Kusirira

Malemba amaletsa momveka bwino kusirira; kumabweretsa zotsatira zoyipa kwambiri ndipo kumalepheretsa munthu kulandira Ufumu wa Mulungu. Kumaonedwa ngati kupembedza mafano, ndipo zitsanzo za mphamvu zake zowononga zinaperekedwa kuchenjeza okhulupirira.

Lamulo losasirira

“Usasirire nyumba ya mnzako. Usasirire mkazi wa mnzako kapena wantchito wake wamwamuna kapena mdzakazi wake, ngʼombe yake kapena bulu wake, kapena chilichonse cha mnzako.” (Eksodo 20:17)
“Usasirire mkazi wa mnzako. Usasirire nyumba ya mnzako kapena munda wake, wantchito wake wamwamuna kapena mdzakazi wake, ngʼombe yake kapena bulu wake, kapena chilichonse cha mnzako.” (Deuteronomo 5:21)
Muwawotche pa moto mafano a milungu yawo. Musasirire siliva ndi golide amene ali pa mafanoyo. Musamutenge kuti akhale wanu chifukwa mukatero mudzakodwa naye ngati msampha, pakuti Yehova Mulungu wanu amanyansidwa nazo. (Deuteronomo 7:25)

Chilango chochenjezedwa chifukwa cha kusirira

Koma musatenge kanthu kalikonse koyenera kuwonongedwa. Mukadzangotenga kanthu kalikonse koyenera kuwonongedwa, mudzaputa mavuto, misasa ya Israeli idzawonongedwa. (Yoswa 6:18)
Tsoka kwa amene amakonzekera chiwembu, kwa amene amakonzekera kuchita zoyipa usiku pa mabedi awo! Kukacha mmawa amakachitadi chifukwa ali ndi mphamvu zochitira zimenezo. Amasirira minda ndi kuyilanda, amasirira nyumba ndi kuzilanda. Amatenga nyumba ya munthu mwachinyengo, munthu mnzawo kumulanda cholowa chake. Nʼchifukwa chake Yehova akuti, “Ine ndikukonzekera kubweretsa tsoka pa anthu awa, tsoka limene simudzatha kudzipulumutsa nokha. Inu simudzayendanso monyada, pakuti idzakhala nthawi ya masautso. (Mika 2:1-3)

Chitsanzo cha chilango chifukwa cha kusirira

Aisraeli achimwa. Iwo aphwanya pangano limene ndinawalamula kuti asunge. Anatengako zinthu zina zofunika kuwonongedwa. Choncho anabako, ananena bodza ndi kuyika zinthu zakubazo pamodzi ndi katundu wawo. Nʼchifukwa chake Aisraeli sangathe kulimbana ndi adani awo. Iwo anathawa pamaso pa adani awo chifukwa ndiwo oyenera kuwonongedwa. Ine sindikhalanso ndi inu pokhapokha mutawononga chilichonse choyenera kuwonongedwa pakati panu. “Nyamuka, ukawawuze anthu kuti, ‘Mudzipatule nokha kukonzekera kuonana nane mawa; pakuti Yehova Mulungu wa Israeli akuti choyenera kuwonongedwa chija chili pakati panu, inu Aisraeli. Simungathe kulimbana ndi adani anu mpaka mutachichotsa.’ “Mawa mmamawa adzabwere pamaso pa Yehova fuko limodzilimodzi. Fuko limene Yehova adzaliloze lidzabwere patsogolo mbumba imodziimodzi. Tsono mbumba imene Yehova adzayiloze idzabwere patsogolo banja limodzilimodzi. Banja limene Yehova adzaliloze lidzabwere patsogolo munthu mmodzimmodzi. Iye amene adzagwidwe ndi zinthu zoyenera kuwonongedwazo adzawotchedwa ndi moto, pamodzi ndi banja lake lonse ndi zinthu zake zonse. Iyeyutu wachita chinthu chonyansa pakati pa Aisraeli ndi kuphwanya pangano limene anthu anga anachita ndi Ine!” Mmawa mwake Yoswa anabweretsa Israeli fuko limodzilimodzi ndipo fuko la Yuda linalozedwa. Anabweretsa poyera mbumba zonse za fuko la Yuda, ndipo mbumba ya Zera inagwidwa. Kenaka anatulutsa poyera mabanja onse a mbumba ya Zera ndipo banja la Zabidi linagwidwa. Potsiriza anatulutsa anthu onse a banja la Zabidi ndipo Akani anagwidwa. Iyeyu anali mwana wa Karimi, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera wa fuko la Yuda. Ndipo Yoswa anati kwa Akani, “Mwana wanga pereka ulemerero kwa Yehova Mulungu wa Israeli ndipo umuyamike Iye. Ndiwuze zimene wachita, ndipo usandibisire.” Akani anayankha kuti, “Zoona! Ine ndachimwira Yehova Mulungu wa Israeli. Chimene ndachita ine ndi ichi: Ndinaona mwa zinthu zolanda ku nkhondo zija, mkanjo wokongola wa ku Babuloni, makilogalamu awiri a siliva ndiponso golide wolemera theka la kilogalamu. Zimenezi ndinazikhumba ndipo ndinazitenga. Ndazibisa mʼkati mwa tenti yanga, ndipo siliva ali pansi pake.” Motero Yoswa anatuma anthu, ndipo anathamanga kupita ku tenti. Anthuwo anakapeza kuti zinthuzo zinabisidwadi mʼtenti yake, ndipo siliva analidi pansi pake. Iwo anazichotsa zinthuzo mu tenti yake nabwera nazo kwa Yoswa ndi kwa Aisraeli onse ndipo anaziyika pamaso pa Yehova. Kenaka Yoswa pamodzi ndi Aisraeli onse anatenga Akani mwana wa Zera pamodzi ndi siliva, mkanjo, golide zimene anapezeka nazo zija. Anatenganso ana ake aamuna ndi aakazi, ngʼombe zake, abulu ndi nkhosa, tenti yake ndi zonse anali nazo, kupita nazo ku chigwa cha Akori. Yoswa anati “Chifukwa chiyani wabweretsa mavuto awa pa ife? Yehova ndiye abweretse mavuto pa iwe lero.” Kenaka Aisraeli onse anaponya miyala Akani, namupha. Anaponyanso miyala banja lake lonse, nʼkulipha. Pambuyo pake anatentha Akani uja, banja lake ndi zonse zimene anali nazo. (Yoswa 7:11-25)

