Uphungu

Malemba amalimbikitsa kwambiri kufunafuna ndi kumvera uphungu wanzeru, umene umabweretsa kupambana, nzeru ndi chitsogozo. Koma kukana uphungu wa Mulungu kapena kutsatira uphungu wa oyipa kumabweretsa kulephera, mikangano ngakhalenso chiwonongeko.

Kufunsa uphungu kumalimbikitsidwa

Munthu wanzeru amvetse bwino miyamboyi kuti awonjezere kuphunzira kwake, ndi munthu womvetsa zinthu bwino apatepo luso, (Miyambo 1:5)
Uphungu wanga munawunyoza. Kudzudzula kwanga simunakusamale. (Miyambo 1:25)
...popeza iwo sanasamale malangizo anga ndipo ananyoza chidzudzulo changa. (Miyambo 1:30)
Zochita za chitsiru mwini wakeyo amaziona ngati zabwino, koma munthu wanzeru amamvera malangizo. (Miyambo 12:15)
Chipongwe chosamalabadirako za anthu ena chimadzetsa mikangano, koma womva malangizo a anzawo ndiwo ali ndi nzeru. (Miyambo 13:10)
Mvera uphungu ndipo landira malangizo; pa mapeto pake udzakhala wanzeru. (Miyambo 19:20)
Zokonzekera zimapindula utafunsira uphungu; ndipo usanamenye nkhondo yamba wapempha malangizo oyenera. (Miyambo 20:18)
Mafuta ndi zonunkhira zimasangalatsa mtima, ndipo kukoma mtima kwa bwenzi kwagona pa malangizo ake. (Miyambo 27:9)
Wachinyamata wosauka koma wanzeru aposa mfumu yokalamba koma yopusa imene simvanso malangizo. (Mlaliki 4:13)
Pa nthawi imeneyo Afarisi anabwera kwa Yesu ndipo anati kwa Iye, “Chokani malo ano ndipo pitani kumalo ena aliwonse. Herode akufuna kukuphani.” (Luka 13:31)

Alangizi ambiri amalimbikitsidwa

Pakasoweka uphungu mtundu wa anthu umagwa; koma pakakhala aphungu ambiri pamakhalanso chipulumutso. (Miyambo 11:14)
Popanda uphungu zolinga zako munthu zimalephereka, koma pakakhala aphungu ambiri zolinga zimatheka. (Miyambo 15:22)
Munthu wodziwa zinthu ali ndi mphamvu yayikulu kuposa munthu wanyonga zambiri, ndipo munthu wachidziwitso amaposa munthu wamphamvu. Pafunika malangizo kuti ukamenye nkhondo. Pakakhala aphungu ambiri kupambana kumakhalapo. (Miyambo 24:5-6)

Anthu owonjezera amachulukitsa ntchito yochitika

Anthu asanu mwa inu adzapirikitsa anthu 100, ndipo anthu 100 mwa inu adzathamangitsa anthu 10,000, ndipo adani anuwo mudzawagonjetsa ndi lupanga. (Levitiko 26:8)
Kukhala awiri nʼkwabwino kuposa kukhala wekha, chifukwa ntchito ya anthu awiri ili ndi phindu: Ngati winayo agwa, mnzakeyo adzamudzutsa. Koma tsoka kwa munthu amene agwa ndipo alibe wina woti amudzutse! Komanso ngati anthu awiri agona malo amodzi, adzafunditsana. Koma nanga mmodzi angadzifunditse yekha? Munthu mmodzi angathe kugonjetsedwa, koma anthu awiri akhoza kudziteteza. Chingwe cha maulusi atatu sichidukirapo. (Mlaliki 4:9-12)

