Lamulo losapembedza mafano
Choncho musadzipangire milungu yasiliva kapena yagolide kuti muziyipembedza pamodzi ndi Ine.’ ” (Eksodo 20:23)
Mafano ndi ntchito ya manja a anthu
Koma mafano awo ndi siliva ndi golide, opangidwa ndi manja a anthu. (Masalimo 115:4)
Mafano a mitundu ya anthu ndi siliva ndi golide, opangidwa ndi manja a anthu. (Masalimo 135:15)
Mulungu amapereka zonse, ngakhale zinthu zopangira mafano
Iye sanazindikire kuti ndine amene ndinkamupatsa tirigu, vinyo watsopano ndi mafuta. Ndine amene ndinkamukhuthulira siliva ndi golide, zimene ankapangira mafano a Baala. (Hoseya 2:8)
Ndidzamulanga chifukwa cha masiku amene anafukiza lubani kwa Abaala; anadzikongoletsa povala mphete ndi mikanda yamtengowapatali ndipo anathamangira zibwenzi zake, koma Ine anandiyiwala,” akutero Yehova. (Hoseya 2:13)
Dyera likufanizidwa ndi kupembedza mafano
Choncho, iphani zilakolako za dziko lapansi mwa inu, monga: dama, zodetsa, kulakalaka zosayenera, kukhumba zoyipa ndi umbombo, pakuti umbombo ndiko kupembedza mafano. (Akolose 3:5)
Mulungu amaweruza amene amapembedza mafano
Adzachita nawe mwachidani. Adzakulanda zonse zimene unagwirira ntchito. Adzakusiya wamaliseche ndiponso wausiwa. Kuyipa kwa makhalidwe ako achiwerewere kudzakhala pammbalambanda. Zonyansa zako ndi chiwerewere chako, zabweretsa izi pa iwe chifukwa unachita zonyansa ndi anthu a mitundu ndi kudziyipitsa ndi mafano awo. (Ezekieli 23:29-30)
Mafano ake onse ndidzawaphwanyaphwanya; mphatso zake zonse ndidzazitentha ndi moto; ndidzawononga zifanizo zonse za milungu yake. Popeza analandira mphatso zake kuchokera ku malipiro a akazi achiwerewere, mphatsozonso zidzagwiritsidwa ntchito ndi ena ngati malipiro a akazi achiwerewere.” (Mika 1:7)
Chitsanzo cha anthu a Mulungu amene anawononga mafano, kenako Ambuye anawadalitsa
Pamenepo mudzawononga mafano anu okutidwa ndi siliva ndiponso zifanizo zanu zokutidwa ndi golide; mudzawataya ngati zinthu zonyansa ndipo mudzati, “Zichoke zonsezi!” Yehova adzakugwetseraninso mvula pa mbewu zanu zimene mukadzale mʼnthaka, ndipo chakudya chimene mudzakolole chidzakhala chabwino ndi chochuluka. Tsiku limenelo ngʼombe zanu zidzadya msipu wochuluka. (Yesaya 30:22-23)
Chitsanzo cha kupembedza mafano kobisika mʼchipembedzo
“Ndinamva inu mukutemberera munthu amene anaba ndalama zanu zasiliva 1,100. Ndalamazo zili ndi ine, ndinatenga ndine.” Pamenepo amayi akewo anati, “Yehova akudalitse mwana wanga!” Choncho Mika anabweza ndalama 1,100 za siliva kwa amayi ake, ndipo amayi akewo anati, “Ine ndapatulira Yehova ndalama za silivazi kuti mwana wanga aseme fano ndi kulikuta ndi siliva. Ndiye tsopano ndikubwezera ndalamazo.” Tsono Mika atabweza ndalama zija kwa amayi ake, iwo anatengapo ndalama za siliva 200 namupatsa mmisiri wosula siliva. Iye anakonza fano, nasungunula siliva uja ndi kulikutira fano lija. Ndipo Mika anayika fanolo mʼnyumba mwake. (Oweruza 17:2-4)