini, ndi zopambana kuposa zopereka ndi nsembe zopsereza.” (Marko 12:33)
Kukhulupirika kwa Mulungu ndi kumudziwa
Pakuti Ine ndimafuna chifundo osati nsembe, ndi kudziwa Mulungu kulekana ndi nsembe zopsereza. (Hoseya 6:6)
Kumvera
Koma Samueli anayankha kuti, “Kodi Yehova amakondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zina kapena kumvera mawu a ake? Taona, kumvera ndi kwabwino kuposa nsembe, ndipo kutchera khutu ndi kwabwino kuposa kupereka mafuta a nkhosa. (1 Samueli 15:22)
Yehova akuti, “Kodi ndili nazo chiyani nsembe zanu zochuluka?” “Zandikola nsembe zanu zopsereza za nkhosa zazimuna ndiponso mafuta a nyama zonenepa; sindikusangalatsidwanso ndi magazi angʼombe zamphongo ndi a ana ankhosa ndi ambuzi zazimuna. (Yesaya 1:11)
Chilungamo
Za chilungamo ndi zolondola ndi zomwe zimakondweretsa Yehova kuposa kupereka nsembe. (Miyambo 21:3)
Zopereka
Zokakamizidwa
“Pa masiku achikondwerero ndi pa masiku ena osankhidwa, zopereka za chakudya zikhale zokwanira efa imodzi pamodzi ndi ngʼombe yayimuna iliyonse, efa imodzinso ndi nkhosa yayimuna, koma pa mwana wankhosa apereke monga angathere. Iperekenso hini imodzi ya mafuta pa efa iliyonse. Pamene mfumu ikufuna kupereka chopereka chaufulu kwa Yehova, kaya ndi nsembe yopsereza kapena zopereka za chiyanjano, ayitsekulire chipata chakummawa. Iyo ipereke nsembe yopsereza kapena zopereka zake za chiyanjano monga imachitira pa tsiku la Sabata. Kenaka ituluke ndipo mfumuyo itatuluka, atseke chitsekocho. “Tsiku lililonse nthawi ya mmawa azipereka kwa Yehova mwana wankhosa wa chaka chimodzi. Pamodzi ndi nyamayo aziperekanso mmawa uliwonse chopereka cha chakudya chokwanira chimodzi mwa zigawo zisanu ndi chimodzi za efa. Aziperekanso chimodzi mwa zigawo zitatu za hini ya mafuta okandira ufa wosalala. Chopereka cha chakudya chimenechi chiziperekedwa kwa Yehova nthawi zonse mwa lamulo. Motero azipereka mwana wankhosa ndi chopereka cha chakudya ndi mafuta mmawa uliwonse kuti zikhale nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku. (Ezekieli 46:11-15)
Zaufulu
Pamene mfumu ikufuna kupereka chopereka chaufulu kwa Yehova, kaya ndi nsembe yopsereza kapena zopereka za chiyanjano, ayitsekulire chipata chakummawa. Iyo ipereke nsembe yopsereza kapena zopereka zake za chiyanjano monga imachitira pa tsiku la Sabata. Kenaka ituluke ndipo mfumuyo itatuluka, atseke chitsekocho. (Ezekieli 46:12)
Zitsanzo za zopereka
Ndipo mfumu pamodzi ndi Aisraeli onse anapereka nsembe pamaso pa Yehova. Solomoni anapereka nsembe zachiyanjano kwa Yehova: ngʼombe 22,000, nkhosa ndi mbuzi 120,000. Motero mfumu pamodzi ndi Aisraeli onse anapatula Nyumba ya Yehova. Tsiku lomwelo mfumu inapatulanso malo a pakati pa bwalo limene linali kutsogolo kwa Nyumba ya Yehova ndiponso nthuli za mafuta za nsembe yachiyanjano, chifukwa guwa lansembe la mkuwa limene linali pamaso pa Yehova linali lochepa kwambiri ndipo nsembe zonse zopsereza, nsembe zachakudya, ndi nthuli za mafuta a nsembe zachiyanjano sizikanakwanirapo. (1 Mafumu 8:62-64)