Zitsanzo za kupereka/kutsatira uphungu

Mpongozi wa Mose ataona zonse zimene iye amawachitira anthu anati, “Nʼchiyani chimene mukuwachitira anthuwa? Nʼchifukwa chiyani mulipo nokha woweruza, pamene anthu onsewa ayimirira kuyambira mmawa mpaka madzulo?” Mose anamuyankha kuti, “Chifukwa anthuwa anabwera kwa ine kudzafunsa zimene Mulungu akufuna. Ngati munthu akangana ndi mʼbale wake, onse awiri amabwera kwa ine, ndipo ine ndimawaweruza. Ndimawawuzanso malamulo a Mulungu ndi malangizo ake.” Mpongozi wa Mose anayankha kuti, “Zimene mukuchitazi si zabwino. Ntchitoyi ndi yayikulu kuposa mphamvu zanu. Inu simungathe kuyigwira nokha. Inu pamodzi ndi anthuwa amene amabwera kwa inu mudzatopa. Tsono tamverani ndikulangizeni, ndipo Mulungu akhale nanu. Inu muziwayimirira anthuwa pamaso pa Mulungu, ndipo mikangano yawo muzibwera nayo kwa Iye. Aphunzitseni mawu ndi malangizo a Mulungu. Aphunzitseni mmene ayenera kukhalira ndi zimene ayenera kuchita. Koma sankhani amuna odziwa ntchito yawo, anthu owopa Mulungu, anthu odalirika amene amadana ndi kupeza phindu mwachinyengo. Tsono muwayike kuti akhale oyangʼanira anthu motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 100, ena a anthu 50 ndi ena a anthu khumi. Tsono amenewa aziweruza anthu nthawi zonse. Mlandu uliwonse waukulu azibwera nawo kwa inu, koma mlandu waungʼono aziweruza okha. Izi zidzachititsa kuti ntchito yanu ipepuke, popeza mudzagwira ntchito mothandizana. Ngati mutsatira malangizowa monga mmene Mulungu wakulamulirani ndiye kuti simudzafowoka ndipo anthu onsewa adzapita kwawo mu mtendere.” Mose anamvera mpongozi wake ndi kuchita zonse zimene iye ananena. (Eksodo 18:14-24)
Pamenepo Natani anafunsa Batiseba, amayi ake a Solomoni, kuti, “Kodi simunamve kuti Adoniya, mwana wa Hagiti, walowa ufumu popanda Davide mbuye wathu kudziwa? Tsopano ine ndikulangizeni inu mmene mungapulumutsire moyo wanu ndi moyo wa mwana wanu Solomoni. (1 Mafumu 1:11-12)
“Anthu ankamvetsera zimene ndinkanena mwachidwi, ankadikira atakhala chete kuti amve malangizo anga. Ndikayankhula, iwo sankayankhulanso; mawu anga ankawagwira mtima. Ankayembekezera ine monga momwe amayembekezera mvula ndipo ankalandira mawu anga ngati mvula ya mʼmalimwe. (Yobu 29:21-23)

Chitsanzo cha kusapereka/kusatsatira uphungu

Amaziya atabwerera kuja anakapha Aedomu, anabweretsa milungu ya anthu a ku Seiri. Ndipo anayika kuti ikhale milungu yake, ankayipembedza ndi kupereka nsembe zopsereza. Yehova anakwiyira Amaziya, ndipo anamutumizira mneneri amene anati, “Nʼchifukwa chiyani mukupembedza milungu ya anthu awa, imene sinathe kupulumutsa anthu ake mʼdzanja lanu?” Iye ali kuyankhula, mfumu inati, “Kodi ife takusankha iwe kuti ukhale mlangizi wa mfumu? Khala chete! Ufuna kuphedweranji?” Choncho mneneriyo analeka koma anati, “Ine ndikudziwa kuti Mulungu watsimikiza kukuwonongani chifukwa mwachita izi ndipo simunamvere uphungu wanga.” (2 Mbiri 25:14-16)

