Kukhutira kumaphunziridwa/kumaperekedwa ndi Ambuye
Sindikunena izi chifukwa choti ndikusowa thandizo, poti ine ndaphunzira kukhala wokwaniritsidwa ndi zimene ndili nazo. Ndimadziwa kusauka nʼkutani, ndipo ndimadziwa kulemera nʼkutani. Ndaphunzira chinsinsi chokhala wokhutitsidwa mwa njira ina iliyonse, kaya nʼkudya bwino kapena kukhala ndi njala, kaya kukhala ndi chuma kapena umphawi. Ndikhoza kuchita zonse kudzera mwa Iye amene amandipatsa mphamvu. (Afilipi 4:11-13)
Khutira/usade nkhawa chifukwa Ambuye ndiye wotipatsa
“Nʼchifukwa chake ndikuwuzani kuti musadere nkhawa za moyo wanu kuti mudzadya chiyani kapena mudzamwa chiyani; kapenanso za thupi lanu kuti mudzavala chiyani. Kodi moyo suposa chakudya? Kodi thupi siliposa zovala? Onani mbalame zamlengalenga sizifesa kapena kukolola kapena kusunga mʼnkhokwe komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Kodi inu simuziposa kwambiri? Kodi ndani wa inu podandaula angathe kuwonjeza ora limodzi pa moyo wake? “Ndipo bwanji inu mudera nkhawa za zovala? Onani makulidwe a maluwa akutchire. Sagwira ntchito kapena kuwomba nsalu. Ndikukuwuzani kuti angakhale Solomoni mu ulemerero wake sanavale mofanana ndi limodzi la maluwa amenewa. Ngati umu ndi mmene Mulungu avekera udzu wa kutchire umene ulipo lero ndipo mawa uponyedwa ku moto, kodi sadzakuvekani koposa? Aa! Inu a chikhulupiriro chochepa! Chifukwa chake musadere nkhawa ndi kuti, ‘Tidzadya chiyani?’ kapena ‘Tidzamwa chiyani?’ kapena ‘Tidzavala chiyani?’ Pakuti anthu akunja amazifuna zinthu zonsezi ndipo Atate anu akumwamba adziwa kuti musowa zimenezi. Koma muyambe mwafuna ufumu wake ndi chilungamo chake ndipo zinthu zonsezi zidzapatsidwa kwa inu. Chifukwa chake musadere nkhawa ndi za mawa, popeza tsiku lililonse lili ndi zovuta zake zokwanira. (Mateyu 6:25-34)
Kenaka Yesu anati kwa ophunzira ake, “Choncho Ine ndikuwuzani kuti musadere nkhawa za moyo wanu, zimene mudzadya; kapena za thupi lanu, zimene mudzavala. Moyo uposa chakudya, ndi thupi liposa chovala. Taonani makwangwala: iwo safesa kapena kukolola, alibe nyumba zosungamo zinthu kapena nkhokwe; komabe, Mulungu amawadyetsa. Koposa kotani inu amene ndi ofunikira kuposa mbalame. Ndi ndani wa inu akhoza kuwonjeza ora pa moyo wake chifukwa cha kudandaula? Popeza simungathe kuchita kanthu kakangʼono aka, nʼchifukwa chiyani mumadandaula ndi zinazi? “Taonani mmene maluwa amakulira. Iwo sagwira ntchito kapena kusoka zovala. Koma Ine ndikuwuzani kuti, ngakhale Solomoni muulemelero wake wonse sanavalepo ngati limodzi la awa. Ngati umu ndi mmene Mulungu amavekera udzu wakuthengo, umene lero ulipo ndipo mawa uponyedwa pa moto, nanga Iye adzakuvekani inu motani. Haa! Inu achikhulupiriro chochepa! Ndipo musayike mtima wanu pa zimene mudzadye kapena kumwa; musade nazo nkhawa. Pakuti anthu akunja amathamanga kufunafuna zinthu zotere, ndipo Atate amadziwa kuti mumazifuna zimenezi. Koma funafunani ufumu wake, ndipo mudzapatsidwa zonsezi. (Luka 12:22-31)
Mtima wanu usakonde ndalama koma mukhutitsidwe ndi zimene muli nazo, chifukwa Mulungu anati, “Sadzakusiyani, kapena kukutayani konse.” Kotero ife tikunena molimba mtima kuti, “Ambuye ndiye mthandizi wanga; sindidzachita mantha. Munthu angandichitenji ine?” (Ahebri 13:5-6)
Khutira pamene zosowa zofunika za moyo zapezeka
Koma ngati tili ndi chakudya ndi zovala, zimenezi zitikwanire. (1 Timoteyo 6:8)
Khutira ndi malipiro ako
Kenaka asilikali ena anamufunsa kuti, “Nanga ife tichite chiyani?” Iye anayankha kuti, “Musamalande ndalama moopseza ndipo musamanamizire anthu, khutitsidwani ndi malipiro anu.” (Luka 3:14)
Kukhutira kumachokera makamaka pa kulakalaka Khristu
Kodi kumwamba ndili ndi yani kupatula Inu? Ndipo dziko lapansi lilibe chilichonse chimene ndimachilakalaka koposa Inuyo. (Masalimo 73:25)
Kukhutira ndi kupembedza kumabweretsa phindu lalikulu
Koma kulemekeza Mulungu kuli ndi phindu lalikulu. (1 Timoteyo 6:6)
Mwamuna wa mkazi wachigololo sadzakhutira
Iye savomera dipo lililonse; sangapepeseke ngakhale umupatse mphatso zochuluka motani. (Miyambo 6:35)