Iye anati, “Koresi mfumu ya Perisiya ikunena kuti, “ ‘Yehova, Mulungu wakumwamba wandipatsa maufumu onse a dziko lapansi, ndipo wandipatsa udindo woti ndimumangire Nyumba ku Yerusalemu mʼdziko la Yuda. Ndipo kumalo kulikonse kumene otsalawo akukhala, athandizidwe ndi eni dzikolo powapatsa siliva, golide, katundu ndi ziweto ndi zopereka za ufulu zoti akapereke ku Nyumba ya Yehova imene ili ku Yerusalemu.’ ” Onse oyandikana nawo anawathandiza powapatsa ziwiya za siliva ndi zagolide, kuphatikizaponso katundu ndi ziweto, ndiponso mphatso zamtengo wapatali, kuwonjezera pa zopereka zaufulu zija. (Ezara 1:2, 4, 6)
Utenge siliva ndi golide zimene ine mfumu ndi alangizi anga tapereka mwa ufulu kwa Mulungu wa Israeli, amene amakhala ku Yerusalemu. Mutengenso siliva yense ndi golide amene mungamupeze mʼdziko lonse la Babuloni, ngakhalenso zinthu zimene anthu pamodzi ndi ansembe adzapereka mwaufulu kuperekera ku Nyumba ya Mulungu wawo ya ku Yerusalemu. Ndi ndalama zimenezi mudzaonetsetse kuti mwagula ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa aamuna pamodzi ndi zopereka zake za chakudya ndi za chakumwa. Mudzapereke zimenezi pa guwa lansembe la Nyumba ya Mulungu wanu ya ku Yerusalemu. Ndalama zotsala mudzagwiritse ntchito zimene inuyo ndi abale anu zikakukomerani malingana nʼkufuna kwa Mulungu wanu. Ndipo chilichonse chimene chingafunike mʼNyumba ya Mulungu wanu, chimene mudzapeze mpata wopereka, ndalama zake zogulira zidzachokere mʼthumba la chuma cha mfumu. Tsopano Ine, mfumu Aritasasita, ndikulamula asungichuma onse a dera la Patsidya pa Yufurate kuti, chilichonse chimene wansembe Ezara, mlembi wa malamulo a Mulungu Wakumwamba adzapempha kwa inu, mupatseni mwa msanga. Ngakhale atafunika makilogalamu 3,400 asiliva, makilogalamu 10,000 a tirigu, malita 2,000 a vinyo, malita 2,000 a mafuta ndi mchere wochuluka motani, zonsezi mupereke monga zingafunikire. (Ezara 7:15-18, 20-22)
Ngati mphatso yako ya uzimu ndi kupereka, igwiritse ntchito
Ife tili ndi mphatso zosiyana, molingana ndi chisomo chopatsidwa kwa ife. Ngati mphatso ya munthu ndi kunenera, musiyeni ayigwiritse ntchito molingana ndi chikhulupiriro chake. Ngati ndi kutumikira, musiyeni atumikire. Ngati ndi kuphunzitsa, musiyeni aphunzitse. Ngati ndi kulimbikitsa, musiyeni alimbikitse. Ngati ndi kupereka kuthandiza osowa, musiyeni apereke mowolowamanja. Ngati ndi utsogoleri, musiyeni alamulire mosamala. Ngati ndi kuonetsa chifundo, musiyeni achite mosangalala. (Aroma 12:6-8)
Pereka kuti upereke zosowa
Ndipo iwo atayeza ndi muyeso wa malita awiri, iye amene anatola zambiri sizinamutsalireko ndipo amene anatola pangʼono sizinamuchepere. Aliyense anatola zomukwanira kudya. (Eksodo 16:18)
Cholinga chathu sikuti tipeputse ena pamene inuyo mukuvutika, koma kuti pakhale kufanana. Zambiri zimene muli nazo pakati panu muthandize nazo osowa, kuti nawonso akadzakhala nazo zambiri adzakuthandizeni pa zosowa zanu. Cholinga nʼkuchita mofanana, monga kwalembedwa kuti, “Iye amene anatola zambiri sizinamutsalireko ndipo amene anatola pangʼono sizinamuchepere.” (2 Akorinto 8:13-15)