Kumene uphungu umachokera

Ambuye

“Kwa Mulungu ndiye kuli nzeru ndi mphamvu; uphungu ndi kumvetsa zinthu ndi zake. (Yobu 12:13)
Ine ndidzatamanda Yehova amene amandipatsa uphungu; ngakhale usiku mtima wanga umandilangiza. (Masalimo 16:7)
Tsono ndani munthu amene amaopa Yehova? Yehova adzamulangiza njira yoti ayitsate. (Masalimo 25:12)
Ndidzakulangiza ndi kukuphunzitsa njira imene udzayendamo; ndidzakupatsa uphungu ndi kukuyangʼanira. (Masalimo 32:8)
Yehova amalepheretsa chikonzero cha anthu a mitundu ina; Iye amaphwanya zolinga za anthu ambiri. Koma chikonzero cha Yehova chimakhala mpaka muyaya, zolinga za mu mtima mwake pa mibado yonse. (Masalimo 33:10-11)
Inu mumanditsogolera ndi malangizo anu ndipo pambuyo pake mudzanditenga ku ulemerero. (Masalimo 73:24)
Munthu amakonzekera zambiri mu mtima mwake, koma cholinga cha Yehova ndiye chidzachitike. (Miyambo 19:21)
Chifukwa mwana watibadwira, mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife, ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake. Ndipo adzamutcha dzina lake lakuti Phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu, Atate Amuyaya, ndi Mfumu ya Mtendere. (Yesaya 9:6)
Mzimu wa Yehova udzakhala pa iye Mzimu wanzeru ndi wa kumvetsa zinthu, Mzimu wauphungu ndi wamphamvu, Mzimu wachidziwitso ndi wakuopa Yehova. (Yesaya 11:2)
Izinso zimachokera kwa Yehova Wamphamvuzonse, wa uphungu wodabwitsa ndi wa nzeru zopambana. (Yesaya 28:29)
Mumaonetsa chikondi chanu kwa anthu osawerengeka koma mumalanga ana chifukwa cha machimo a makolo awo. Inu ndinu Mulungu Wamkulu ndi Wamphamvu. Dzina lanu ndinu Yehova Wamphamvuzonse. Zolinga zanu ndi zazikulu ndipo zochita zanu ndi zamphamvu. Maso anu amaona zonse zimene anthu amachita. Mumapereka mphotho kwa munthu aliyense molingana ndi makhalidwe ake ndi ntchito zake. (Yeremiya 32:18-19)

Zotsatira za kusafunsa uphungu wa Ambuye

Sauli anafa chifukwa anali wosakhulupirika pamaso pa Yehova. Iye sanasunge mawu a Yehova, pakuti anakafunsira nzeru kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa, sanafunsire nzeruzo kwa Yehova. Choncho Yehova anamupha ndi kupereka ufumu kwa Davide mwana wa Yese. (1 Mbiri 10:13-14)
Aisraeli anatengako chakudya chawo koma sanafunse kwa Yehova. Choncho Yoswa anapangana nawo za mtendere kuti sadzawapha, ndipo atsogoleri a gulu anavomereza pochita lumbiro. (Yoswa 9:14-15)
Koma posachedwa anayiwala zimene Iye anachita, ndipo sanayembekezere uphungu wake. Mʼchipululu, anadzipereka ku zilakolako zawo; mʼdziko lopanda kanthu anayesa Mulungu. Choncho Iye anawapatsa chimene anapempha, koma anatumiza nthenda yowondetsa. (Masalimo 106:13-15)
Ena anakhala mu mdima ndi mʼchisoni chachikulu, amʼndende ovutika mʼmaunyolo achitsulo, pakuti iwowo anawukira mawu a Mulungu ndi kunyoza uphungu wa Wammwambamwamba. Kotero Iye anawapereka kuti agwire ntchito yakalavulagaga; anagwa pansi ndipo panalibe woti awathandize. (Masalimo 107:10-12)