Zitsanzo za kusirira zoperekedwa kuti zitiphunzitse

Tsono zinthu izi zinachitika kuti zikhale chitsanzo, kuti ife tisayike mitima yathu pa zinthu zoyipa monga anachitira makolo athuwo. (1 Akorinto 10:6)

Osirira sadzalandira Ufumu wa Mulungu

Kodi simukudziwa kuti munthu woyipa sadzalowa mu ufumu wa Mulungu? Musanyengedwe: achigololo, kapena opembedza mafano, kapena achiwerewere, kapena amuna adama, kapena ogonana ndi amuna okhaokha; kapena akuba, kapena aumbombo, kapena oledzera, kapena achipongwe, kapena opeza ndalama mwachinyengo sadzalowa mu ufumu wa Mulungu. (1 Akorinto 6:9-10)

Munthu wosirira ndi wopembedza mafano

Koma pakati panu pasamveke nʼpangʼono pomwe zadama, kapena za mtundu wina uliwonse wa chodetsa, kapena za umbombo, chifukwa izi ndi zosayenera kwa anthu oyera a Mulungu. (Aefeso 5:3)
Dziwani ichi, palibe wadama, wochita zonyansa kapena waumbombo, munthu wotero ali ngati wopembedza mafano, amenewa alibe malo mu ufumu wa Khristu ndi Mulungu. (Aefeso 5:5)

Usayanjane ndi wokhulupirira wosirira

Ndakulemberani mʼkalata yanga kuti musayanjane nawo anthu achigololo. Pamenepatu sindikutanthauzatu anthu a dziko lapansi lino amene ndi achigololo, kapena aumbombo, kapena opeza ndalama mwachinyengo, kapena opembedza mafano. Kukanatero mukanangochoka mʼdziko lapansi lino. Koma tsopano ndikukulemberani kuti musayanjane ndi aliyense amene adzitcha mʼbale koma ndi wachigololo, kapena waumbombo, kapena wopembedza mafano, kapena wonamizira anzake, woledzera kapena wopeza ndalama mwachinyengo. Munthu wotere ngakhale kudya, osadya naye pamodzi. (1 Akorinto 5:9-11)

Chitsanzo cha munthu wopembedza amene sanasirire

Ine sindinasirire siliva kapena golide kapena zovala za munthu aliyense. (Machitidwe a Atumwi 20:33)

Mulungu akhoza kulamulira kusirira

Amuna onse azionekera pamaso pa Yehova Mulungu wa Israeli, katatu pa chaka. Ine ndidzapirikitsa mitundu inayo pamene inu mukufikako ndi kukulitsa malire anu. Palibe ndi mmodzi yemwe adzafune kulanda dziko lanu ngati inu muzidzapita katatu pa chaka pamaso pa Yehova Mulungu wanu, chaka chilichonse. (Eksodo 34:23-24)

Kusirira kumagwiritsidwa ntchito ngati chitsanzo cha ntchito ya lamulo

Nanga ife tinene chiyani? Kodi Malamulo ndi oyipa? Ayi. Nʼkosatheka! Kunena zoona, popanda Malamulo, ine sindikanazindikira tchimo. Pakuti sindikanadziwa kuti kusirira ndi tchimo ngati Malamulo sakananena kuti, “Usasirire.” Koma chifukwa cha Malamulo uchimo unapeza mwayi owutsa mʼkati mwanga khalidwe lililonse la kusirira. Pakuti pakanapanda Malamulo, uchimo ukanakhala wopanda mphamvu. (Aroma 7:7-8)