Ambuye amalamulira uphungu wa anthu

Tsono Davide anamva kuti, “Ahitofele ali pakati pa anthu owukira pamodzi ndi Abisalomu.” Choncho Davide anapemphera, “Inu Yehova, musandutse uphungu wa Ahitofele ukhale uchitsiru.” Davide anati kwa iye, “Ngati iwe upite ndi ine, udzakhala chondilemetsa. Koma ngati ubwerera ku mzinda ndi kukanena kwa Abisalomu kuti, ‘Inu mfumu ine ndidzakhala wantchito wanu.’ Mʼmbuyomu ndinali wantchito wa abambo anu koma tsopano ndidzakhala wantchito wanu. Ukatero udzandithandiza kulepheretsa malangizo a Ahitofele. (2 Samueli 15:31, 33-34)
Abisalomu anati kwa Ahitofele, “Tiwuze malangizo ako. Kodi tichite chiyani?” Tsono masiku amenewo malangizo amene Ahitofele amapereka anali ngati mawu ochokera kwa Mulungu. Umu ndi mmene Davide ndi Abisalomu amalandirira malangizo onse a Ahitofele. (2 Samueli 16:20, 23)
Husai atabwera kwa iye, Abisalomu anati, “Ahitofele wapereka malangizo ake. Kodi tichite zimene wanena? Ngati sichoncho, tiwuze maganizo ako.” Husai anayankha Abisalomu kuti, “Malangizo amene Ahitofele wapereka si abwino pa nthawi ino. Inu mukudziwa bwino abambo anu ali ndi ankhondo awo. Iwo ndi anthu ankhondo komanso ndi woopsa ngati chimbalangondo chimene chalandidwa ana ake. Kuwonjezera apa abambo anu ndi katswiri wa nkhondo. Iwo sanagone pamodzi ndi asilikali awo. Onani, ngakhale tsopano lino abisala mʼphanga lina ku malo ena ake. Ngati iwo atayamba kuthira nkhondo asilikali anu, aliyense amene adzamve zimenezi adzati, ‘Gulu lalikulu lankhondo lotsatira Abisalomu laphedwa.’ Tsono ngakhale msilikali wolimba mtima kwambiri, amene mtima wake uli ngati wa mkango, adzagwidwa ndi mantha aakulu pakuti Aisraeli akudziwa kuti abambo anu ndi ankhondo ndipo kuti iwo amene ali nawo ndi anthu olimba mtima. “Kotero ine ndikukulangizani kuti: Aisraeli onse, kuchokera ku Dani mpaka ku Beeriseba; ochuluka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja, asonkhane kwa inu ndipo muwatsogolera kupita ku nkhondo. Ndipo ife tidzapita kukamuthira nkhondo kulikonse kumene tikamupeze, ndipo ife tikamuthira nkhondo ngati mame pa nthaka. Palibe amene adzakhale wamoyo kaya iye kapena ankhondo ake. Iye akakathawira mu mzinda, Aisraeli onse adzabweretsa zingwe ku mzindawo, ndipo ife tidzawugwetsera ku chigwa mpaka sipadzapezeka ngakhale kachidutswa.” Abisalomu ndi ankhondo ena onse a Israeli anati, “Malangizo a Husai Mwariki ndi abwino kuposa a Ahitofele.” Pakuti Yehova anatsimikiza kutsutsa malangizo onse abwino a Ahitofele ndi cholinga choti zimuvute Abisalomu. Husai anawuza ansembe Zadoki ndi Abiatara kuti, “Ahitofele analangiza Abisalomu ndi akuluakulu a Israeli zakuti, koma ine ndawalangiza kuchita zakutizakuti. Tsopano tumizani wamthenga msangamsanga kuti akamuwuze Davide kuti, ‘Musakagone powolokera Yorodani ku chipululu koma mukawoloke. Mukapanda kutero, mfumu ndi anthu onse amene ali naye adzaphedwa.’ ” Yonatani ndi Ahimaazi amakhala ku Eni Rogeli. Tsono wantchito wamkazi ndiye amapita kukawawuza ndipo iwo amayenera kupita kukamuwuza mfumu Davide, pakuti iwowo sankayenera kuonekera polowa mu mzinda. Koma mnyamata wina anawaona ndipo anakawuza Abisalomu. Kotero anthu awiriwo anachoka mofulumira ndipo anapita ku nyumba ya munthu wina ku Bahurimu. Iye anali ndi chitsime ku mpanda kwake ndipo iwo analowamo. Mkazi wake anatenga chophimba ndipo anachiyika pamwamba pa chitsimecho nawazapo tirigu. Palibe amene anadziwa chilichonse za izi. Anthu a Abisalomu atafika kwa mkaziyo pa nyumbapo anafunsa kuti, “Kodi Ahimaazi ndi Yonatani ali kuti?” Mkaziyo anawayankha kuti, “Awoloka mtsinje.” Anthuwo anafunafuna koma sanapeze munthu, kotero anabwerera ku Yerusalemu. Anthu aja atapita, awiriwo anatuluka mʼchitsimemo ndipo anapita kukawuza mfumu Davide nati kwa iye, “Nyamukani, muwoloke mtsinje msangamsanga. Ahitofele wapereka malangizo akutiakuti kutsutsana nanu.” Kotero Davide ndi anthu onse amene anali nawo ananyamuka ndi kuwoloka Yorodani. Pofika mmamawa, panalibe munthu amene anatsala asanawoloke Yorodani! Ahitofele ataona kuti malangizo ake sanatsatidwe, iye anakwera bulu wake napita ku mzinda wa kwawo ku nyumba yake. Iye anakonza mʼnyumba mwakemo ndi kudzimangirira. Kotero anafa nayikidwa mʼmanda a abambo ake. (2 Samueli 17:6-23)

Malemba

Malamulo anu amandikondweretsa; ndiwo amene amandilangiza. (Masalimo 119:24)

Anthu opembedza

Amayi ndi abambo

Mwana wanga, mvera malangizo a abambo ako ndipo usakane mawu okuwongolera a amayi ako. Ali ngati sangamutu yokongola ya maluwa pamutu pako ndiponso ali ngati mkanda mʼkhosi mwako. (Miyambo 1:8-9)
Mwana wanga, usunge malamulo a abambo ako; ndipo usataye zimene anakuphunzitsa amayi ako. Zimenezi uzimatirire pa mtima pako masiku onse, uzimangirire mʼkhosi mwako. Ukamayenda, zidzakulozera njira; ukugona, zidzakulondera; ukudzuka, zidzakuyankhula. (Miyambo 6:20-22)
Mvera abambo ako amene anakubala, usanyoze amayi ako pamene akalamba. (Miyambo 23:22)

Chitsanzo cha uphungu wa bambo wopembedza

Davide ali pafupi kumwalira, analangiza mwana wake Solomoni kuti: “Ndatsala pangʼono kupita kumene munthu wina aliyense amayenera kupitako. Tsono khala wamphamvu, uvale zilimbe, ndipo uzichita zimene Yehova Mulungu wako amafuna, uziyenda mʼnjira zake, uzisunga malangizo ndi malamulo ake monga momwe zinalembedwera mʼMalamulo a Mose, kuti zonse zimene udzachite zidzakuyendere bwino kulikonse kumene udzapite. Ndipo Yehova akwaniritse zimene anandilonjeza kuti, ‘Ngati zidzukulu zako zidzakhala mosamala, niziyenda mokhulupirika pamaso panga ndi mtima wawo wonse ndi moyo wawo wonse, sudzasowa munthu wokhala pa mpando waufumu wa Israeli.’ (1 Mafumu 2:1-4)

Amene apatsidwa nzeru

Mafumu onse a dziko lapansi ankafunafuna kuonana ndi Solomoni kuti adzamve nzeru zimene Mulungu anayika mu mtima mwake. (2 Mbiri 9:23)
Woyenda ndi anthu anzeru nayenso adzakhala wanzeru; koma woyenda ndi zitsiru adzapwetekeka. (Miyambo 13:20)
Mzimu amapereka kwa munthu wina mawu anzeru, Mzimu yemweyonso amapereka kwa wina mawu achidziwitso. (1 Akorinto 12:8)

Anthu odziwa zinthu

Ndipo Mfumu Rehobowamu anapempha nzeru kwa akuluakulu amene ankatumikira Solomoni abambo ake pamene anali ndi moyo. Iye anawafunsa kuti, “Kodi mungandilangize zotani kuti ndiwayankhe anthu amenewa?” Iwo anayankha kuti, “Ngati lero mudzakhala mtumiki wa anthu amenewa ndi kuwatumikira ndipo mukawayankha bwino, iwowo adzakhala atumiki anu nthawi zonse.” Koma Rehobowamu anakana malangizo amene akuluakuluwo anamupatsa ndipo anafunsira nzeru kwa anyamata anzake amene anakulira nawo limodzi omwe ankamutumikira. (1 Mafumu 12:6-8)
Kenaka mfumu Rehobowamu anafunsira nzeru kwa akuluakulu amene ankatumikira abambo ake, Solomoni, pamene anali moyo. Iye anafunsa kuti, “Kodi inu mungandilangize zotani kuti ndiwayankhe anthu awa?” Iwo anayankha kuti, “Ngati inu muwakomera mtima anthu awa ndi kuwasangalatsa ndiponso kuwayankha mawu abwino, iwo adzakutumikirani nthawi zonse.” Koma Rehobowamu anakana malangizo amene akuluakulu anamupatsa ndipo anakafunsira nzeru kwa anyamata amene anakula naye pamodzi komanso amamutumikira. (2 Mbiri 10:6-8)

Uphungu woti upewe

Oyipa

Koma anthuwo amawuza Mulungu kuti, ‘Tichokereni!’ Ife tilibe chikhumbokhumbo chofuna kudziwa njira zanu. Kodi Wamphamvuzonseyo ndani kuti timutumikire? Ife tipindula chiyani tikamapemphera kwa Iyeyo? Komatu ulemerero wawo suli mʼmanja mwawo, koma ine ndimakhala patali ndi uphungu wa anthu oyipa. (Yobu 21:14-16)
Wodala munthu amene satsatira uphungu wa anthu ochimwa, kapena kuyima mʼnjira ya anthu oyipa, kapena kukhala mʼmagulu a anthu onyoza. (Masalimo 1:1)
Maganizo a anthu olungama ndi owongoka, koma malangizo a anthu oyipa ndi achinyengo. (Miyambo 12:5)

Chitsanzo cha uphungu woyipa

Tsono anthu a mʼdzikomo anayamba kuchititsa ulesi anthu a ku Yuda, ndi kuwachititsa mantha kuti aleke ntchito yomangayo. Analemba alangizi ena kuti alepheretse cholinga chawo pa ntchitoyo pa nthawi yonse ya Koresi, mfumu ya ku Perisiya, ndiponso mpaka pamene Dariyo mfumu ya ku Perisiya ankalamulira dzikolo. (Ezara 4:4-5)
Kwa iwe, Ninive, kunachokera munthu wa cholinga choyipa, wofuna kuchitira Yehova chiwembu, amene amapereka uphungu woyipa. (Nahumu 1:11)

Anthu opembedza mafano

Iwo ndi mtundu wopanda maganizo, iwo alibe nzeru nʼpangʼono pomwe. (Deuteronomo 32:28)
Koma ndikayangʼana palibe ndi mmodzi yemwe, palibe ndi mmodzi yemwe pakati pawo wotha kupereka uphungu, palibe woti ayankhe pamene ine ndawafunsa. Taonani, milungu yonseyi ndi yachinyengo! Zochita zawo si kanthu konse; mafano awo ali ngati mphepo yachabechabe. (Yesaya 41:28-29)

Akuluakulu

Koma Rehobowamu anakana malangizo amene akuluakuluwo anamupatsa ndipo anafunsira nzeru kwa anyamata anzake amene anakulira nawo limodzi omwe ankamutumikira. Iye anawafunsa kuti, “Kodi malangizo anu ngotani? Kodi ndiwayankhe chiyani anthu amene akunena kwa ine kuti, ‘Peputsani goli limene abambo anu anatisenzetsa’?” Anyamata anzake amene anakula nawo limodzi aja anamuyankha kuti, “Anthu amene ananena kwa iwe kuti, ‘Abambo anu anatisenzetsa goli lolemetsa, koma inu peputsani goli lathu,’ uwawuze kuti ‘Chala changa chakanise nʼchachikulu kupambana chiwuno cha abambo anga. Mfumuyo inawayankha anthuwo mwankhanza. Kukana malangizo amene akuluakulu anayipatsa. Anatsatira malangizo amene anyamata anzake anamupatsa ndipo anati “Abambo anga ankakusenzetsani goli lolemetsa. Ine ndidzachititsa kuti likhale lolemera kwambiri. Abambo anga ankakukwapulani ndi zikoti wamba koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.” (1 Mafumu 12:8-10, 13-14)
Koma Rehobowamu anakana malangizo amene akuluakulu anamupatsa ndipo anakafunsira nzeru kwa anyamata amene anakula naye pamodzi komanso amamutumikira. Iye anawafunsa kuti, “Kodi malangizo anu ndi otani? Kodi tiwayankhe chiyani anthu amene akunena kuti, ‘Peputsani goli limene abambo anu anayika pa ife?’ ” Anyamata amene anakula pamodzi naye anamuyankha kuti, “Anthu amene anena kwa inu kuti, ‘Abambo anu anatisenzetsa goli lolemetsa koma inu mupeputse goli lathu,’ muwawuze kuti, ‘Chala changa chachingʼono ndi chachikulu kuposa chiwuno cha abambo anga. Mfumu inawayankha mwankhanza, pokana malangizo a akuluakulu aja. Iye anatsatira malangizo a anyamata ndipo anati, “Abambo anga anakusenzetsani goli lolemetsa koma ine ndidzalichititsa kukhala lolemetsa kwambiri. Abambo anga anakukwapulani ndi zikoti wamba koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.” (2 Mbiri 10:8-10, 13-14)

Madalitso ndi matemberero

Madalitso ndi ubwino wa kufunsa uphungu

Kupambana

Pakasoweka uphungu mtundu wa anthu umagwa; koma pakakhala aphungu ambiri pamakhalanso chipulumutso. (Miyambo 11:14)
Popanda uphungu zolinga zako munthu zimalephereka, koma pakakhala aphungu ambiri zolinga zimatheka. (Miyambo 15:22)
Pafunika malangizo kuti ukamenye nkhondo. Pakakhala aphungu ambiri kupambana kumakhalapo. (Miyambo 24:6)

Malangizo ndi chitsogozo

Ndidzakulangiza ndi kukuphunzitsa njira imene udzayendamo; ndidzakupatsa uphungu ndi kukuyangʼanira. (Masalimo 32:8)
Inu mumanditsogolera ndi malangizo anu ndipo pambuyo pake mudzanditenga ku ulemerero. (Masalimo 73:24)
Mwana wanga, usunge malamulo a abambo ako; ndipo usataye zimene anakuphunzitsa amayi ako. Zimenezi uzimatirire pa mtima pako masiku onse, uzimangirire mʼkhosi mwako. Ukamayenda, zidzakulozera njira; ukugona, zidzakulondera; ukudzuka, zidzakuyankhula. (Miyambo 6:20-22)

Nzeru

Chipongwe chosamalabadirako za anthu ena chimadzetsa mikangano, koma womva malangizo a anzawo ndiwo ali ndi nzeru. (Miyambo 13:10)
Mvera uphungu ndipo landira malangizo; pa mapeto pake udzakhala wanzeru. (Miyambo 19:20)

Chimwemwe pa kupereka uphungu

Mʼmitima ya anthu amene amakonza zoyipa muli chinyengo; koma anthu olimbikitsa za mtendere amakhala ndi chimwemwe. (Miyambo 12:20)

Matemberero/zotsatira za kusafunsa uphungu kapena kufunsa uphungu wa oyipa

Imfa

Sauli anafa chifukwa anali wosakhulupirika pamaso pa Yehova. Iye sanasunge mawu a Yehova, pakuti anakafunsira nzeru kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa, sanafunsire nzeruzo kwa Yehova. Choncho Yehova anamupha ndi kupereka ufumu kwa Davide mwana wa Yese. (1 Mbiri 10:13, 14)
Nayenso anayenda mʼnjira ya banja la Ahabu, pakuti amayi ake anamulimbikitsa kuchita zolakwika. Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova monga momwe banja la Ahabu linachitira, pakuti atamwalira abambo ake, iwo anakhala alangizi ake, kumene kunali kudziwononga kwake. Iyeyo anatsatiranso uphungu wawo pamene anapita ndi Yehoramu, mwana wa Ahabu, mfumu ya Israeli kukachita nkhondo ndi Hazaeli mfumu ya Aramu ku Ramoti Giliyadi. Aaramu anavulaza Yehoramu, (2 Mbiri 22:3-5)
Iye ali kuyankhula, mfumu inati, “Kodi ife takusankha iwe kuti ukhale mlangizi wa mfumu? Khala chete! Ufuna kuphedweranji?” Choncho mneneriyo analeka koma anati, “Ine ndikudziwa kuti Mulungu watsimikiza kukuwonongani chifukwa mwachita izi ndipo simunamvere uphungu wanga.” (2 Mbiri 25:16)
Popeza ndinakuyitanani koma inu munakana kumvera. Ndinayesa kukuthandizani koma panalibe amene anasamala. Uphungu wanga munawunyoza. Kudzudzula kwanga simunakusamale. Ndiye inenso ndidzakusekani mukadzakhala mʼmavuto; ndidzakunyogodolani chikadzakugwerani chimene mumachiopacho. Chiwonongeko chikadzakugwerani ngati namondwe, tsoka likadzakufikirani ngati kamvuluvulu, mavuto ndi masautso akadzakugwerani. “Tsono mudzandiyitana koma sindidzayankha; mudzandifunafuna, koma simudzandipeza. Popeza iwo anadana ndi chidziwitso ndipo sanasankhe kuopa Yehova, popeza iwo sanasamale malangizo anga ndipo ananyoza chidzudzulo changa. Tsono adzadya zipatso zoyenera mayendedwe awo ndi kukhuta ndi ntchito zimene anachita kwa ena. Pakuti anthu osachangamuka amaphedwa chifukwa cha kusochera kwawo, ndipo zitsiru zimadziwononga zokha chifukwa cha mphwayi zawo. (Miyambo 1:24-32)

Mkangano

Chipongwe chosamalabadirako za anthu ena chimadzetsa mikangano, koma womva malangizo a anzawo ndiwo ali ndi nzeru. (Miyambo 13:10)

Zolinga zolephereka

Popanda uphungu zolinga zako munthu zimalephereka, koma pakakhala aphungu ambiri zolinga zimatheka. (Miyambo 15:22)

Kulephera

Pakasoweka uphungu mtundu wa anthu umagwa; koma pakakhala aphungu ambiri pamakhalanso chipulumutso. (Miyambo 11:14)

Matemberero ndi zotsatira zina

Aisraeli anatengako chakudya chawo koma sanafunse kwa Yehova. Choncho Yoswa anapangana nawo za mtendere kuti sadzawapha, ndipo atsogoleri a gulu anavomereza pochita lumbiro. (Yoswa 9:14-15)
Koma posachedwa anayiwala zimene Iye anachita, ndipo sanayembekezere uphungu wake. Mʼchipululu, anadzipereka ku zilakolako zawo; mʼdziko lopanda kanthu anayesa Mulungu. Choncho Iye anawapatsa chimene anapempha, koma anatumiza nthenda yowondetsa. (Masalimo 106:13-15)
Ena anakhala mu mdima ndi mʼchisoni chachikulu, amʼndende ovutika mʼmaunyolo achitsulo, pakuti iwowo anawukira mawu a Mulungu ndi kunyoza uphungu wa Wammwambamwamba. Kotero Iye anawapereka kuti agwire ntchito yakalavulagaga; anagwa pansi ndipo panalibe woti awathandize. (Masalimo 107:10-12)